Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
13 Mpaka liti Yehova? Kodi mudzandiyiwala mpaka kalekale?
Mpaka liti mudzandibisira nkhope yanu?
2 Ndidzalimbana ndi maganizo anga
ndi kukhala ndi chisoni mu mtima mwanga tsiku lililonse mpaka liti?
Mpaka liti adani anga adzandipambana?
3 Ndiyangʼaneni ndi kundiyankha, Inu Yehova Mulungu wanga.
Walitsani maso anga kuti ndingafe;
4 mdani wanga adzati, “Ndamugonjetsa,”
ndipo adani anga adzakondwera pamene ine ndagwa.
5 Koma ndikudalira chikondi chanu chosasinthika;
mtima wanga umakondwera ndi chipulumutso chanu.
6 Ine ndidzayimbira Yehova
pakuti wandichitira zokoma.
18 Kodi alipo Mulungu wofanana nanu,
amene amakhululukira tchimo ndi kuyiwala zolakwa
za anthu otsala amene ndi cholowa chake?
Inu simusunga mkwiyo mpaka muyaya
koma kwanu nʼkuonetsa chikondi chosasinthika.
19 Inu mudzatichitiranso chifundo;
mudzapondereza pansi machimo athu
ndi kuponyera zolakwa zathu zonse pansi pa nyanja.
20 Mudzakhala wokhulupirika kwa Yakobo,
ndi kuonetsa chifundo chanu kwa Abrahamu,
monga munalonjeza molumbira kwa makolo athu
masiku amakedzana.
2 Chonde mvetsetsani! Ine Paulo, ndikukuwuzani kuti mukalola kuchita mdulidwe, Khristu simupindula nayenso konse. 3 Ndikubwerezanso kuwuza munthu aliyense wovomereza kuchita mdulidwe kuti ayeneranso kutsata Malamulo onse. 4 Inu amene mukufuna kulungamitsidwa ndi lamulo mwachotsedwa mwa Khristu; munagwa kusiyana nacho chisomo. 5 Koma mwachikhulupiriro, ife tikudikira mwachidwi kudzera mwa Mzimu, chilungamo chimene tikuyembekeza. 6 Pakuti mwa Khristu Yesu mdulidwe kapena kusachita mdulidwe zilibe phindu. Chinthu chokhacho chimene chimafunika ndi chikhulupiriro chogwira ntchito mwachikondi.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.