Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 114

114 Pamene Israeli anatuluka mu Igupto,
    nyumba ya Yakobo kuchoka ku mtundu wa anthu a chiyankhulo chachilendo,
Yuda anasanduka malo opatulika a Mulungu,
    Israeli anasanduka ufumu wake.

Nyanja inaona ndi kuthawa,
    mtsinje wa Yorodani unabwerera mʼmbuyo;
mapiri analumphalumpha ngati nkhosa zazimuna,
    timapiri ngati ana ankhosa.

Nʼchifukwa chiyani iwe unathawa?
    iwe mtsinje wa Yorodani unabwereranji mʼmbuyo?
inu mapiri, munalumphalumphiranji ngati nkhosa zazimuna,
    inu timapiri, ngati ana ankhosa?

Njenjemera pamaso pa Ambuye iwe dziko lapansi,
    pamaso pa Mulungu wa Yakobo,
amene anasandutsa thanthwe kukhala chitsime,
    thanthwe lolimba kukhala akasupe a madzi.

Oweruza 6:36-40

36 Gideoni anati kwa Mulungu, “Ngati mudzapulumutsa Israeli ndi dzanja langa monga mwalonjezeramu, 37 onani, ine ndiyala ubweya wankhosa pa malo opunthira tirigu. Ngati mame adzagwera pa ubweya wankhosa pokhapa, pa nthaka ponse pakhala powuma, ndiye ndidziwa kuti mudzapulumutsadi Israeli ndi dzanja langa monga mwanenera.” 38 Ndipo zimenezi zinachitikadi. Gideoni atadzuka mʼmamawa ndi kuwufinya ubweya uja, anafinya madzi odzaza mtsuko.

39 Kenaka Gideoni anati kwa Mulungu, “Musandikwiyire. Mundilole ndiyankhule kamodzi kokhaka. Ndiyeseko kamodzi kokha ndi ubweyawu kuti pa ubweya pokhapa pakhale powuma koma pa nthaka ponse pakhale ponyowa ndi mame.” 40 Ndipo Mulungu anachita zomwezo usiku umenewo. Pa ubweya pokha panali powuma, koma pa nthaka ponse panagwa mame.

1 Akorinto 15:12-20

Kuuka kwa Oyera Mtima

12 Koma ngati timalalikira kuti Khristu anaukitsidwa kwa akufa, zikutheka bwanji kuti ena mwa inu azinena kuti kulibe kuuka kwa akufa? 13 Ngati kulibe kuuka kwa akufa, ndiye kuti ngakhale Khristu sanaukenso. 14 Ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe, ndiye kuti kulalikira kwathu nʼkopanda ntchito, ndipo chikhulupiriro chanu nʼchopandanso ntchito. 15 Kuwonjezera pamenepa, ndiye kuti ndife mboni zabodza pa za Mulungu, pakuti tikuchita umboni kuti Mulungu anaukitsa Khristu kwa akufa. Ngati nʼzoona kuti akufa saukitsidwa, ndiye kuti Mulungu sanaukitsenso Khristu. 16 Pakuti ngati akufa saukitsidwa, ndiye kuti nayenso Khristu sanaukitsidwe. 17 Ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe, chikhulupiriro chanu nʼchopanda ntchito; mukanali mu machimo anu. 18 Ndiye kuti nawonso amene agona tulo mwa Ambuye ndi otayika. 19 Ngati kukanakhala kuti tili ndi chiyembekezo mwa Khristu mʼmoyo uno wokha, tikanakhala omvetsa chisoni kuposa anthu ena onse.

20 Koma nʼzoonadi kuti Khristu anaukitsidwa kwa kufa, chipatso choyamba cha onse ogona tulo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.