Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kuyanjana kwa Okhulupirira
42 Iwo ankasonkhana pamodzi kuphunzitsidwa ndi atumwi, pachiyanjano, pachakudya ndi popemphera. 43 Aliyense ankachita mantha chifukwa cha zodabwitsa ndi zizindikiro zambiri zimene atumwi ankachita. 44 Okhulupirira onse anali pamodzi ndipo aliyense ankapereka zinthu zake kuti zikhale za onse. 45 Ankagulitsa minda yawo ndi katundu wawo, ndi kugawira kwa aliyense molingana ndi zosowa zake. 46 Tsiku ndi tsiku ankasonkhana pamodzi pa bwalo la pa Nyumba ya Mulungu. Ankadya pamodzi mʼnyumba zawo mwasangala ndi mtima woona. 47 Ankayamika Mulungu ndipo anthu onse ankawakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankawonjezera ena pa chiwerengero cha olandira chipulumutso.
Salimo la Davide.
23 Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
2 Amandigoneka pa msipu wobiriwira,
amanditsogolera ku madzi akumwa abwino,
3 amatsitsimutsa moyo wanga.
Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo
chifukwa cha dzina lake.
4 Ngakhale ndiyende
mʼchigwa cha mdima wakuda bii,
sindidzaopa choyipa,
pakuti Inu muli ndi ine;
chibonga chanu ndi ndodo yanu
zimanditonthoza.
5 Mumandikonzera chakudya
adani anga akuona.
Mumadzoza mutu wanga ndi mafuta;
chikho changa chimasefukira.
6 Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata
masiku onse a moyo wanga,
ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova
kwamuyaya.
19 Pakuti ndi chinthu chokoma ngati munthu apirira mu zowawa zimene sizinamuyenera chifukwa chodziwa kuti Mulungu alipo. 20 Kodi pali choti akuyamikireni ngati mupirira pomenyedwa chifukwa choti mwalakwa? Koma ngati mumva zowawa chifukwa chochita zabwino ndi kupirira, mwachita choyamikika pamaso pa Mulungu. 21 Munayitanidwa kudzachita zimenezi, chifukwa Khristu anamva zowawa chifukwa cha inu, anakusiyirani chitsanzo, kuti inu mutsatire mʼmapazi ake.
22 “Iye sanachite tchimo
kapena kunena bodza.”
23 Pamene anthu ankamuchita chipongwe, Iye sanabwezere chipongwe, pamene Iye ankamva zowawa, sanaopseze. Mʼmalo mwake, anadzipereka kwa Mulungu amene amaweruza molungama. 24 Iye mwini anasenza machimo athu mʼthupi lake pa mtanda, kuti ife tife kutchimo ndi kukhala ndi moyo potsata chilungamo, ndipo ndi mabala ake munachiritsidwa. 25 Pakuti munali monga nkhosa zosochera, koma tsopano mwabwerera kwa mʼbusa ndi woyangʼanira miyoyo yanu.
Mʼbusa Wabwino ndi Nkhosa Zake
10 “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani inu Afarisi, kuti munthu amene salowera pa khomo mʼkhola la nkhosa, koma amalowera pena pake ndi wakuba ndi wachifwamba. 2 Munthu amene amalowera pa khomo ndi mʼbusa wankhosazo. 3 Mlonda amamutsekulira khomo, ndipo nkhosa zimamvera mawu ake. Iye amaziyitana mayina nkhosa zakezo, nazitulutsa. 4 Akazitulutsa nkhosa zake zonse, iye amazitsogolera, ndipo nkhosa zakezo zimamutsata chifukwa zimadziwa mawu ake. 5 Koma nkhosazo sizidzatsatira mlendo. Izo zidzamuthawa chifukwa sizizindikira mawu a mlendo.” 6 Yesu ananena mawu ophiphiritsawa, koma Afarisi sanazindikire zimene ankawawuza.
7 Choncho Yesu anatinso, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Ine ndine khomo la nkhosa. 8 Onse amene anadza ndisanabwere Ine ndi akuba ndi achifwamba, ndipo nkhosa sizinawamvere. 9 Ine ndine khomo, aliyense amene alowa kudzera mwa Ine adzapulumuka. Iye adzalowa ndi kutuluka ndi kupeza msipu. 10 Mbala sibwera chabe koma kuti idzabe, kupha ndi kuwononga. Ine ndabwera kuti iwo akhale ndi moyo, ndi kukhala nawo wochuluka.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.