Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 86:11-17

11 Ndiphunzitseni njira yanu Yehova,
    ndipo ndidzayenda mʼchoonadi chanu;
patseni mtima wosagawikana
    kuti ndilemekeze dzina lanu.
12 Ndidzakutamandani Ambuye Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse;
    ndidzalemekeza dzina lanu kwamuyaya.
13 Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu kwa ine;
    mwandipulumutsa ku malo ozama a manda.

14 Inu Mulungu wanga, anthu odzikuza akundithira nkhondo;
    anthu ankhanza akufuna kundipha,
    amene salabadira za Inu.
15 Koma Ambuye ndinu Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima,
    wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi ndi wokhulupirika.
16 Tembenukirani kwa ine ndipo ndichitireni chifundo;
    perekani mphamvu zanu kwa mtumiki wanu
    ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu.
17 Mundionetse chizindikiro cha ubwino wanu
    kuti adani achione ndi kuchititsidwa manyazi,
    pakuti Yehova mwandithandiza ndi kunditonthoza.

Yeremiya 42:18-22

18 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Momwe ndinawakwiyira mwaukali anthu okhala mu Yerusalemu, koteronso ndidzakukwiyirani mukapita ku Igupto. Mudzasanduka chinthu chotembereredwa ndi chochititsa mantha, choseketsa ndi chonyozeka. Malo ano simudzawaonanso.’

19 “Inu otsala a ku Yuda, Yehova wakuwuzani kuti, ‘Musapite ku Igupto.’ Dziwani chinthu ichi: Ine lero ndikukuchenjezani 20 kuti munalakwitsa kwambiri. Inu munandituma kwa Yehova Mulungu wanu nʼkumati ‘Mukatipempherere kwa Yehova Mulungu wathu, nʼkudzatiwuza chimene afuna kuti tichite, ndipo ife tidzachita.’ 21 Ine lero ndakuwuzani, koma inu simukumverabe zonse zimene Yehova Mulungu anandituma kuti ndikuwuzeni. 22 Tsono dziwani ichi: mudzafadi ndi nkhondo, njala ndi mliri kumalo kumene mukufuna mukakhaleko.”

Mateyu 10:5-23

Yesu anatuma khumi ndi awiriwo ndi kuwalamula kuti, “Musapite kwa anthu a mitundu ina kapena kulowa mʼmudzi uliwonse wa Asamariya. Koma pitani kwa nkhosa zotayika za banja la Israeli. Pamene mukupita, muzikalalikira uthenga uwu: ‘Ufumu wakumwamba wayandikira.’ Chiritsani odwala, ukitsani akufa, chiritsani akhate, tulutsani ziwanda. Munalandira kwaulere, perekani kwaulere.

“Musatenge ndalama zagolide kapena zasiliva kapena zakopala mʼzikwama mwanu; 10 musatenge thumba la paulendo, kapena malaya awiri kapena nsapato kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira chakudya chake. 11 Mukalowa mu mzinda ndi mʼmudzi uliwonse, funafunani munthu woyenera ndipo mukhale mʼnyumba mwake kufikira mutachoka. 12 Pamene mulowa mʼnyumba mupereke moni. 13 Mtendere wanu ukhale pa a mʼnyumbayo ngati ndi oyenera. Koma ngati siwoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu. 14 Ngati wina aliyense sakakulandirani kapena sakamvera mawu anu, musase fumbi la kumapazi anu pamene mutuluka mʼnyumbayo kapena mu mzindawo. 15 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti pa tsiku lachiweruziro, mlandu wa Sodomu ndi Gomora udzachepa kusiyana ndi wa mzindawo.

16 “Taonani ndikukutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu. Chifukwa chake khalani ochenjera ngati njoka ndi woona mtima ngati nkhunda. 17 Chenjerani ndi anthu pakuti adzakuperekani ku mabwalo amilandu nadzakukwapulani mʼmasunagoge mwawo. 18 Chifukwa cha Ine, mudzaperekedwa kwa olamulira ndi kwa mafumu kuti mukhale mboni kwa iwo ndi kwa a mitundu ina. 19 Koma pamene akumangani, inu musadandaule kuti mukanena bwanji kapena mukanena chiyani. Mudzapatsidwa pa nthawi imeneyo zoti munene, 20 pakuti sindinu mudzanena, koma Mzimu Woyera wa Atate anu, adzayankhula mwa inu.

21 “Mʼbale adzapereka mʼbale kuti aphedwe ndi abambo mwana wawo: ndipo ana adzawukira makolo awo ndi kuwapereka kuti aphedwe. 22 Anthu onse adzada inu chifukwa cha Ine, koma iye amene apirira mpaka kumapeto, adzapulumuka. 23 Pamene akuzunzani pamalo ena thawirani kwina. Pakuti ndikuwuzani zoonadi kuti simudzamaliza mizinda yonse ya Israeli Mwana wa Munthu asanabwere.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.