Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
24 Ntchito zanu ndi zochulukadi Inu Yehova!
Munazipanga zonse mwanzeru,
dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.
25 Kuli nyanja yayikulu ndi yotambalala,
yodzaza ndi zolengedwa zosawerengeka,
zamoyo zanu zazikulu ndi zazingʼono zomwe.
26 Kumeneko sitima zapamadzi zimayenda uku ndi uku,
ndiponso Leviyatani amene munamulenga kuti asewere kumeneko.
27 Zonsezi zimayangʼana kwa Inu
kuti muzipatse chakudya chawo pa nthawi yake yoyenera.
28 Mukazipatsa,
zimachisonkhanitsa pamodzi;
mukatsekula dzanja lanu,
izo zimakhutitsidwa ndi zinthu zabwino.
29 Mukabisa nkhope yanu,
izo zimachita mantha aakulu;
mukachotsa mpweya wawo,
zimafa ndi kubwerera ku fumbi.
30 Mukatumiza mzimu wanu,
izo zimalengedwa
ndipo mumakozanso maonekedwe a dziko lapansi.
31 Ulemerero wa Yehova ukhalebe mpaka muyaya;
Yehova akondwere ndi ntchito ya manja ake;
32 Iye amene amayangʼana dziko lapansi ndipo limanjenjemera,
amene amakhudza mapiri ndipo amatuluka utsi.
33 Ine ndidzayimbira Yehova moyo wanga wonse;
ndidzayimbira matamando Mulungu wanga nthawi yonse imene ndili ndi moyo.
34 Zolingalira zanga zikhale zomukomera Iye,
pamene ndikusangalala mwa Yehova.
35 Koma anthu ochimwa awonongeke pa dziko lapansi
ndipo anthu oyipa asapezekenso.
Tamanda Yehova, Iwe moyo wanga.
Tamandani Yehova.
Yankho la Yehova
18 Pamenepo Yehova adzachitira nsanje dziko lake
ndi kuchitira chisoni anthu ake.
19 Yehova adzawayankha kuti,
“Ine ndikukutumizirani tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta
ndipo mudzakhuta ndithu;
sindidzakuperekaninso kuti mukhale chitonzo
kwa anthu a mitundu ina.
20 “Ine ndidzachotsa ankhondo akumpoto kuti apite kutali ndi inu,
kuwapirikitsira ku dziko lowuma ndi lachipululu,
gulu lawo lakutsogolo ndidzalipirikitsira ku nyanja ya kummawa
ndi gulu lawo lakumbuyo, ku nyanja ya kumadzulo.
Ndipo mitembo yawo idzawola,
fungo lake lidzamveka.”
Zoonadi Yehova wachita zinthu zazikulu.
21 Iwe dziko usachite mantha;
sangalala ndipo kondwera.
Zoonadi Yehova wachita zinthu zazikulu.
22 Inu nyama zakuthengo, musachite mantha,
pakuti msipu wa ku chipululu ukuphukira.
Mitengo ikubala zipatso zake;
mitengo ya mkuyu ndi mpesa ikubereka kwambiri.
23 Inu anthu a ku Ziyoni sangalalani,
kondwerani mwa Yehova Mulungu wanu,
pakuti wakupatsani
mvula yoyambirira mwachilungamo chake.
Iye wakutumizirani mivumbi yochuluka,
mvula yoyambirira ndi mvula ya nthawi ya mphukira, monga poyamba paja.
24 Pa malo opunthira padzaza tirigu;
mʼmitsuko mudzasefukira vinyo watsopano ndi mafuta.
25 “Ine ndidzakubwezerani zonse zimene zinawonongedwa ndi dzombe,
dzombe lalikulu ndi dzombe lalingʼono,
dzombe lopanda mapiko ndi dzombe lowuluka;
gulu langa lalikulu la nkhondo limene ndinalitumiza pakati panu.
26 Mudzakhala ndi chakudya chambiri, mpaka mudzakhuta,
ndipo mudzatamanda dzina la Yehova Mulungu wanu,
amene wakuchitirani zodabwitsa;
ndipo anthu anga sadzachitanso manyazi.
27 Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndili mu Israeli,
kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu,
ndi kuti palibenso wina;
ndipo anthu anga sadzachitanso manyazi.
Tsiku la Yehova
28 “Ndipo patapita nthawi,
ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse.
Ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenera,
nkhalamba zanu zidzalota maloto,
anyamata anu adzaona masomphenya.
29 Ngakhalenso pa antchito anga aamuna ndi aakazi
ndidzakhuthulira Mzimu wanga masiku amenewo.
Ulemerero wa Mʼtsogolo
18 Ine ndiganiza kuti masautso amene tikuwamva nthawi ino, sakufanana ndi ulemerero umene udzaonetsedwa mwa ife. 19 Pakuti chilengedwe chikudikira ndi chiyembekezo kuonetsedwa poyera kwa ana a Mulungu. 20 Pakuti chilengedwe sichinasankhe kugonjera zopanda pake, koma mwachifuniro cha Iye amene analola kuti chigonjere. Koma chili ndi chiyembekezo 21 chakuti chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi ndi kulandiranso ufulu ndi ulemerero wa ana a Mulungu.
22 Ife tikudziwa kuti chilengedwe chonse chakhala chikubuwula ndi ululu ngati ululu wa nthawi yobereka mwana mpaka tsopano lino. 23 Si zokhazo ayi, ngakhale ife tomwe, amene tili ndi zipatso zoyamba za Mzimu, tikubuwulira mʼkati mwathu pomwe tikudikira mwachidwi kusankhidwa kwathu ngati ana, kuwomboledwa kwa matupi athu. 24 Pakuti ife tinapulumutsidwa mʼchiyembekezo ichi. Koma chiyembekezo chimene chimaoneka si chiyembekezo ayi. Kodi ndani amene amayembekezera chimene ali nacho kale?
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.