Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Genesis 22:1-14

Kuyesedwa kwa Abrahamu

22 Nthawi ina zitatha izi, Mulungu anamuyesa Abrahamu. Iye anati, “Abrahamu!”

Ndipo iye anayankha kuti, “Ee Ambuye.”

Ndipo Mulungu anati, “Tenga Isake, mwana wako yekhayo amene umamukonda ndi kupita naye ku dziko la Moriya. Ukamupereke iye ngati nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri a kumeneko limene ndidzakuwuza.”

Abrahamu anadzuka mmamawa wake namangirira chokhalira pa bulu. Atadula nkhuni zokwanira zowotchera nsembe yopsereza, Abrahamu, antchito ake awiri pamodzi ndi Isake ananyamuka kupita kumalo kumene Mulungu anamuwuza Abrahamu. Pa tsiku lachitatu, Abrahamu anakweza maso ake ndipo anaona malowo chapatali. Ndipo Abrahamu anati kwa antchito ake aja, “Bakhalani pano ndi buluyu. Ine ndi mnyamatayu tipita uko kukapemphera, koma tibweranso.”

Abrahamu anatenga nkhuni za nsembe yopsereza zija namusenzetsa mwana wake Isake, ndipo iye mwini anatenga moto ndi mpeni. Pamene awiriwo amayendera pamodzi, Isake anati kwa abambo ake Abrahamu, “Abambo?”

Abrahamu anayankha, “Ee mwana wanga.”

Isake anafunsa, “Moto ndi nkhuni zilipo, koma nanga mwana wankhosa wa nsembe yopsereza ali kuti?”

Abrahamu anayankha, “Mwana wanga, Mulungu adzipezera yekha mwana wankhosa wa nsembe yopsereza.” Ndipo awiriwo anapitiriza ulendo.

Atafika pamalo pamene Mulungu anamuwuza paja, Abrahamu anamangapo guwa lansembe nayika nkhuni pamwamba pa guwapo. Kenaka anamumanga mwana wake Isake namugoneka paguwapo, pamwamba pa nkhuni paja. 10 Kenaka Abrahamu anatambasula dzanja lake natenga mpeni kuti aphe mwana wake. 11 Koma mngelo wa Yehova anayitana Abrahamu kuchokera kumwamba nati, “Abrahamu! Abrahamu!”

Iye anayankha kuti, “Ee Ambuye.”

12 Mngeloyo anati, “Usatambasulire mwanayo dzanja lako kuti umuphe, pakuti tsopano ndadziwa kuti iwe umaopa Mulungu. Iwe sunandimane mwana wako mmodzi yekhayo.”

13 Abrahamu anatukula maso ake ndipo anaona nkhosa yamphongo itakoledwa ndi nyanga zake mu ziyangoyango. Iye anapita nakatenga nkhosa ija ndikuyipha ngati nsembe yopsereza mʼmalo mwa mwana wake. 14 Choncho Abrahamu anatcha malo amenewa kuti Yehova-Yire (Wopereka). Ndipo mpaka lero amatchula malowo kuti ndi “Pa phiri la Yehova wopereka.”

Masalimo 13

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

13 Mpaka liti Yehova? Kodi mudzandiyiwala mpaka kalekale?
    Mpaka liti mudzandibisira nkhope yanu?
Ndidzalimbana ndi maganizo anga
    ndi kukhala ndi chisoni mu mtima mwanga tsiku lililonse mpaka liti?
    Mpaka liti adani anga adzandipambana?

Ndiyangʼaneni ndi kundiyankha, Inu Yehova Mulungu wanga.
    Walitsani maso anga kuti ndingafe;
mdani wanga adzati, “Ndamugonjetsa,”
    ndipo adani anga adzakondwera pamene ine ndagwa.

Koma ndikudalira chikondi chanu chosasinthika;
    mtima wanga umakondwera ndi chipulumutso chanu.
Ine ndidzayimbira Yehova
    pakuti wandichitira zokoma.

Aroma 6:12-23

12 Nʼchifukwa chake, musalole tchimo lilamulire matupi anu amene anafa kuti mumvere zilakolako zonyansa. 13 Musapereke ziwalo zathupi lanu ku tchimo, ngati zipangizo zamakhalidwe oyipa. Mʼmalo mwake, mudzipereke kwa Mulungu, ngati amene achoka ku imfa kupita ku moyo. Ndipo mupereke ziwalo zathupi lanu ngati zipangizo zachilungamo. 14 Tchimo silidzakhalanso ndi mphamvu pa inu, chifukwa Malamulo sakulamulira moyo wanu koma chisomo.

Ife Ndife Akapolo a Mulungu

15 Nʼchiyani tsono? Kodi tidzichimwa chifukwa sitikulamulidwa ndi Malamulo koma chisomo? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! 16 Kodi inu simudziwa kuti pamene mudzipereka kwa wina wake, kumumvera ngati akapolo, ndinu akapolo a amene mumumvera? Ngati ndinu akapolo a tchimo mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo akumvera, mudzakhala olungama pamaso pake. 17 Koma ayamikidwe Mulungu pakuti ngakhale munali akapolo a tchimo, munamvera ndi mtima wonse chiphunzitso chimene munalandira. 18 Inu munamasulidwa ku tchimo ndipo tsopano mwasanduka akapolo achilungamo.

19 Ine ndikufanizira zinthu za tsiku ndi tsiku chifukwa chikhalidwe chanu nʼchofowoka. Monga momwe munkapereka ziwalo za matupi kukhala akapolo a zonyansa ndi makhalidwe oyipa, zimene zimanka zichulukirabe, choncho tsopano dziperekeni ziwalozo kuti zikhale akapolo achilungamo ndi a kuyera mtima. 20 Pomwe munali akapolo atchimo, simunkalabadira za chilungamo. 21 Kodi munapeza phindu lanji pochita zinthu zimenezi, zomwe tsopano mukuchita nazo manyazi? Zinthu zimenezo zotsatira zake ndi imfa! 22 Koma tsopano pakuti inu mwamasulidwa ku tchimo ndipo mwasanduka akapolo a Mulungu, phindu lomwe mulipeza ndi kuyera mtima ndipo chotsatira chake ndi moyo wosatha. 23 Pakuti malipiro a tchimo ndi imfa, koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Mateyu 10:40-42

40 “Iye amene alandira inu alandira Ine, ndipo amene alandira Ine alandiranso amene anandituma Ine. 41 Aliyense amene alandira mneneri chifukwa chakuti ndi mneneri alandira mphotho ya mneneri, ndipo aliyense amene alandira munthu wolungama chifukwa chakuti ndi munthu wolungama, adzalandira mphotho ya wolungama. 42 Ngati aliyense apereka madzi ozizira a mʼchikho kwa mmodzi wa angʼonoangʼono awa chifukwa cha kuti ndi ophunzira anga, ndikuwuzani zoona, ndithudi sadzataya mphotho yake.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.