Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
114 Pamene Israeli anatuluka mu Igupto,
nyumba ya Yakobo kuchoka ku mtundu wa anthu a chiyankhulo chachilendo,
2 Yuda anasanduka malo opatulika a Mulungu,
Israeli anasanduka ufumu wake.
3 Nyanja inaona ndi kuthawa,
mtsinje wa Yorodani unabwerera mʼmbuyo;
4 mapiri analumphalumpha ngati nkhosa zazimuna,
timapiri ngati ana ankhosa.
5 Nʼchifukwa chiyani iwe unathawa?
iwe mtsinje wa Yorodani unabwereranji mʼmbuyo?
6 inu mapiri, munalumphalumphiranji ngati nkhosa zazimuna,
inu timapiri, ngati ana ankhosa?
7 Njenjemera pamaso pa Ambuye iwe dziko lapansi,
pamaso pa Mulungu wa Yakobo,
8 amene anasandutsa thanthwe kukhala chitsime,
thanthwe lolimba kukhala akasupe a madzi.
Pemphero la Yona
2 Yona ali mʼmimba mwa chinsomba chija anapemphera kwa Yehova Mulungu wake. 2 Iye anati:
“Pamene ndinali mʼmavuto anga ndinayitana Yehova,
ndipo Iye anandiyankha.
Ndili ku dziko la anthu akufa ndinapempha thandizo,
ndipo Inu munamva kulira kwanga.
3 Munandiponya mʼnyanja yozama,
mʼkati mwenimweni mwa nyanja,
ndipo madzi oyenda anandizungulira;
mafunde anu onse ndi mkokomo wake
zinandimiza.
4 Ndinati, ‘Ine ndachotsedwa
pamaso panu;
komabe ndidzayangʼananso
ku Nyumba yanu yopatulika.’
5 Madzi wondimiza anandichititsa mantha,
nyanja yozama inandizungulira;
udzu wa mʼmadzi zinakuta mutu wanga.
6 Ndinatsikira kunsi ndithu, mʼtsinde mwa mapiri;
mipiringidzo ya dziko inanditsekereza kosatha.
Koma Inu munatulutsa moyo wanga mʼmandamo,
Inu Yehova Mulungu wanga.
7 “Pamene moyo wanga umachoka mwa ine,
ine ndinakumbukira Inu Yehova,
ndipo pemphero langa linafika kwa inu,
ku Nyumba yanu yopatulika.
8 “Iwo amene amagwiritsitsa mafano achabechabe
amataya chisomo chawo.
9 Koma ine ndidzapereka kwa Inu nsembe
ndikuyimba nyimbo yamayamiko.
Chimene ndinalonjeza ndidzachikwaniritsa.
Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.”
10 Ndipo Yehova analamula chinsomba chija, ndipo chinakamusanza Yonayo mʼmbali mwa nyanja.
Chizindikiro cha Yona
38 Pamenepo ena mwa Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo anati kwa Iye, “Aphunzitsi, tikufuna tione chizindikiro chodabwitsa kuchokera kwa Inu.”
39 Iye anayankha kuti, “Mʼbado woyipa ndi wachigololo ufunsa za chizindikiro chodabwitsa! Koma ndi chimodzi chomwe sichidzapatsidwa kwa inu kupatula chizindikiro cha mneneri Yona. 40 Pakuti monga Yona anali mʼmimba mwa nsomba yayikulu masiku atatu, usana ndi usiku, momwemonso Mwana wa Munthu adzakhala masiku atatu, usana ndi usiku, mʼkati mwa nthaka. 41 Anthu a ku Ninive adzayimirira pachiweruzo ndi mʼbado uwu ndi kuwutsutsa pakuti iwo analapa Yona atalalikira ndipo tsopano wamkulu kuposa Yona ali pano. 42 Mfumu yayikazi yakummwera idzayimirira pa tsiku lachiweruzo ndi mʼbado uwu ndipo idzawutsutsa pakuti inachokera kumathero a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomoni, ndipo pano pali woposa Solomoni.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.