Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 130

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

130 Ndikulirira kwa Inu Yehova ndili mʼdzenje lozama;
    Ambuye imvani mawu anga.
Makutu anu akhale tcheru kumva
    kupempha chifundo kwanga.

Inu Yehova, mukanamawerengera machimo,
    Inu Yehova, akanayima chilili ndani wopanda mlandu?
Koma kwa Inu kuli chikhululukiro;
    nʼchifukwa chake mumaopedwa.

Ndimayembekezera Yehova, moyo wanga umayembekezera,
    ndipo ndimakhulupirira mawu ake.
Moyo wanga umayembekezera Ambuye,
    kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,
    inde, kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,

Yembekeza Yehova, iwe Israeli,
    pakuti Yehova ali ndi chikondi chosasinthika
    ndipo alinso ndi chipulumutso chochuluka.
Iye mwini adzawombola Israeli
    ku machimo ake onse.

Ezekieli 33:10-16

10 “Iwe mwana wa munthu, akumbutse Aisraeli mawu awo akuti, ‘Ife talemedwa ndi zolakwa zathu ndi machimo athu, ndipo tikuwonda chifukwa cha zimene tachita. Kodi tingakhale ndi moyo bwanji?’ ” 11 Uwawuze kuti, Ine Ambuye Yehova ndikuti: “Pali Ine wamoyo, sindikondwera ndi imfa ya munthu woyipa. Ndimakondwera ndikamaona munthu woyipa akuleka zoyipa zake kuti akhale ndi moyo. Tembenukani! Tembenukani, siyani makhalidwe anu oyipa! Muferanji, Inu Aisraeli?

12 “Tsono iwe mwana wa munthu, awuze anthu a mtundu wako kuti, ‘Ngati munthu wolungama achimwa, ndiye kuti ntchito zake zabwino zija sizidzamupulutsa. Koma wochimwa akaleka ntchito zake zoyipazo, sadzalangidwa konse. Ndithu ngati munthu wolungama ayamba kuchimwa sadzatha kukhala ndi moyo chifukwa cha ntchito zake zabwino zija.’ 13 Ngati ndiwuza munthu wolungama kuti adzafa ndithu, koma iyeyo nʼkumadalira ntchito zake zabwino zimene anachita kale ndi kuyamba kuchimwa, ndiye kuti ntchito zake zabwinozo zidzayiwalika. Iye adzafa chifukwa cha machimo ake. 14 Ndipo ngati ndiwuza munthu woyipa kuti, ‘Udzafa ndithu,’ tsono iye nʼkutembenuka kuleka machimo ake ndi kuyamba kuchita zimene Yehova afuna, 15 monga kubweza chimene anatenga ngati chikole cha ngongole, kubweza chimene anaba, kutsatira malamulo omwe amapereka moyo ndi kuleka kuchita zoyipa, iye adzakhala ndithu ndi moyo; sadzafa. 16 Ndidzakhululuka machimo ake onse anachita. Iye wachita zimene ndi zolungama ndi zoyenera ndipo iye adzakhala ndi moyo ndithu.

Chivumbulutso 11:15-19

Lipenga Lachisanu ndi Chiwiri

15 Mngelo wachisanu ndi chiwiri anawomba lipenga lake, ndipo kumwamba kunamveka mawu ofuwula amene anati,

“Ufumu wa dziko lapansi uli
    mʼmanja mwa Ambuye athu ndi Khristu wake uja,
    ndipo adzalamulira mpaka muyaya.”

16 Ndipo akuluakulu 24 aja okhala pa mipando yawo yaufumu pamaso pa Mulungu, anadzigwetsa chafufumimba napembedza Mulungu 17 Iwo anati,

“Ife tikuyamika Inu Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse,
    amene mulipo ndipo munalipo,
chifukwa mwaonetsa mphamvu yanu yayikulu,
    ndipo mwayamba kulamulira.
18 A mitundu ina anapsa mtima;
    koma yafika nthawi yoonetsa mkwiyo.
Nthawi yakwana yoweruza anthu akufa,
    yopereka mphotho kwa atumiki anu, aneneri,
anthu oyera mtima anu ndi amene amaopa dzina lanu,
    wamngʼono pamodzi ndi wamkulu yemwe.
Yafika nthawi yowononga amene awononga dziko lapansi.”

19 Pamenepo anatsekula Nyumba ya Mulungu kumwamba ndipo mʼkati mwake munaoneka Bokosi la Chipangano. Kenaka kunachita mphenzi, phokoso, mabingu, chivomerezi ndipo kunachita mkuntho wamatalala akuluakulu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.