Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 93

93 Yehova akulamulira, wavala ulemerero;
    Yehova wavala ulemerero ndipo wadzimangirira mphamvu,
    dziko lonse lakhazikika kolimba; silingasunthidwe.
Mpando wanu waufumu unakhazikika kalekale;
    Inu ndinu wamuyaya.

Nyanja zakweza Inu Yehova,
    nyanja zakweza mawu ake;
    nyanja zakweza mafunde ake ochita mkokomo.
Yehova ndi wamphamvu kupambana mkokomo wa madzi ambiri,
    ndi wamphamvu kupambana mafunde a nyanja,
    Yehova mmwamba ndi wamphamvu.

Malamulo anu Yehova ndi osasinthika;
    chiyero chimakongoletsa nyumba yanu
    mpaka muyaya.

Deuteronomo 31:1-13

Yoswa Alowa Mʼmalo mwa Mose

31 Tsono Mose anapita ndi kukayankhula mawu awa kwa Aisraeli onse: “Tsopano ndili ndi zaka 120, ndipo sindingathenso kukutsogolerani. Yehova wandiwuza kuti, ‘Iwe sudzawoloka Yorodani.’ Mwini wake Yehova Mulungu wanu ndiye amene adzakutsogolerani powoloka. Iye adzawononga mitundu ina yonse, ndipo inu mudzatenga dziko lawo. Yoswa adzakutsogoleraninso powoloka, monga momwe ananenera Yehova. Ndipo Yehova adzawawononga iwo monga momwe anawonongera Sihoni ndi Ogi, mafumu Aamori, amene Iye anawawononga pamodzi ndi dziko lawo. Ambuye adzawapereka kwa inu, ndipo inu mukawachitire zonse zimene ndakulamulani. Khalani amphamvu ndi olimba mtima. Musachite nawo mantha kapena kunjenjemera pamaso pawo, chifukwa Yehova Mulungu wanu apita nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani.”

Pamenepo Yehova anayitana Yoswa pamaso pa Aisraeli onse ndipo anamuwuza kuti, “Khala wamphamvu ndi wolimba mtima, pakuti iwe udzatsogolera anthu awa ku dziko limene Yehova analumbira kulipereka kwa makolo awo, ndipo iwe ukaligawe pakati pawo kuti likakhale cholowa chawo. Yehova mwini ndiye akukutsogolerani ndipo adzakhala nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani. Usachite mantha ndiponso usataye mtima.”

Kuwerenga Malamulo

Choncho Mose analemba malamulo awa nawapereka kwa ansembe, ana Alevi, amene amanyamula Bokosi la Chipangano la Yehova, ndiponso kwa akuluakulu onse a Aisraeli. 10 Kenaka Mose anawalamula kuti, “Pamapeto pa zaka zisanu ndi ziwiri zilizonse, chaka cha kukhululukidwa ngongole, pa nthawi ya Chikondwerero cha Misasa, 11 pamene Aisraeli onse abwera kudzaonekera pamaso pa Yehova Mulungu wanu pamalo pamene Iye adzasankhe, mudzawerenge malamulo onsewa iwo akumva. 12 Mudzasonkhanitse anthu onse pamodzi, amuna, akazi ndi ana pamodzi ndi alendo amene akukhala mʼmizinda yanu, kuti adzawamve ndi kuphunzira kuopa Yehova Mulungu wanu ndi kutsatira mosamala mawu onse a mʼmalamulowa. 13 Ana awo amene sadziwa malamulo awa, ayenera kuwamva ndi kuphunzira kuopa Yehova Mulungu wanu nthawi zonse pamene mukukhala mʼdziko limene mukuwoloka Yorodani kukalitenga.”

Yohane 16:16-24

Chisoni cha Ophunzira Chisandulika Chimwemwe

16 Yesu anapitiriza kuyankhula kuti, “Mwa kanthawi kochepa, simudzandionanso, ndipo patatha nthawi pangʼono mudzandionanso.”

17 Ena a ophunzira ake anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi Iye akutanthauza chiyani ponena kuti, ‘Mwa kanthawi kochepa, simudzandionanso,’ ndi ‘ndipo patatha nthawi pangʼono mudzandionanso,’ ndiponso ‘chifukwa ndikupita kwa Atate?’ ” 18 Iwo anapitiriza kufunsana kuti, “Kodi akutanthauza chiyani, ‘kanthawi kochepa?’ Ife sitikumvetsetsa chimene Iye akuyankhula.”

19 Yesu anadziwa kuti ankafuna kuti amufunse za zimenezi, choncho anawafunsa kuti, “Kodi mukufunsana wina ndi mnzake chimene Ine ndimatanthauza pamene ndinati, ‘Mwa kanthawi kochepa simudzandionanso,’ ndi ‘patatha nthawi pangʼono mudzandionanso?’ 20 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti inu mudzalira ndi kubuma pomwe dziko lapansi lidzakhale likukondwera. Inu mudzamva chisoni, koma chisoni chanu chidzasandulika chimwemwe. 21 Mayi akamabereka mwana amamva ululu chifukwa nthawi yake yafika; koma mwana wake akabadwa amayiwala ululu wake chifukwa cha chimwemwe chake chakuti mwana wabadwa mʼdziko lapansi. 22 Chimodzimodzinso ndi inu. Tsopano ino ndi nthawi yanu yomva chisoni, koma Ine ndidzakuonaninso ndipo inu mudzasangalala, ndipo palibe amene adzachotsa chimwemwe chanu. 23 Tsiku limenelo inu simudzandipemphanso kalikonse. Ine ndikukuwuzani zoona kuti Atate anga adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa. 24 Mpaka tsopano simunapemphe kalikonse mʼdzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, ndipo chimwemwe chanu chidzakhala chathunthu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.