Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 86:1-10

Pemphero la Davide.

86 Ndimvereni Yehova ndipo mundiyankhe,
    pakuti ndine wosauka ndi wosowa.
Yangʼanirani moyo wanga, pakuti ndine wodzipereka kwa Inu.
    Inu ndinu Mulungu wanga;
    pulumutsani mtumiki wanu amene amadalira Inu.
Inu ndinu Mulungu wanga.
Mundichitire chifundo, Inu Ambuye,
    pakuti ndikuyitana Inu tsiku lonse.
Bweretsani chimwemwe kwa mtumiki wanu, Ambuye,
    pakuti ndimadalira Inu.

Inu Ambuye, ndinu wokhululuka ndi wabwino,
    wodzaza ndi chikondi kwa onse amene amayitana Inu.
Yehova imvani pemphero langa;
    mvetserani kulira kwanga kofuna chifundo.
Pa tsiku la mavuto anga ndidzayitana Inu,
    pakuti Inu mudzandiyankha.

Pakati pa milungu palibe wina wofanana nanu Ambuye;
    palibe ntchito zolingana ndi ntchito zanu.
Mitundu yonse ya anthu imene munayipanga
    idzabwera ndi kudzalambira pamaso panu Ambuye;
    iwo adzabweretsa ulemerero pa dzina lanu.
10 Pakuti ndinu wamkulu ndipo mumachita zodabwitsa;
    Inu nokha ndiye Mulungu.

Genesis 35:1-4

Yakobo Abwerera ku Beteli

35 Tsono Mulungu anati kwa Yakobo, “Nyamuka uchoke kuno kupita ku Beteli. Kumeneko ukamange guwa lansembe la Mulungu amene anadza kwa iwe pamene umathawa Esau, mʼbale wako.”

Choncho Yakobo anawuza a pa banja pake ndi onse amene anali naye kuti, “Chotsani milungu yachilendo imene muli nayo, ndipo mudziyeretse nokha ndi kusintha zovala zanu. Tiyeni tinyamuke kuchoka kuno kupita ku Beteli. Kumeneko ndikamumangira guwa lansembe Mulungu amene anandithandiza pa nthawi za masautso anga, komanso amene wakhala nane mʼmayendedwe anga onse.” Choncho anamupatsa Yakobo milungu yachilendo yonse imene anali nayo pamodzi ndi ndolo. Iye anazikwirira pansi pa mtengo wa thundu ku Sekemu.

Machitidwe a Atumwi 5:17-26

Atumwi Azunzidwa

17 Koma mkulu wa ansembe pamodzi ndi onse omuthandiza, amene anali a gulu la Asaduki, anachita nsanje. 18 Iwo anagwira atumwi ndi kuwatsekera mʼndende ya anthu wamba. 19 Koma usiku mngelo wa Ambuye anatsekula zitseko za ndende ndi kuwatulutsa 20 Mngeloyo anati, “Pitani, ku mabwalo a Nyumba ya Mulungu ndipo mukawuze anthu uthenga onse wamoyo watsopanowu.”

21 Kutacha mmawa, atumwi analowa mʼbwalo la mʼNyumba ya Mulungu, monga anawuzidwa ndipo anayamba kuphunzitsa anthu.

Mkulu wa ansembe pamodzi ndi omuthandiza ake amene anali naye anafika, anayitanitsa msonkhano wa Bwalo Lalikulu, ndilo bwalo la akulu onse a Israeli. Anatuma alonda kuti akatenge atumwi aja kundende. 22 Koma alonda aja atafika kundende, sanawapezemo. Iwo anabwerera nakawafotokozera 23 kuti, “Tinakapeza ndende ili chitsekere ndithu, ndi alonda atayimirira pa khomo, koma pamene tinatsekula zitseko, sitinapezemo munthu aliyense mʼkatimo.” 24 Mkulu wa alonda a Nyumba ya Mulungu ndi akulu a ansembe atamva zimenezi anathedwa nzeru, osadziwa kuti zimenezi zidzatha bwanji.

25 Ndipo wina anabwera ndi kuti, “Taonani! Anthu aja amene munawatsekera mʼndende ali ku Nyumba ya Mulungu ndipo akuphunzitsa anthu.” 26 Pamenepo mkulu wa alonda pamodzi ndi alonda anakawatenga atumwi. Sanakawatenge mwaukali, chifukwa amaopa kuti anthu angawaponye miyala.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.