Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Yesu Akwera Kumwamba
6 Atumwi atasonkhana pamodzi, iwo anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi nthawi ino mubwezeretsa ufumu kwa Israeli?”
7 Yesu anawawuza kuti, “Sikofunika kuti mudziwe za nthawi kapena masiku amene Atate ayika mwa ulamuliro wawo. 8 Koma mudzalandira mphamvu Mzimu Woyera akadzafika pa inu; ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”
9 Atatha kuyankhula zimenezi, Yesu anatengedwa kupita kumwamba ophunzira ake akuona, ndipo anabisika mʼmitambo.
10 Yesu akukwera kumwamba, ophunzira ake anayangʼanitsitsa ndi chidwi mʼmitambo. Mwadzidzidzi anaona anthu awiri ovala zoyera atayimirira pambali pawo. 11 Iwo anati, “Inu, anthu a ku Galileya, chifukwa chiyani mukuyima ndi kumayangʼana mʼmitambo? Yesu amene wachotsedwa pakati panu ndi kupita kumwamba, adzabweranso mʼnjira yomweyi mwamuona akupita kumwamba.”
Matiyasi Alowa Mʼmalo mwa Yudasi Isikarioti
12 Pamenepo atumwi anabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku phiri la Olivi, mtunda wosakwana kilomita kuchokera mu mzindamo. 13 Atafika mu mzindamo, analowa mʼchipinda chammwamba kumene amakhala. Amene analipo anali awa: Petro, Yohane, Yakobo ndi Andreya; Filipo ndi Tomasi, Bartumeyu ndi Mateyu; Yakobo mwana wa Alifeyo ndi Simoni Zelote ndi Yuda mwana wa Yakobo. 14 Onsewa ndi mtima umodzi anapitiriza kupemphera pamodzi ndi amayi, ndi Mariya amayi ake a Yesu, ndiponso abale ake a Yesu.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
68 Adzuke Mulungu, adani ake amwazikane;
adani ake athawe pamaso pake.
2 Monga momwe mphepo imachotsera utsi; Inu muwawulutsire kutali.
Monga phula limasungunukira pa moto,
oyipa awonongeke pamaso pa Mulungu.
3 Koma olungama asangalale
ndi kukondwera pamaso pa Mulungu;
iwo akondwere ndi kusangalala.
4 Imbirani Mulungu imbirani dzina lake matamando,
mukwezeni Iye amene amakwera pa mitambo;
dzina lake ndi Yehova ndipo sangalalani pamaso pake.
5 Atate wa ana amasiye, mtetezi wa akazi amasiye,
ndiye Mulungu amene amakhala mʼmalo oyera.
6 Mulungu amakhazikitsa mtima pansi osungulumwa mʼmabanja,
amatsogolera amʼndende ndi kuyimba;
koma anthu osamvera amakhala ku malo owuma a dziko lapansi.
7 Pamene munatuluka kutsogolera anthu anu, Inu Mulungu,
pamene munayenda kudutsa chipululu,
8 dziko lapansi linagwedezeka, miyamba inakhuthula pansi mvula,
pamaso pa Mulungu, Mmodzi uja wa ku Sinai.
Pamaso pa Mulungu, Mulungu wa Israeli.
9 Munapereka mivumbi yochuluka, Inu Mulungu;
munatsitsimutsa cholowa chanu cholefuka.
10 Anthu anu anakhala mʼmenemo
ndipo munapatsa anthu osauka zimene zinkawasowa chifukwa cha ubwino wanu Mulungu.
32 Imbirani Mulungu Inu mafumu a dziko lapansi
imbirani Ambuye matamando.
Sela
33 Kwa Iye amene amakwera pa mitambo yakalekale ya mmwamba
amene amabangula ndi mawu amphamvu.
34 Lengezani za mphamvu za Mulungu,
amene ulemerero wake uli pa Israeli
amene mphamvu zake zili mʼmitambo.
35 Ndinu woopsa, Inu Mulungu mʼmalo anu opatulika;
Mulungu wa Israeli amapereka mphamvu ndi nyonga kwa anthu ake.
Matamando akhale kwa Mulungu!
Kumva Zowawa Chifukwa cha Chikhristu
12 Abale okondedwa musadabwe ndi mayesero owawa amene mukukumana nawo ngati kuti china chake chachilendo chakuchitikirani. 13 Koma kondwerani popeza mukumva zowawa pamodzi ndi Khristu, kuti mudzakondwere kwakukulu pamene ulemerero wake udzaonekera. 14 Ngati akuchitani chipongwe chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala, ndiye kuti Mzimu waulemerero wa Mulungu uli pa inu.
6 Choncho, mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthawi yake adzakukwezeni. 7 Tayani pa Iye nkhawa zanu zonse chifukwa ndiye amakusamalani.
8 Khalani odziretsa ndi atcheru. Mdani wanu mdierekezi amayendayenda monga mkango wobangula kufunafuna wina kuti amumeze. 9 Mukaneni iye, ndipo mukhazikike mʼchikhulupiriro, chifukwa mukudziwa kuti abale anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso akumva zowawa zomwezi.
10 Ndipo Mulungu wachisomo chonse, amene anakuyitanani ku ulemerero wake wamuyaya mwa Khristu, mutamva zowawa pa kanthawi, adzakukonzaninso ndi kukulimbitsani pa maziko olimba. 11 Kwa Iye kukhale mphamvu mpaka muyaya, Ameni.
Yesu Adzipempherera Yekha
17 Yesu atatha kunena izi, anayangʼana kumwamba ndipo anapemphera:
“Atate, nthawi yafika. Lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanuyo akulemekezeni Inu. 2 Pakuti Inu munamupatsa Iye ulamuliro pa anthu onse kuti apereke moyo wosatha kwa onse amene mwamupatsa. 3 Tsono moyo wosathawo ndi uwu: Iwo akudziweni Inu, Mulungu yekhayo woona, ndi Yesu Khristu, amene Inu mwamutuma. 4 Ine ndabweretsa ulemerero wanu pa dziko pamene ndamaliza ntchito imene munandipatsa kuti ndi igwire. 5 Ndipo tsopano, Atate, ndilemekezeni Ine pamaso panu ndi ulemerero uja umene ndinali nawo kwa Inu dziko lapansi lisanayambe.
Yesu Apempherera Ophunzira Ake
6 “Ine ndawadziwitsa za Inu anthu amene munandipatsa mʼdziko lapansi. Iwo anali anu. Inu munawapereka kwa Ine ndipo amvera mawu anu. 7 Tsopano akudziwa kuti zonse zimene munandipatsa nʼzochokera kwa Inu. 8 Pakuti Ine ndiwapatsa mawu amene Inu munandipatsa ndipo awalandira. Iwo akudziwa ndithu kuti Ine ndinachokera kwa Inu, ndipo akukhulupirira kuti Inu ndiye amene munandituma Ine. 9 Ine ndikuwapempherera. Ine sindikupempherera dziko lapansi, koma anthu amene Inu mwandipatsa, pakuti ndi anu. 10 Zonse zimene Ine ndili nazo ndi zanu, ndipo zonse zimene Inu muli nazo ndi zanga. Choncho Ine ndalemekezedwa mwa iwowo. 11 Ine sindikukhalanso mʼdziko lapansi nthawi yayitali, koma iwo akanali mʼdziko lapansi. Ine ndikubwera kwa Inu. Atate Woyera, atetezeni ndi mphamvu za dzina lanu. Dzina limene munandipatsa Ine, kuti iwo akhale amodzi monga Ife tili amodzi.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.