Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 33:12-22

12 Wodala mtundu wa anthu umene Mulungu wake ndi Yehova,
    anthu amene Iye anawasankha kukhala cholowa chake.
13 Kuchokera kumwamba Yehova amayangʼana pansi
    ndi kuona anthu onse;
14 kuchokera ku malo ake okhalako Iye amayangʼanira
    onse amene amakhala pa dziko lapansi.
15 Iye amene amapanga mitima ya onse,
    amaona zonse zimene akuchita.
16 Palibe mfumu imene imapulumutsidwa chifukwa cha kukula kwa gulu lake lankhondo;
    palibe msilikali amene amathawa ndi mphamvu zake zazikulu.
17 Kavalo ndi chiyembekezo cha chabechabe cha chipulumutso,
    ngakhale ali ndi mphamvu yayikulu sangathe kupulumutsa.
18 Koma maso a Yehova ali pa iwo amene amaopa Iye;
    amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosatha,
19 kuwawombola iwo ku imfa
    ndi kuwasunga ndi moyo nthawi ya njala.

20 Ife timadikira kwa Yehova mwachiyembekezo;
    Iye ndiye thandizo lathu ndi chishango chathu.
21 Mwa Iye mitima yathu imakondwera,
    pakuti ife timadalira dzina lake loyera.
22 Chikondi chanu chosatha
    chikhale pa ife Inu Yehova, pamene tikuyembekeza kwa Inu.

Eksodo 20:1-21

Malamulo Khumi

20 Ndipo Mulungu anayankhula mawu onse awa nati:

“Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa ku Igupto, mʼdziko la ukapolo.

“Usakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha.”

“Usadzipangire chofanizira chinthu chilichonse chakumwamba kapena cha pa dziko lapansi kapena cha mʼmadzi a pansi pa dziko. Usazigwadire kapena kuzipembedza, pakuti Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, wolanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane. Koma ndimaonetsa chikondi chosasinthika ku mibado miyandamiyanda ya anthu amene amandikonda, ndi kusunga malamulo anga.

“Usagwiritse ntchito molakwika dzina la Yehova Mulungu wako, pakuti Yehova adzamutenga kukhala wochimwa aliyense amene akugwiritsa ntchito dzina lakelo molakwika.

“Uzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika. Uzigwira ntchito zako zonse masiku asanu ndi limodzi. 10 Koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, tsiku loperekedwa kwa Yehova Mulungu wako. Tsiku limeneli musagwire ntchito iliyonse, inuyo kapena mwana wanu wamwamuna kapena mwana wanu wamkazi, wantchito wanu wamwamuna kapena mdzakazi wanu, ziweto zanu kapena mlendo amene akukhala mʼmudzi mwanu. 11 Pakuti Yehova anapanga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo mʼmasiku asanu ndi limodzi. Iye anapuma pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Kotero Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale loyera.

12 “Lemekeza abambo ako ndi amayi ako kuti ukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.

13 “Usaphe.

14 “Usachite chigololo.

15 “Usabe.

16 “Usapereke umboni womunamizira mnzako.

17 “Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako kapena wantchito wake wamwamuna kapena mdzakazi wake, ngʼombe yake kapena bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.”

18 Pamene anthu ankamva mabingu ndi kuona ziphaliwali ndi kumvanso lipenga ndi kuona utsi umene umafuka mʼphiri, ananjenjemera ndi mantha. Ndipo iwo anayima patali. 19 Ndipo anati kwa Mose, “Iwe utiyankhule ndipo tidzamvera. Koma usalole kuti Mulungu atiyankhule, tingafe.”

20 Koma Mose anati kwa anthuwo, “Musachite mantha. Mulungu wabwera kudzakuyesani kuti mukhale ndi mtima woopa Mulungu kuti musamuchimwire.”

21 Anthu aja anayima patali koma Mose anayandikira mtambo wakuda kumene kunali Mulungu.

Mateyu 5:1-12

Chiphunzitso cha pa Phiri

Iye ataona anthu ambiri, anakwera pa phiri nakhala pansi. Ndipo ophunzira ake anabwera kwa Iye, ndipo anayamba kuwaphunzitsa kuti,

“Odala ndi amene ali osauka mu mzimu,
    chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.
Odala ndi amene ali achisoni,
    chifukwa adzatonthozedwa.
Odala ndi amene ali ofatsa,
    chifukwa adzalandira dziko lapansi.
Odala ndi amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo,
    chifukwa adzakhutitsidwa.
Odala ndi amene ali ndi chifundo,
    chifukwa adzawachitira chifundo.
Odala ndi amene ali oyera mtima,
    chifukwa adzaona Mulungu.
Ndi odala amene amabweretsa mtendere,
    chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.
10 Odala ndi amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo,
    pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo.”

11 “Inu ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani, kukunenerani zoyipa zilizonse ndi kukunamizirani chifukwa cha Ine. 12 Sangalalani, kondwerani chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu kumwamba, chifukwa moterenso ndi mmene anazunzira aneneri inu musanabadwe.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.