Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 33:12-22

12 Wodala mtundu wa anthu umene Mulungu wake ndi Yehova,
    anthu amene Iye anawasankha kukhala cholowa chake.
13 Kuchokera kumwamba Yehova amayangʼana pansi
    ndi kuona anthu onse;
14 kuchokera ku malo ake okhalako Iye amayangʼanira
    onse amene amakhala pa dziko lapansi.
15 Iye amene amapanga mitima ya onse,
    amaona zonse zimene akuchita.
16 Palibe mfumu imene imapulumutsidwa chifukwa cha kukula kwa gulu lake lankhondo;
    palibe msilikali amene amathawa ndi mphamvu zake zazikulu.
17 Kavalo ndi chiyembekezo cha chabechabe cha chipulumutso,
    ngakhale ali ndi mphamvu yayikulu sangathe kupulumutsa.
18 Koma maso a Yehova ali pa iwo amene amaopa Iye;
    amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosatha,
19 kuwawombola iwo ku imfa
    ndi kuwasunga ndi moyo nthawi ya njala.

20 Ife timadikira kwa Yehova mwachiyembekezo;
    Iye ndiye thandizo lathu ndi chishango chathu.
21 Mwa Iye mitima yathu imakondwera,
    pakuti ife timadalira dzina lake loyera.
22 Chikondi chanu chosatha
    chikhale pa ife Inu Yehova, pamene tikuyembekeza kwa Inu.

Eksodo 19:1-9

Pa Phiri la Sinai

19 Ana a Israeli aja anafika ku chipululu cha Sinai pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu chichokere mʼdziko la Igupto. Atachoka ku Refidimu, anafika ku Sinai, ndipo Aisraeli anamangako misasa yawo moyangʼanana ndi phirilo.

Mose anakwera ku phiri kukakumana ndi Mulungu ndipo Yehova anamuyitana nati, “Ukawuze zidzukulu za Yakobo, ana onse a Israeli kuti, ‘Inu eni munaona zimene ndinawachitira Aigupto ndiponso mmene ndinakunyamulirani, monga mmene chiwombankhanga chimanyamulira ana ake pa mapiko,’ ndikukubweretsani kwa Ine. Tsopano, ngati mumveradi mawu anga ndi kusunga pangano langa, mudzakhala chuma changa chapamtima pakati pa mitundu yonse. Ngakhale kuti dziko lonse lapansi ndi langa, inu mudzakhala ansembe achifumu ndi mtundu woyera mtima. Awa ndi mawu amene uyenera kuwawuza Aisraeli.”

Ndipo Mose anabwerera ndi kuyitanitsa akuluakulu. Atabwera anawafotokozera mawu amene Yehova anamulamulira kuti adzanene. Anthu onse anayankha pamodzi kuti, “Ife tidzachita zonse zimene Yehova wanena.” Choncho Mose anabweza yankho lawo kwa Yehova.

Yehova anati kwa Mose, “Ine ndibwera kwa iwe mu mtambo wakuda kuti anthu adzandimve ndikuyankhula ndi iwe. Choncho adzakukhulupirira nthawi zonse.” Kenaka Mose anawuza Yehova zimene anthu ananena.

Machitidwe a Atumwi 2:1-11

Kubwera kwa Mzimu Woyera

Litafika tsiku la chikondwerero cha Pentekosite, onse anali pamodzi. Mwadzidzidzi kunamveka mkokomo kuchokera kumwamba ngati wa mphepo yamphamvu, ndipo inadzaza nyumba yonse imene amakhala. Iwo anaona zinthu zokhala ngati malilime amoto ogawikana ndipo anakhala pa aliyense wa iwo. Ndipo onse anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kuyankhula mu ziyankhulo zina, monga Mzimu Woyerayo anawayankhulitsa.

Ayuda woopa Mulungu ochokera ku mayiko onse a dziko lapansi ankakhala mu Yerusalemu nthawi imeneyi. Utamveka mkokomo uja, gulu la anthu linasonkhana. Anthuwo anadabwa chifukwa aliyense anawamva atumwiwo akuyankhula ziyankhulo zosiyanasiyana. Mothedwa nzeru anafunsana kuti, “Kodi anthu onse amene akuyankhulawa si Agalileya? Nanga bwanji aliyense wa ife akuwamva iwo mu chinenero cha kwawo? Apanti, Amedi ndi Aelami; okhala ku Mesopotamiya, ku Yudeya ndi ku Kapadokiya, ku Ponto ndi ku Asiya, 10 ku Frugiya ndi Pamfiliya, ku Igupto ndi ku madera a ku Libiya kufupi ndi ku Kurene; alendo ochokera ku Roma, 11 Ayuda ndi otsatira chipembedzo cha Chiyuda onse pamodzi; Akrete ndi Aarabu, ife tonse tikuwamva akuyankhula za ntchito zodabwitsa za Mulungu mu ziyankhulo zathu.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.