Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Ezekieli 37:1-14

Chigwa cha Mafupa Owuma

37 Dzanja la Yehova linali pa ine, ndipo Mzimu wa Yehova unandinyamula nʼkukandikhazika pakati pa chigwa. Chigwacho chinali chodzaza ndi mafupa. Yehova anandiyendetsa uku ndi uku pakati pa mafupawo. Mafupawo anali ochuluka kwambiri mʼchigwa monsemo ndipo anali owuma kwambiri. Tsono Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi mafupa amenewa angakhalenso ndi moyo?”

Ndinayankha kuti, “Inu Ambuye Yehova, Inuyo nokha ndiye mukudziwa.”

Pamenepo anandiwuza kuti, “Lengeza kwa mafupa amenewa ndi kuwawuza kuti amve mawu a Ine Yehova! Uwawuze kuti zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena kwa mafupa ndi izi: Ndidzawuzira mpweya mwa inu, ndipo mudzakhalanso ndi moyo. Ndidzakupatsani mitsempha ndi mnofu. Ndiponso ndidzakukutani ndi khungu. Pambuyo pake ndidzawuzira mpweya mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

Ndipo ndinanenera monga anandilamulira. Ndipo pamene ndinkanenera, ndinamva gobedegobede, ndipo mafupa aja anayamba kulumikizana, fupa ku fupa linzake. Ine ndinayangʼana, ndipo mitsempha ndi mnofu zinabwera pa mafupawo ndipo khungu linaphimba pamwamba pake, koma munalibe mpweya mwa iwo.

Tsono Yehova anandiwuza kuti, “Nenera kwa mpweya, nenera iwe mwana wa munthu ndi kuwuza mpweya mawu a Ine Ambuye Yehova kuti, ‘Bwera kuno iwe mpweya. Bwera kuchokera ku mbali zonse zinayi ndi kudzawuzira anthu ophedwawa kuti akhalenso ndi moyo.’ 10 Choncho ndinanenera monga anandilamulira ndipo mpweya unalowa mwa iwo; apo anthu akufawo anakhala ndi moyo, nayimirira ndipo linali gulu lalikulu lankhondo.”

11 Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, mafupa awa ndi nyumba yonse ya Israeli. Iwo amanena kuti, ‘Mafupa athu awuma ndipo chiyembekezo chathu chatayika, ife tawonongeka!’ 12 Nʼchifukwa chake nenera ndi kuwawuza kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Inu anthu anga, ndidzafukula manda anu, ndipo ndidzakutulutsanimo ndi kukubwezerani ku dziko la Israeli. 13 Ndipo inu, anthu anga, mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pamene ndidzafukula manda anu ndikukutulutsanimo. 14 Ine ndidzayika Mzimu wanga mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo. Pambuyo pake ndidzakulowetsani mʼdziko lanulanu. Choncho mudzadziwa kuti Ambuye Yehova ndayankhula zimenezi, ndipo ndidzazichitadi. Ndikutero Ine Yehova!’ ”

Masalimo 130

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

130 Ndikulirira kwa Inu Yehova ndili mʼdzenje lozama;
    Ambuye imvani mawu anga.
Makutu anu akhale tcheru kumva
    kupempha chifundo kwanga.

Inu Yehova, mukanamawerengera machimo,
    Inu Yehova, akanayima chilili ndani wopanda mlandu?
Koma kwa Inu kuli chikhululukiro;
    nʼchifukwa chake mumaopedwa.

Ndimayembekezera Yehova, moyo wanga umayembekezera,
    ndipo ndimakhulupirira mawu ake.
Moyo wanga umayembekezera Ambuye,
    kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,
    inde, kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,

Yembekeza Yehova, iwe Israeli,
    pakuti Yehova ali ndi chikondi chosasinthika
    ndipo alinso ndi chipulumutso chochuluka.
Iye mwini adzawombola Israeli
    ku machimo ake onse.

Aroma 8:6-11

Kuyika mtima pa zathupi ndi imfa koma kuyika mtima pa za Mzimu ndi moyo ndi mtendere. Pakuti mtima umene wakhazikika pa zathupi ndi wodana ndi Mulungu. Sunagonjere lamulo la Mulungu ndipo sungathe kutero. Ndipo anthu amene amalamulidwa ndi khalidwe lauchimo sangathe kukondweretsa Mulungu.

Koma inu simulamulidwanso ndi khalidwe lanu lauchimo koma ndi Mzimu ngati Mzimu wa Mulungu akhaladi mwa inu. Koma ngati munthu aliyense alibe Mzimu wa Khristu, iyeyu si wa Khristu. 10 Ndipo ngati Khristu ali mwa inu, thupi lanu ndi lakufa chifukwa cha uchimo, koma mzimu wanu ndi wamoyo chifukwa cha chilungamo. 11 Ndipo ngati Mzimu wa Mulungu amene anaukitsa Yesu kwa akufa akhala mwa inu, Iyeyo amene anaukitsa Khristu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu amene amafa kudzera mwa Mzimu wake amene amakhala mwa inu.

Yohane 11:1-45

Imfa ndi Kuukitsidwa kwa Lazaro

11 Tsopano munthu wina dzina lake Lazaro anadwala. Iye anali wa ku Betaniya, mudzi wa Mariya ndi mchemwali wake Marita. Mariyayo ndi yemwe uja amene anadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake. Lazaro wodwalayo anali mlongo wake. Choncho alongo ake anatumiza mawu kwa Yesu kuti, “Ambuye, uja amene Inu mumamukonda akudwala.”

Atamva izi, Yesu anati, “Kudwalako safa nako. Koma akudwala kuti Mulungu alemekezedwe; ndi kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe chifukwa cha matendawo.” Yesu anakonda Marita, mchemwali wake ndi Lazaro. Koma atamva kuti Lazaro akudwala, Iye anakhalabe kumene anali masiku ena awiri.

Kenaka anati kwa ophunzira ake, “Tiyeni tibwerere ku Yudeya.”

Ophunzira akewo anati, “Rabi, posachedwa pomwepa Ayuda anafuna kukugendani ndi miyala, koma Inu mukupitanso komweko?”

Yesu anayankha kuti, “Kodi sipali maora khumi ndi awiri pa tsiku? Munthu amene amayenda masana sapunthwa, popeza akuona chifukwa cha kuwala kwa dziko lapansi. 10 Koma amene akuyenda usiku amapunthwa, chifukwa kuwalako alibe.”

11 Iye atatha kunena izi, anapitirira kuwawuza iwo kuti, “Bwenzi lathu Lazaro wagona tulo; koma Ine ndikupita kumeneko kukamudzutsa.”

12 Ophunzira ake anayankha kuti, “Ambuye, ngati wagona adzapeza bwino.” 13 Yesu ankayankhula za imfa yake koma ophunzira ake ankaganiza kuti amanena za tulo chabe.

14 Ndipo kenaka anawawuza momveka kuti, “Lazaro wamwalira. 15 Ine ndikukondwera chifukwa cha inu kuti kunalibe kumeneko; koma kuti mukakhulupirire tiyeni tipiteko.”

16 Pamenepo Tomasi, wotchedwa Didimo, anati kwa ophunzira anzake, “Tiyeni nafenso tipite, kuti tikafere naye pamodzi.”

Yesu Atonthoza Alongo a Lazaro

17 Yesu atafika, anapeza kuti Lazaro anali atagona mʼmanda masiku anayi. 18 Mudzi wa Betaniya unali pafupi ndi Yerusalemu pa mtunda wosachepera makilomita atatu, 19 ndipo Ayuda ambiri anabwera kwa Marita ndi Mariya kudzawatonthoza pa imfa ya mʼbale wawo. 20 Pamene Marita anamva kuti Yesu akubwera, anapita kukakumana naye. Koma Mariya anatsala ku nyumba.

21 Marita anati kwa Yesu, “Ambuye, mukanakhala muli kuno, mlongo wanga sakanamwalira. 22 Koma ine ndikudziwa kuti ngakhale tsopano Mulungu adzakupatsani chilichonse chimene mudzamupempha.”

23 Yesu anati kwa iye, “Mlongo wako adzauka.”

24 Marita anayankha kuti, “Ine ndikudziwa kuti adzauka pa kuukanso pa tsiku lomaliza.”

25 Yesu anati kwa iye, “Ine ndine kuuka ndi moyo. Wokhulupirira Ine, angakhale amwalira adzakhala ndi moyo. 26 Aliyense amene ali ndi moyo ndi kukhulupirira Ine sadzamwalira. Kodi iwe ukukhulupirira izi?”

27 Marita anamuwuza Iye kuti, “Inde Ambuye, ine ndikukhulupirira kuti ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu, amene abwera mʼdziko lapansi.”

28 Ndipo iye atanena izi anabwerera ndi kukayitana mchemwali wake Mariya namuyankhula monongʼona pambali, nati, “Aphunzitsi abwera ndipo akukuyitana.” 29 Mariya atamva izi, anayimirira mofulumira napita kwa Iye. 30 Tsopano nʼkuti Yesu asanalowe mʼmudzi, koma anali akanali pa malo pamene Marita anakumana naye. 31 Ayuda amene ankamutonthoza Mariya mʼnyumba, anaona mmene iye anayimira mofulumira ndi kutuluka kunja, iwo anamutsata akuganizira kuti ankapita ku manda kukalirira kumeneko.

32 Mariya anafika pamalo pamene panali Yesu ndipo atamuona, anagwa pa mapazi ake ndipo anati, “Ambuye mukanakhala muli kuno mlongo wanga sakanamwalira.”

33 Yesu ataona iye akulira, ndi Ayuda amene anabwera naye akuliranso, anakhudzidwa kwambiri ndi kuvutika mu mzimu. 34 Iye anafunsa kuti, “Kodi mwamuyika kuti?”

Iwo anayankha kuti, “Ambuye tiyeni mukaone.”

35 Yesu analira.

36 Pamenepo Ayuda anati, “Taonani mmene Iye anamukondera Lazaro!”

37 Koma ena a iwo anati, “Iye amatsekula maso a munthu wosaona, kodi sakanakhoza kuletsa kuti munthu uyu asamwalire?”

Yesu Aukitsa Lazaro

38 Yesu atakhudzidwanso kwambiri anafika ku manda. Manda akewo anali phanga ndipo anatsekapo ndi mwala. 39 Yesu anati, “Chotsani mwala.”

Marita mlongo wa womwalirayo anati, “Koma Ambuye, nthawi ino wayamba kununkha, pakuti wakhala mʼmenemu masiku anayi.”

40 Kenaka Yesu anati, “Kodi Ine sindinakuwuze kuti ngati iwe ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu?”

41 Choncho iwo anachotsa mwalawo. Kenaka Yesu anayangʼana kumwamba ndikuti, “Atate, Ine ndikukuthokozani chifukwa mumandimvera. 42 Ine ndimadziwa kuti Inu mumandimvera nthawi zonse, koma Ine ndanena izi chifukwa cha anthu amene ayima pano, kuti iwo akhulupirire kuti Inu munandituma Ine.”

43 Yesu atanena izi, Iye anayitana ndi mawu ofuwula kuti, “Lazaro, tuluka!” 44 Munthu womwalirayo anatuluka, womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za ku manda, ndi nkhope yake yokulungidwa nsalu.

Yesu anawawuza kuti, “Mʼmasuleni, ndipo muloleni apite.”

Ayuda Apangana za Kupha Yesu

45 Choncho Ayuda ambiri amene anabwera kudzamuchereza Mariya ndi kuona zimene Yesu anachita anamukhulupirira Iye.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.