Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 16

Mikitamu ya Davide.

16 Ndisungeni Inu Mulungu,
    pakuti ine ndimathawira kwa Inu.

Ndinati kwa Yehova, “Inu ndinu Ambuye anga;
    popanda Inu, ine ndilibe chinthu chinanso chabwino.”
Kunena za oyera mtima amene ali pa dziko,
    amenewa ndi olemekezeka, amene ndimakondwera nawo.
Anthu amene amathamangira kwa milungu ina
    mavuto awo adzachulukadi.
Ine sindidzathira nawo nsembe zawo zamagazi
    kapena kutchula mayina awo ndi pakamwa panga.

Yehova, Inu mwandipatsa cholowa changa ndi chikho changa;
    mwateteza kolimba gawo langa.
Malire a malo anga akhala pabwino;
    ndithudi, ine ndili cholowa chokondweretsa kwambiri.

Ine ndidzatamanda Yehova amene amandipatsa uphungu;
    ngakhale usiku mtima wanga umandilangiza.
Ndayika Yehova patsogolo panga nthawi zonse.
    Popeza Iyeyo ali kudzanja langa lamanja,
    sindidzagwedezeka.

Choncho mtima wanga ndi wosangalala ndipo pakamwa panga pakukondwera;
    thupi langanso lidzakhala pabwino,
10 chifukwa Inu simudzandisiya ku manda,
    simudzalola kuti woyera wanu avunde.
11 Inu mwandidziwitsa njira ya moyo;
    mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu,
    ndidzasangalala mpaka muyaya pa dzanja lanu lamanja.

Nyimbo ya Solomoni 2:8-15

Tamverani bwenzi langa!
    Taonani! Uyu akubwera apayu,
akulumphalumpha pa mapiri,
    akujowajowa pa zitunda.
Bwenzi langa ali ngati gwape kapena mwana wa mbawala.
    Taonani! Uyo wayima kuseri kwa khoma lathulo,
akusuzumira mʼmazenera,
    akuyangʼana pa mpata wa zenera.
10 Bwenzi langa anayankha ndipo anati kwa ine,
    “Dzuka bwenzi langa,
    wokongola wanga, ndipo tiye tizipita.
11 Ona, nyengo yozizira yatha;
    mvula yatha ndipo yapitiratu.
12 Maluwa ayamba kuoneka pa dziko lapansi;
    nthawi yoyimba yafika,
kulira kwa njiwa kukumveka
    mʼdziko lathu.
13 Mtengo wankhuyu ukubereka zipatso zake zoyambirira;
    mitengo ya mpesa ya maluwa ikutulutsa fungo lake.
Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga
    tiye tizipita.”

Mwamuna

14 Nkhunda yanga yokhala mʼmingʼalu ya thanthwe,
    mʼmalo obisala a mʼmbali mwa phiri,
onetsa nkhope yako,
    nʼtamvako liwu lako;
pakuti liwu lako ndi lokoma,
    ndipo nkhope yako ndi yokongola.
15 Mutigwirire nkhandwe,
    nkhandwe zingʼonozingʼono
zimene zikuwononga minda ya mpesa,
    minda yathu ya mpesa imene yayamba maluwa.

Akolose 4:2-5

Malangizo Ena

Pempherani modzipereka, mukhale atcheru ndiponso oyamika. Ndipo muzitipemphereranso ife kuti Mulungu atitsekulire khomo la uthenga wathu, kuti tilalikire chinsinsi cha Khristu, chimene ndine womangidwa nacho mʼndende. Pempherani kuti ndilalikire momveka bwino, monga ndikuyenera. Mayendedwe anu pakati pa akunja, akhale anzeru ndipo mugwiritse ntchito mpata uliwonse umene muli nawo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.