Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 31:1-5

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

31 Mwa Inu Yehova, ine ndimathawiramo;
    musalole nʼkomwe kuti ndichititsidwe manyazi;
    mundipulumutse chifukwa cha chilungamo chanu.
Tcherani khutu lanu kwa ine,
    bwerani msanga kudzandilanditsa;
mukhale thanthwe langa lothawirapo,
    linga lolimba kundipulumutsa ine.
Popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa,
    chifukwa cha dzina lanu tsogolereni ndi kundiwongolera.
Ndimasuleni mu msampha umene anditchera
    pakuti ndinu pothawirapo panga.
Mʼmanja mwanu ndipereka mzimu wanga;
    womboleni Yehova Mulungu wachoonadi.

Masalimo 31:15-16

15 Masiku anga ali mʼmanja mwanu;
    ndipulumutseni kwa adani anga
    ndi kwa iwo amene akundithamangitsa.
16 Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu;
    pulumutseni mwa chikondi chanu chosatha.

Eksodo 3:1-12

Kuyitanidwa kwa Mose pa Chitsamba Choyaka Moto

Tsono Mose amaweta ziweto za mpongozi wake Yetero, wansembe uja wa ku Midiyani. Tsiku lina iye anazitsogolera kupita ku chipululu ndipo anafika ku phiri la Mulungu lotchedwa Horebu. Kumeneko mngelo wa Yehova anaonekera kwa iye mʼmalawi amoto mʼchitsamba. Mose anaona kuti ngakhale chitsambacho chimayaka koma sichimanyeka. Tsono Mose anati mu mtima mwake, “Ine ndipita komweko ndikaone zodabwitsazi, chitsamba sichikunyeka chifukwa chiyani?”

Yehova ataona kuti Mose anapatuka kuti adzaonetsetse, Mulungu anamuyitana Mose kuchokera mʼchitsambamo nati, “Mose! Mose!”

Ndipo anayankha, “Wawa.”

Mulungu anati, “Usayandikire kuno. Vula nsapato zako, pakuti malo amene wayimapo ndi opatulika.” Mulungu anati, “Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo.” Atamva zimenezi, Mose anaphimba nkhope yake chifukwa anaopa kuona Mulungu.

Yehova anati, “Ine ndaona ndithu mazunzo a anthu anga amene ali ku Igupto. Ndamva kulira kwawo chifukwa cha anthu amene akuwapsinja, ndipo ndakhudzidwa ndi masautso awo. Choncho ndabwera kuti ndiwapulumutse mʼdzanja la Aigupto, kuwatulutsa mʼdzikolo ndi kukawalowetsa mʼdziko labwino ndi lalikulu, dziko loyenda mkaka ndi uchi, kwawo kwa Akanaani, Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Ine ndamva ndithu kulira kwa Aisraeli, ndipo ndaona mmene Aigupto akuwazunzira. 10 Kotero tsopano, pita. Ine ndikukutuma kwa Farao kuti ukatulutse anthu anga, Aisraeli mʼdziko la Igupto.”

11 Koma Mose anafunsa Mulungu, “Ine ndine yani kuti ndipite kwa Farao ndi kukatulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto?”

12 Ndipo Mulungu anati, “Ine ndidzakhala nawe, ndipo ichi chidzakhala chizindikiro kwa iwe kuti ndine amene ndakutuma; Ukadzatulutsa anthu anga mʼdziko la Igupto, udzapembedza Mulungu pa phiri lino.”

Machitidwe a Atumwi 7:1-16

Mawu a Stefano

Kenaka mkulu wa ansembe anafunsa Stefano kuti, “Kodi zimene akukunenerazi ndi zoona?”

Stefano anayankha kuti, “Abale ndi makolo, tamverani! Mulungu waulemerero anaoneka kwa kholo lathu Abrahamu pamene ankakhala ku Mesopotamiya, asanakakhale ku Harani. Mulungu anati, ‘Tuluka mʼdziko lako, siya abale ako, ndipo pita ku dziko limene ndidzakusonyeza.’

“Ndipo iye anatulukadi mʼdziko la Akaldeya ndi kukakhala ku Harani. Atamwalira abambo ake, Mulungu anamuchotsa kumeneko ndi kumubweretsa mʼdziko lino limene inu mukukhalamo tsopano. Mulungu sanamupatse cholowa kuno, ngakhale kadera kakangʼono kadziko. Koma Mulungu anamulonjeza kuti adzapereka dziko lino kwa iye ndi kwa zidzukulu zake, ngakhale kuti pa nthawi imeneyi analibe mwana. Mulungu anayankhula motere kwa iye: ‘Zidzukulu zako zidzakhala alendo mʼdziko lachilendo, ndipo zidzakhala akapolo ndi kuzunzidwa zaka 400.’ Mulungu anati, ‘Ine ndidzalanga dziko limene zidzukulu zako zidzagwireko ukapolo, ndipo pambuyo pake akadzatuluka mʼdzikolo adzandipembedza Ine pamalo pano.’ Kenaka Mulungu anachita pangano la mdulidwe ndi Abrahamu. Ndipo Abrahamu, anabereka Isake, namudula ali ndi masiku asanu ndi atatu. Ndipo Isake anabereka Yakobo, Yakobo anabereka makolo khumi ndi awiri aja.

“Makolo athu anachita nsanje ndi Yosefe ndipo anamugulitsa kuti akakhale kapolo ku Igupto. Koma Mulungu anali naye 10 ndipo anamupulumutsa iye kumasautso ake onse. Mulungu anamupatsa Yosefe nzeru ndi chisomo pamaso pa Farao mfumu ya ku Igupto, kotero mfumuyo inamuyika iye kukhala nduna yayikulu ya dziko la Igupto ndiponso nyumba yake yonse yaufumu.

11 “Kenaka munalowa njala mʼdziko la Kanaani, kotero kuti anthu anavutika kwambiri, ndipo makolo athu sanathe kupeza chakudya. 12 Pamene Yakobo anamva kuti ku Igupto kunali tirigu, iye anatuma makolo athu ulendo woyamba. 13 Pa ulendo wawo wachiwiri, Yosefe anadziwulula kwa abale akewo ndipo Farao anadziwa za banja la Yosefe. 14 Izi zinachitika, Yosefe anayitanitsa abambo ake Yakobo ndi banja lonse, onse pamodzi analipo 75. 15 Motero Yakobo anapita ku Igupto, kumene iye ndiponso makolo athu anamwalira. 16 Mitembo yawo anayinyamula ndi kupita nayo ku Sekemu kumene inayikidwa mʼmanda amene Abrahamu anagula kochokera kwa ana a Hamori ku Sekemuko.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.