Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 116:1-4

116 Ndimakonda Yehova pakuti Iyeyo amamva mawu anga;
    Iye amamva kulira kwanga kopempha chifundo.
Pakuti ananditchera khutu,
    ndidzayitana Iye masiku onse a moyo wanga.

Zingwe za imfa zinandizinga,
    zoopsa za ku dziko la anthu akufa zinandigwera;
    ndinapeza mavuto ndi chisoni.
Pamenepo ndinayitana dzina la Yehova:
    “Inu Yehova, pulumutseni!”

Masalimo 116:12-19

12 Ndingamubwezere chiyani Yehova,
    chifukwa cha zokoma zake zonse zimene wandichitira?
13 Ndidzakweza chikho cha chipulumutso
    ndipo ndidzayitana dzina la Yehova.
14 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova
    pamaso pa anthu ake onse.

15 Imfa ya anthu oyera mtima
    ndi yamtengowapatali pamaso pa Yehova.
16 Inu Yehova, zoonadi ndine mtumiki wanu:
    ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu;
    Inu mwamasula maunyolo anga.

17 Ndidzapereka nsembe yachiyamiko kwa Inu
    ndipo ndidzayitanira pa dzina la Yehova.
18 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova
    pamaso pa anthu ake onse,
19 mʼmabwalo a nyumba ya Yehova,
    mʼkati mwako iwe Yerusalemu.

Tamandani Yehova.

Yesaya 25:6-9

Pa phiri ili Yehova Wamphamvuzonse adzakonzera
    anthu a mitundu yonse madyerero a zakudya zokoma ndi vinyo wabwino.
Phwando la nyama yonona
    ndi vinyo wabwino kwambiri.
Iye adzachotsa kulira
    kumene kwaphimba anthu ngati nsalu.
Adzachotsa chinsalu chimene chakuta mitundu yonse ya anthu.
    Yehova adzathetsa imfa mpaka muyaya,
Ambuye Yehova adzapukuta misozi mʼmaso
    mwa munthu aliyense;
adzachotsa manyazi a anthu ake
    pa dziko lonse lapansi,
            Yehova wayankhula.

Tsiku limenelo iwo adzati,

“Ndithudi, uyu ndiye Mulungu wathu;
    ife tinamudalira ndipo anatipulumutsa.
Uyu ndiye Yehova, ife tinamudalira;
    tiyeni tikondwe ndi kusangalala chifukwa watipulumutsa.”

Luka 14:12-14

12 Kenaka Yesu anati kwa mwini malo uja, “Ukakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usamayitane abwenzi ako, abale ako, anthu afuko lako kapena anzako achuma; ngati iwe utero, iwo adzakuyitananso, choncho udzalandiriratu mphotho yako. 13 Koma ukakonza phwando, itana anthu osauka, ofa ziwalo, olumala ndi osaona. 14 Pamenepo udzakhala wodala, chifukwa iwo sangakubwezere kanthu, koma Mulungu ndiye adzakubwezera pa chiukitso cha olungama.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.