Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 143

Salimo la Davide.

143 Yehova imvani pemphero langa,
    mvetserani kulira kwanga kopempha chifundo;
mwa kukhulupirika kwanu ndi chilungamo chanu
    bwerani kudzandithandiza.
Musazenge mlandu mtumiki wanu,
    pakuti palibe munthu wamoyo amene ndi wolungama pamaso panu.

Mdani akundithamangitsa,
    iye wandipondereza pansi;
wachititsa kuti ndikhale mu mdima
    ngati munthu amene anafa kale.
Choncho mzimu wanga ukufowoka mʼkati mwanga;
    mʼkati mwanga, mtima wanga uli ndi nkhawa.

Ndimakumbukira masiku amakedzana;
    ndimalingalira za ntchito yanu yonse,
    ndimaganizira zimene manja anu anachita.
Ndatambalitsa manja anga kwa Inu;
    moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu monga nthaka yowuma.
            Sela

Yehova ndiyankheni msanga;
    mzimu wanga ukufowoka.
Musandibisire nkhope yanu,
    mwina ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje.
Lolani kuti mmawa ubweretse mawu achikondi chanu chosasinthika,
    pakuti ine ndimadalira Inu.
Mundisonyeze njira yoti ndiyendemo,
    pakuti kwa Inu nditukulira moyo wanga.
Pulumutseni kwa adani anga, Inu Yehova,
    pakuti ndimabisala mwa Inu.
10 Phunzitseni kuchita chifuniro chanu,
    popeza ndinu Mulungu wanga;
Mzimu wanu wabwino unditsogolere
    pa njira yanu yosalala.

11 Sungani moyo wanga Inu Yehova chifukwa cha dzina lanu;
    mwa chilungamo chanu tulutseni mʼmasautso anga.
12 Mwa chikondi chanu chosasinthika khalitsani chete adani anga;
    wonongani adani anga,
    pakuti ndine mtumiki wanu.

Yeremiya 32:1-9

Yeremiya Agula Munda

32 Yehova anayankhula ndi Yeremiya mʼchaka chakhumi cha Zedekiya mfumu ya Yuda, chimene chinalinso chaka cha 18 cha ulamuliro wa Nebukadinezara. Pa nthawi imeneyi nʼkuti ankhondo a mfumu ya ku Babuloni atazinga Yerusalemu, ndipo mneneri Yeremiya ndiye anamutsekera mʼbwalo la alonda mʼnyumba yaufumu ya ku Yuda.

Tsono Zedekiya mfumu ya Yuda nʼkuti itamutsekera mʼmenemo, ndipo inati, “Nʼchifukwa chiyani ukulosera motero? Iwe ukunena kuti, ‘Yehova akuti: Ndidzapereka mzinda uno kwa mfumu ya ku Babuloni, ndipo idzawulanda. Zedekiya mfumu ya Yuda sidzapulumuka mʼmanja mwa Ababuloni, koma idzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babuloni. Adzayankhula naye ndi kuonana naye maso ndi maso. Zedekiya adzatengedwa kupita naye ku Babuloni, kumene adzakhale mpaka nditamukhawulitsa, akutero Yehova. Ngakhale iye adzamenyane ndi Babuloni, koma sadzapambana.’ ”

Yeremiya anati, “Yehova wandiwuza kuti: Taonani, Hanameli mwana wa Salumu, amalume ako akubwera ndipo adzakuwuza kuti, ‘Gula munda wanga wa ku Anatoti, chifukwa iwe ndiwe mʼbale wanga ndipo ndiwe woyenera kuwuwombola.’ ”

Ndipo monga momwe Yehova ananenera, Hanameli, msuweni wanga anabweradi ku bwalo la alonda ndipo anati, “Gula munda wanga wa ku Anatoti mʼdziko la Benjamini. Popeza ndiwe woyenera kuwugula ndi kukhala wako, gula munda umenewu kuti ukhale wako.”

“Ine ndinadziwa kuti amenewa anali mawu a Yehova aja; choncho ndinagula munda wa ku Anatoti kwa Hanameli msuweni wanga, ndipo ndinamupatsa masekeli asiliva 17.

Yeremiya 32:36-41

36 “Anthu ponena za mzindawu akuti udzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babuloni mwa nkhondo, njala ndi mliri, koma Yehova Mulungu wa Israeli akuti, 37 Ine ndidzawasonkhanitsadi anthuwa kuchokera ku mayiko onse kumene ndinawapirikitsira ndili wokwiya ndi waukali kwambiri. Ndidzabwera nawo ku malo ano ndipo ndidzawalola kukhala mwamtendere. 38 Iwo adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo. 39 Ndidzawapatsa mtima umodzi ndi khalidwe limodzi kotero kuti azidzandiopa nthawi zonse ndipo iwo pamodzi ndi zidzukulu zawo zinthu zidzawayendera bwino. 40 Ndidzachita nawo pangano losatha: sindidzaleka kuwachitira zabwino, ndipo ndidzawapatsa mtima woti azidzandiopa, kuti asadzandisiyenso. 41 Ndidzakondwera powachitira zabwino, ndipo ndidzawakhazikitsa ndithu mʼdziko lino ndi mtima wanga wonse ndi moyo wanga wonse.

Mateyu 22:23-33

Ukwati ndi za Kuuka kwa Akufa

23 Tsiku lomwelo Asaduki amene amati kulibe za kuukanso, anabwera kwa Iye ndi funso. 24 Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatiwuza kuti munthu akamwalira wosasiya ana, mʼbale wake akuyenera kukwatira mkazi wamasiyeyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo. 25 Tsopano panali abale asanu ndi awiri pakati pathu. Woyambayo anakwatira ndipo anamwalira, ndipo popeza analibe ana, mʼbale wake analowa chokolo. 26 Izi zinachitikiranso mʼbale wa chiwiri ndi wachitatu mpaka wachisanu ndi chiwiri. 27 Pa mapeto pake mkaziyo anamwaliranso. 28 Tsopano, kodi akadzaukitsidwa adzakhala mkazi wa ndani mwa asanu ndi awiriwa popeza aliyense anamukwatirapo?”

29 Yesu anayankha kuti, “Inu mukulakwitsa chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu ya Mulungu. 30 Anthu akadzaukitsidwa, sadzakwatira kapena kukwatiwa; adzakhala ngati angelo kumwamba. 31 Koma za kuukitsidwa kwa akufa, kodi simunawerenge zimene Mulungu ananena kwa inu kuti, 32 ‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo?’ Iyeyo si Mulungu wa akufa koma wa amoyo.”

33 Magulu a anthu atamva zimenezi, anazizwa ndi chiphunzitso chake.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.