Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 33:12-22

12 Wodala mtundu wa anthu umene Mulungu wake ndi Yehova,
    anthu amene Iye anawasankha kukhala cholowa chake.
13 Kuchokera kumwamba Yehova amayangʼana pansi
    ndi kuona anthu onse;
14 kuchokera ku malo ake okhalako Iye amayangʼanira
    onse amene amakhala pa dziko lapansi.
15 Iye amene amapanga mitima ya onse,
    amaona zonse zimene akuchita.
16 Palibe mfumu imene imapulumutsidwa chifukwa cha kukula kwa gulu lake lankhondo;
    palibe msilikali amene amathawa ndi mphamvu zake zazikulu.
17 Kavalo ndi chiyembekezo cha chabechabe cha chipulumutso,
    ngakhale ali ndi mphamvu yayikulu sangathe kupulumutsa.
18 Koma maso a Yehova ali pa iwo amene amaopa Iye;
    amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosatha,
19 kuwawombola iwo ku imfa
    ndi kuwasunga ndi moyo nthawi ya njala.

20 Ife timadikira kwa Yehova mwachiyembekezo;
    Iye ndiye thandizo lathu ndi chishango chathu.
21 Mwa Iye mitima yathu imakondwera,
    pakuti ife timadalira dzina lake loyera.
22 Chikondi chanu chosatha
    chikhale pa ife Inu Yehova, pamene tikuyembekeza kwa Inu.

Eksodo 19:16-25

16 Mʼmamawa wa tsiku lachitatu kunali mabingu, ziphaliwali ndi mtambo wakuda umene unaphimba phiri, ndiponso lipenga lolira kwambiri. Aliyense ku misasa kuja ananjenjemera ndi mantha. 17 Ndipo Mose anatsogolera anthu kutuluka mʼmisasa kukakumana ndi Mulungu, ndipo anayima mʼmunsi mwa phiri. 18 Phiri la Sinai linakutidwa ndi utsi, chifukwa Yehova anatsika ndi moto pa phiripo. Utsi unakwera ngati wochokera mʼngʼanjo yamoto ndipo phiri lonse linagwedezeka kwambiri. 19 Liwu la lipenga linkakulirakulira. Tsono Mose anayankhula ndipo Yehova anamuyankha ndi mabingu.

20 Yehova anatsika nafika pamwamba pa phiri la Sinai, ndipo anayitana Mose kuti apite pa phiripo. Choncho Mose anakwera, 21 ndipo Yehova anati kwa iye, “Tsika ukawachenjeze anthu kuti asayesere kudutsa malire kuti adzandione chifukwa ambiri a iwo adzafa. 22 Ngakhale ansembe amene amatumikira pamaso pa Yehova ayenera kudziyeretsa kuopa kuti ndingadzawalange.”

23 Mose anati kwa Yehova, “Anthu sangakwere phiri la Sinai chifukwa inu munatichenjeza. Lembani malire kuzungulira phiri ndipo mulipatule kuti likhale loyera.”

24 Yehova anayankha, “Tsika ukamutenge Aaroni. Koma ansembe ndi anthu asayesere kubzola malire kuti abwere kwa Yehova chifukwa Iye adzawalanga.”

25 Ndipo Mose anatsika ndi kukawawuza anthuwo.

Aroma 8:14-17

14 Onse amene amatsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu ndi ana a Mulungu. 15 Mzimu amene inu munalandira samakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha, koma Mzimu amakusandutsani ana. Ndipo mwa Iye ife timafuwula kuti, “Abba, Atate.” 16 Mzimu mwini amavomerezana ndi mzimu wathu kuti ife ndife ana a Mulungu. 17 Tsono ngati tili ana ake, ndiye kuti ndife olowa mʼmalo a Mulungu ndi olowa mʼmalo pamodzi ndi Khristu. Ngati ife timva zowawa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.