Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 116:1-2

116 Ndimakonda Yehova pakuti Iyeyo amamva mawu anga;
    Iye amamva kulira kwanga kopempha chifundo.
Pakuti ananditchera khutu,
    ndidzayitana Iye masiku onse a moyo wanga.

Masalimo 116:12-19

12 Ndingamubwezere chiyani Yehova,
    chifukwa cha zokoma zake zonse zimene wandichitira?
13 Ndidzakweza chikho cha chipulumutso
    ndipo ndidzayitana dzina la Yehova.
14 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova
    pamaso pa anthu ake onse.

15 Imfa ya anthu oyera mtima
    ndi yamtengowapatali pamaso pa Yehova.
16 Inu Yehova, zoonadi ndine mtumiki wanu:
    ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu;
    Inu mwamasula maunyolo anga.

17 Ndidzapereka nsembe yachiyamiko kwa Inu
    ndipo ndidzayitanira pa dzina la Yehova.
18 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova
    pamaso pa anthu ake onse,
19 mʼmabwalo a nyumba ya Yehova,
    mʼkati mwako iwe Yerusalemu.

Tamandani Yehova.

Genesis 21:1-7

Kubadwa kwa Isake

21 Yehova anakomera mtima Sara monga ananenera, ndipo Yehovayo anachita monga momwe analonjezera. Sara anakhala ndi pathupi ndipo anamuberekera Abrahamu mwana wamwamuna mu ukalamba wake, pa nyengo imene Mulungu anamulonjeza. Abrahamu anapereka dzina loti Isake kwa mwana wamwamuna amene Sara anamuberekera. Isake atakwanitsa masiku asanu ndi atatu, Abrahamu anamuchita mdulidwe monga Mulungu anamulamulira. Abrahamu anali ndi 100 pamene mwana wake Isake anabadwa.

Sara anati, “Mulungu wandibweretsera mseko, ndipo aliyense amene adzamva zimenezi adzaseka nane pamodzi.” Ndipo anawonjezera kuti, “Ndani akanamuwuza Abrahamu kuti Sara nʼkudzayamwitsako ana? Chonsecho ndamubalira mwana wamwamuna kuwukalamba wake.”

Ahebri 3:1-6

Yesu ndi Wamkulu Kuposa Mose

Nʼchifukwa chake abale oyera mtima, amenenso munayitanidwa ndi kumwamba, lingalirani za Yesu amene ndi Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chikhulupiriro chimene timavomereza. Iye anali wokhulupirika kwa Mulungu amene anamupatsa udindowo, monga momwe Mose anali wokhulupirika mʼnyumba yonse ya Mulungu. Yesu anapezeka woyenera kulandira ulemu waukulu kuposa Mose, monga momwemonso womanga nyumba amalandira ulemu waukulu kuposa nyumbayo. Pakuti nyumba iliyonse imamangidwa ndi munthu wina, koma amene anapanga zonse ndi Mulungu. Mose anali wokhulupirika monga mtumiki mʼnyumba yonse ya Mulungu, kuchitira umboni zimene zidzayankhulidwe mʼtsogolo. Koma Khristu ndi wokhulupirika monga mwana pa nyumba ya Mulungu. Ndipo ndife nyumba yake ngati tipitirire kulimbika mtima ndi kunyadira zomwe tikuyembekerazo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.