); 1 Kings 18:36-39 (“God of Abraham”); 1 John 4:1-6 (Testing the spirits) (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora.
47 Ombani mʼmanja, inu anthu onse;
fuwulani kwa Mulungu ndi mawu achimwemwe.
2 Ndi woopsadi Yehova Wammwambamwamba;
Mfumu yayikulu ya dziko lonse lapansi!
3 Iye anatigonjetsera mitundu yambirimbiri ya anthu;
anayika anthu pansi pa mapazi athu.
4 Iye anatisankhira cholowa chathu,
chonyaditsa cha Yakobo, amene anamukonda.
Sela
5 Mulungu wakwera, anthu akumufuwulira mwachimwemwe,
Yehova wakwera, akumuyimbira malipenga.
6 Imbani matamando kwa Mulungu, imbani matamando;
imbani matamando kwa mfumu yathu, imbani matamando.
7 Pakuti Mulungu ndi mfumu ya dziko lonse lapansi;
imbirani Iye salimo la matamando.
8 Mulungu akulamulira mitundu ya anthu;
Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.
9 Anthu otchuka mwa anthu a mitundu ina asonkhana
monga anthu a Mulungu wa Abrahamu,
pakuti mafumu a dziko lapansi ndi ake a Mulungu;
Iye wakwezedwa kwakukulu.
36 Pa nthawi yopereka nsembe, mneneri Eliya anasendera pafupi ndi guwa lansembe, napemphera kuti, “Inu Yehova, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, lero zidziwike kuti ndinu Mulungu mu Israeli ndipo kuti ine ndine mtumiki wanu, kuti ine ndachita zonsezi chifukwa mwalamula ndinu. 37 Ndiyankheni, Inu Yehova, ndiyankheni, kuti anthu awa adziwe Inu Yehova, kuti ndinu Mulungu, ndipo kuti mutembenuziranso mitima yawo kwa Inu.”
38 Pamenepo moto wa Yehova unagwa, nunyeketsa nsembe yopserezayo, nkhuni, miyala ndi dothi lomwe. Unawumitsanso madzi amene anali mʼngalande.
39 Anthu onse ataona zimenezi, anaweramitsa nkhope zawo pansi, nafuwula kuti, “Yehova ndiye Mulungu! Yehova ndiye Mulungu!”
Kuyesa Mizimu
4 Anzanga okondedwa, musakhulupirire mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ikuchokera kwa Mulungu, chifukwa aneneri onama ambiri afalikira mʼdziko lapansi. 2 Mungathe kuzindikira Mzimu wa Mulungu motere: Mzimu uliwonse umene umavomereza kuti Yesu Khristu anabwera mʼthupi, ndi wochokera kwa Mulungu, 3 koma mzimu uliwonse umene suvomereza Yesu, siwochokera kwa Mulungu. Uwu ndi mzimu wa wokana Khristu umene munawumva kuti ukubwera ndipo ngakhale tsopano wabwera kale mʼdziko lapansi.
4 Inu ana okondedwa, ndinu ochokera kwa Mulungu ndipo mwawagonjetsa aneneri onyengawa, chifukwa Iye amene ali mwa inu ndi wamkulu kuposa amene ali mʼdziko lapansi. 5 Aneneri onyengawa ndi ochokera mʼdziko lapansi, nʼchifukwa chake amayankhula za dziko lapansi, ndipo dziko lapansi limawamvera. 6 Ife ndi ochokera kwa Mulungu, ndipo aliyense amene amadziwa Mulungu amamvera zimene timayankhula. Koma aliyense amene sachokera kwa Mulungu samvera zimene timayankhula. Mmenemu ndiye mmene timasiyanitsira pakati pa mzimu wachoonadi ndi Mzimu wachinyengo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.