Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Davide.
23 Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
2 Amandigoneka pa msipu wobiriwira,
amanditsogolera ku madzi akumwa abwino,
3 amatsitsimutsa moyo wanga.
Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo
chifukwa cha dzina lake.
4 Ngakhale ndiyende
mʼchigwa cha mdima wakuda bii,
sindidzaopa choyipa,
pakuti Inu muli ndi ine;
chibonga chanu ndi ndodo yanu
zimanditonthoza.
5 Mumandikonzera chakudya
adani anga akuona.
Mumadzoza mutu wanga ndi mafuta;
chikho changa chimasefukira.
6 Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata
masiku onse a moyo wanga,
ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova
kwamuyaya.
Abusa a Israeli
34 Yehova anandiyankhula kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, yankhula mawu oyimba mlandu abusa a Israeli. Lengeza ndipo uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Tsoka kwa abusa a Israeli amene mumangodzisamala nokha! Kodi abusa sayenera kusamalira nkhosa? 3 Mumadya chambiko, mumadziveka zovala zaubweya, ndi kupha nyama zonenepa, koma simusamalira nkhosazo. 4 Simunalimbitse nkhosa zofowoka, kapena kuchiritsa zodwala, kapena kumanga mabala a nkhosa zopweteka. Simunabweze zosochera kapena kufunafuna zotayika. Munaziweta mozunza ndi mwankhanza. 5 Kotero zinabalalika chifukwa zinalibe mʼbusa, ndipo pamene zinabalalika zinakhala chakudya cha zirombo zonse zakuthengo. 6 Nkhosa zanga zinayendayenda mʼmapiri onse ndi mʼzitunda zonse zazitali. Zinabalalika pa dziko lonse lapansi, ndipo palibe amene anazilondola kapena kuzifunafuna.
7 “ ‘Choncho Inu abusa, tamvani zimene Ine Yehova ndikukuwuzani. 8 Pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Wamphamvuzonse, ndithu, nkhosa zanga zinajiwa ndi zirombo zakuthengo, zinasanduka chakudya cha zirombo chifukwa panalibe abusa. Abusa anga sanafunefune nkhosa zanga. Iwo ankangosamala za iwo okha mʼmalo mosamala nkhosa zanga. 9 Chifukwa chake, inu abusa, tamvani zimene Ine Yehova ndikukuwuzani. 10 Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndayipidwa nanu, inu abusa. Ndidzakulandani nkhosa zanga ndipo simudzazidyetsanso. Ndidzakuchotsani pa ntchito ya ubusa kuti musamangodzidyetsa nokha. Ndidzalanditsa nkhosa zanga kukamwa kwanu ndipo simudzazidyanso.
11 “ ‘Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti, mwini wakene ndidzazifunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalira. 12 Monga mʼbusa amanka nafunafuna nkhosa zake pamene zina zabalalikira kutali, moteronso Ine ndidzafunafuna nkhosa zanga. Ndidzazipulumutsa kuchoka kumalo onse kumene zinabalalikira pa nthawi yankhungu ndi mdima. 13 Ndidzazitulutsa pakati pa mitundu ya anthu ndi kuzisonkhanitsa kuchokera ku mayiko ena, ndipo ndidzazibwezera ku dziko lawo. Ndidzaziwetera ku mapiri a Israeli, mʼmbali mwa mitsinje ndi kumalo kumene kumakhala anthu. 14 Ndidzaziwetera kumalo a msipu wabwino. Mapiri okwera a Israeli adzakhala malo azidyetserako. Kumeneko zidzapumula ku abusa abwino a msipu ndipo zizidzadyadi msipu wonenepetsa pa mapiri a Israeli. 15 Ine mwini wake ndidzaziweta nkhosa zanga ndi kuzilola kuti zipumule. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 16 Ndidzafunafuna zotayika ndi kubweza zosochera. Ndidzamanga mabala a zopweteka ndi kulimbikitsa zofowoka. Koma zonenepa ndi zamphamvu ndidzaziwononga. Ndidzaweta nkhosazo mwachilungamo.
Fanizo la Nkhosa Yotayika
15 Tsopano amisonkho ndi “ochimwa” ankasonkhana kudzamvera mawu ake. 2 Koma Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo amangʼungʼudza nati, “Munthu uyu amalandira ochimwa ndi kudya nawo.”
3 Ndipo Yesu anawawuza fanizo ili: 4 “Tiyerekeze kuti mmodzi mwa inu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi yatayika, kodi iye sangasiye 99 zija kutchire ndi kupita kukafuna yotayikayo mpaka atayipeza? 5 Ndipo iye akayipeza, amayinyamula pa phewa lake mwachimwemwe 6 ndi kupita kwawo. Kenaka amayitana anzake ndi anansi pamodzi, ndi kuti, ‘Kondwerani nane; ine ndayipeza nkhosa yanga yotayika ija.’ 7 Ine ndikukuwuzani kuti momwemonso kudzakhala chikondwerero chachikulu kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima kusiyana ndi anthu olungama 99 amene ali otembenuka mtima kale.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.