Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 66:8-20

Tamandani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthu,
    mulole kuti mawu a matamando ake amveke;
Iye watchinjiriza miyoyo yathu
    ndi kusunga mapazi athu kuti angaterereke.
10 Pakuti Inu Mulungu munatiyesa;
    munatiyenga ngati siliva.
11 Inu mwatilowetsa mʼndende
    ndi kutisenzetsa zolemera pa misana yathu.
12 Inu munalola kuti anthu akwere pa mitu yathu;
    ife tinadutsa mʼmoto ndi mʼmadzi,
    koma Inu munatibweretsa ku malo a zinthu zochuluka.

13 Ine ndidzabwera ku Nyumba yanu ndi nsembe zopsereza
    ndi kukwaniritsa malumbiro anga.
14 Malumbiro amene milomo yanga inalonjeza
    ndi pakamwa panga panayankhula pamene ndinali pa mavuto.
15 Ndidzapereka nsembe nyama zonenepa kwa Inu
    ndi chopereka cha nkhosa zazimuna;
    ndidzapereka ngʼombe zamphongo ndi mbuzi.
            Sela

16 Bwerani ndipo mudzamve inu nonse amene mumaopa Mulungu.
    Ndidzakuwuzani zimene Iyeyo wandichitira.
17 Ndinafuwula kwa Iye ndi pakamwa panga,
    matamando ake anali pa lilime panga.
18 Ndikanasekerera tchimo mu mtima mwanga
    Ambuye sakanamvera;
19 koma ndithu Mulungu wamvetsera
    ndipo watchera khutu ku mawu a kupempha kwanga.
20 Matamando akhale kwa Mulungu
    amene sanakane pemphero langa
    kapena kuletsa chikondi chake pa ine!

Genesis 8:13-19

13 Pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba wa chaka chimene Nowa anakwanitsa zaka 601, madzi anawuma pa dziko lapansi. Ndipo Nowa anachotsa denga la chombo ndipo anaona kuti kunja kwawuma. 14 Pokwana tsiku la 27 la mwezi wachiwiri dziko lapansi linawumiratu.

15 Tsono Mulungu anawuza Nowa kuti, 16 “Iwe, mkazi wako, ana ako pamodzi ndi akazi awo tulukani mʼchombomo. 17 Tulutsa zamoyo zonse zili ndi iwe, mbalame, nyama ndi zokwawa zonse kuti ziswane ndi kuchulukana pa dziko lapansi.”

18 Nowa anatuluka pamodzi ndi ana ake aamuna, mkazi wake ndi akazi a ana ake. 19 Nyama zonse, zokwawa zonse, mbalame zonse, chilichonse choyenda pa dziko lapansi, zinatuluka mʼchombo motsogozana monga mwa mitundu yawo.

Yohane 14:27-29

27 Ine ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Ine sindikukupatsani monga dziko lapansi limaperekera. Mtima wanu usavutike ndipo musachite mantha.

28 “Inu munamva Ine ndikunena kuti, ‘Ine ndikupita ndipo ndidzabweranso kwa inu.’ Mukanandikonda, mukanasangalala kuti Ine ndikupita kwa Atate, pakuti Atate ndi wamkulu kuposa Ine. 29 Ine ndakuwuzani tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika mudzakhulupirire.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.