Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 31:9-16

Mundichitire chifundo Inu Yehova pakuti ndili pa mavuto;
    maso anga akulefuka ndi chisoni,
    mʼmoyo mwanga ndi mʼthupi mwanga momwe mukupweteka.
10 Moyo wanga ukunyeka chifukwa cha kuwawidwa mtima
    ndi zaka zanga chifukwa cha kubuwula;
mphamvu zanga zatha chifuwa cha masautso,
    ndipo mafupa anga akulefuka.
11 Chifukwa cha adani anga onse,
    ndine wonyozeka kwambiri ndi anansi anga;
ndine chochititsa manyazi kwa abwenzi anga.
    Iwo amene amandiona mu msewu amandithawa.
12 Ine ndinayiwalika kwa iwo ngati kuti ndinamwalira;
    ndakhala ngati mʼphika wosweka.
13 Pakuti ine ndamva zonena zoyipa za anthu ambiri;
    zoopsa zandizungulira mbali zonse;
iwo akukonza chiwembu kuti alimbane nane,
    kuti atenge moyo wanga.

14 Koma ndikudalira Inu Yehova;
    ndikunena kuti, “Ndinu Mulungu wanga.”
15 Masiku anga ali mʼmanja mwanu;
    ndipulumutseni kwa adani anga
    ndi kwa iwo amene akundithamangitsa.
16 Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu;
    pulumutseni mwa chikondi chanu chosatha.

Yobu 13:13-19

13 “Khalani chete ndipo ndilekeni ndiyankhule;
    tsono zimene zindichitikire zichitike.
14 Chifukwa chiyani ndikuyika moyo wanga pa chiswe
    ndi kutengera mʼmanja moyo wangawu?
15 Ngakhale Iye andiphe, komabe ndidzamukhulupirira;
    ndithu, ndidzafotokoza mlandu wanga pamaso pake.
16 Zoonadi, ichi ndiye chidzakhala chipulumutso changa
    pakuti palibe munthu wosapembedza amene angafike pamaso pake!
17 Mvetserani mosamala mawu anga;
    makutu anu amve zimene ndikunena.
18 Pakuti tsopano ndawukonzekera mlandu wanga,
    ndikudziwa ndipo adzandipeza wolungama.
19 Kodi alipo wina amene angatsutsane nane?
    ngati zili choncho, ndidzakhala chete ndi kufa.

Afilipi 1:21-30

21 Pakuti kwa ine kukhala moyo ndi Khristu ndipo kufa ndi phindu. 22 Ngati nditi ndipitirire kukhala ndi moyo mʼthupi ndiye kuti kwa ine ndi kugwira ntchito yopindulitsa. Kodi ndisankhe chiyani? Sindikudziwa. 23 Ndathinidwa ndi zinthu ziwirizi: Ndikulakalaka kunyamuka kuti ndikakhale ndi Khristu, chimene ndi chinthu chabwino kwambiri. 24 Komanso nʼkofunika kwambiri kuti ndikhalebe mʼthupi chifukwa cha inu. 25 Ndili ndi chitsimikizo, ndikudziwa kuti ndidzakhala ndi moyo ndipo ndidzapitirira nanu kuti nonse mupite mʼtsogolo ndi kukhala ndi chimwemwe mu chikhulupiriro 26 kuti pokhala nanunso, kudzitamandira kwanu mwa Khristu Yesu kudzasefukire chifukwa cha ine.

Moyo Woyenerana ndi Uthenga Wabwino

27 Chilichonse chimene chingachitike, chachikulu nʼchakuti mukhale moyo ofanana ndi Uthenga Wabwino wa Khristu. Tsono ngati ndingabwere kudzakuonani kapena kumangomva za inu ndili kutali, ndidzadziwa kuti mwayima mwamphamvu mwa Mzimu mmodzi, kulimbika pamodzi ngati munthu mmodzi chifukwa cha chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino 28 osachita mantha ndi pangʼono pomwe ndi amene akutsutsana nanu. Ichi ndi chizindikiro kwa iwo kuti adzawonongedwa, koma inu mudzapulumutsidwa ndi Mulungu. 29 Pakuti inu mwapatsidwa mwayi osati ongokhulupirira Khristu kokha, koma wakumva zowawa mʼmalo mwa Khristu. 30 Inunso mukudutsa mʼzowawa zomwe zija munaona ndikudutsamo inenso ndipo pano mukumva kuti ndikukumana nazobe.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.