Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
99 Yehova akulamulira,
mitundu ya anthu injenjemere;
Iye wakhala pa mpando wake waufumu, pakati pa akerubi,
dziko lapansi ligwedezeke.
2 Mʼziyoni wamkulu ndi Yehova;
Iye ndi wokwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.
3 Anthu atamande dzina lanu lalikulu ndi loopsa kwambiri,
Iye ndi woyera.
4 Mfumu yamphamvu, iyo imakonda chilungamo
Inu mwakhazikitsa khalidwe losakondera;
mwachita zolungama ndi zoyenera mwa Yakobo.
5 Kwezani Yehova Mulungu wathu
ndipo mulambireni pa mapazi ake;
Iye ndi woyera.
6 Mose ndi Aaroni anali ena mwa ansembe ake,
Samueli anali pamodzi ndi iwo amene anayitana pa dzina lake;
iwo anayitana Yehova
ndipo Iyeyo anawayankha.
7 Iye anayankhula nawo kuchokera mʼchipilala cha mtambo;
iwo anasunga malamulo ake ndi zophunzitsa zomwe anawapatsa.
8 Inu Yehova Mulungu wathu,
munawayankha iwo;
Inu kwa Israeli munali Mulungu wokhululuka,
ngakhale munawalanga pa zochita zawo zoyipa.
9 Kwezani Yehova Mulungu wathu
ndipo mumulambire pa phiri lake loyera,
pakuti Yehova Mulungu wathu ndi woyera.
41 Tsiku lotsatira, gulu lonse la Aisraeli linatsutsana ndi Mose ndi Aaroni. Iwo anati, “Inu mwapha anthu a Yehova.”
42 Koma pamene anthuwo anasonkhana kuti atsutsane ndi Mose ndi Aaroni, atatembenuka kuyangʼana ku tenti ya msonkhano, mwadzidzidzi mtambo unaphimba tentiyo ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera. 43 Pamenepo Mose ndi Aaroni anapita patsogolo pa tenti ya msonkhano ija 44 ndipo Yehova anawuza Mose kuti, 45 “Chokani pakati pa gulu la anthuwa kuti ndiwawononge kamodzinʼkamodzi.” Ndipo iwo anagwa pansi chafufumimba.
46 Kenaka Mose anawuza Aaroni kuti, “Tenga chofukizira chako ndipo ikamo lubani pamodzi ndi moto wochokera pa guwa lansembe, fulumira, pita pa gulu la anthuwo ndipo ukachite nsembe yopepesera machimo awo popeza mkwiyo wa Yehova wafika, mliri wayamba.” 47 Ndipo Aaroni anachita monga ananenera Mose, nathamangira mʼkatikati mwa gulu la anthuwo. Pamenepo nʼkuti mliri utayamba kale pakati pa anthu aja ndipo Aaroni anafukiza lubani ndi kupereka nsembe yopepesera machimo awo. 48 Iye anayimirira pakati pa anthu amoyo ndi akufa ndipo mliri unaleka. 49 Komabe anthu 14, 700 anafa ndi mliriwo, kuwonjezera pa aja amene anafa chifukwa cha Kora. 50 Ndipo Aaroni anabwerera kwa Mose ku khomo la tenti ya msonkhano, chifukwa mliriwo unali utatha.
7 Chimaliziro cha zinthu zonse chili pafupi. Choncho khalani maso ndi odziletsa kuti muthe kupemphera. 8 Koposa zonse muzikondana wina ndi mnzake kwambiri, chifukwa chikondi chimaphimba machimo ambiri. 9 Muzisamalirana wina ndi mnzake osamanyinyirika. 10 Aliyense agwiritse ntchito mokhulupirika mphatso iliyonse imene anayilandira potumikira ena ngati adindo ogwiritsa bwino ntchito mphatso za Mulungu za mitundumitundu. 11 Ngati wina ayankhula, ayankhuledi mawu enieni a Mulungu. Ngati wina atumikira, atumikire ndi mphamvu imene Mulungu amapereka, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu mpaka muyaya, Ameni.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.