Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 23

Salimo la Davide.

23 Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
    Amandigoneka pa msipu wobiriwira,
amanditsogolera ku madzi akumwa abwino,
    amatsitsimutsa moyo wanga.
Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo
    chifukwa cha dzina lake.
Ngakhale ndiyende
    mʼchigwa cha mdima wakuda bii,
sindidzaopa choyipa,
    pakuti Inu muli ndi ine;
chibonga chanu ndi ndodo yanu
    zimanditonthoza.

Mumandikonzera chakudya
    adani anga akuona.
Mumadzoza mutu wanga ndi mafuta;
    chikho changa chimasefukira.
Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata
    masiku onse a moyo wanga,
ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova
    kwamuyaya.

1 Samueli 15:22-31

22 Koma Samueli anayankha kuti,

“Kodi Yehova amakondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zina
    kapena kumvera mawu a ake?
Taona, kumvera ndi kwabwino kuposa nsembe,
    ndipo kutchera khutu ndi kwabwino kuposa kupereka mafuta a nkhosa.
23 Pakuti kuwukira kuli ngati tchimo lowombeza,
    ndipo kukhala nkhutukumve kuli ngati tchimo lopembedza mafano.
Chifukwa mwakana mawu a Yehova.
    Iyenso wakukana kuti iweyo ukhale mfumu.”

24 Tsono Sauli anati kwa Samueli, “Ine ndachimwa. Ndaphwanya malamulo a Yehova ndiponso malangizo anu. Ndinkaopa anthu ndipo ndinawamvera. 25 Tsopano ndikukupemphani, khululukireni tchimo langa ndipo mubwerere nane kuti ndikapembedze Yehova.”

26 Koma Samueli anawuza Sauli kuti, “Ine sindibwerera nawe. Inu mwakana mawu a Yehova. Choncho Iyenso wakukanani kuti musakhale mfumu yolamulira Aisraeli.”

27 Samueli akutembenuka kuti azipita, Sauli anagwira mpendero wa mkanjo wake, ndipo unangʼambika. 28 Samueli anati kwa iye, “Yehova wangʼamba ufumu wanu kuchoka kwa inu, ndipo waupereka kwa mnzanu woposa inu. 29 Mulungu wa ulemerero wa Israeli sanama kapena kusintha maganizo ake; pakuti iye si munthu, kuti asinthe maganizo ake.”

30 Sauli anati, “Ine ndachimwa. Komabe, chonde mundilemekeze pamaso pa akuluakulu, anthu anga, ndiponso pamaso pa Israeli. Mubwerere nane kuti ndikapembedze Yehova Mulungu wanu.” 31 Pamenepo Samueli anabwerera ndi Sauli, ndipo Sauli anapembedza Yehova.

Aefeso 5:1-9

Choncho, monga ana okondedwa, tsatirani chitsanzo cha Mulungu. Muzikondana monga Khristu anakonda ife nadzipereka yekha chifukwa cha ife monga chopereka cha fungo lokoma ndi nsembe kwa Mulungu.

Koma pakati panu pasamveke nʼpangʼono pomwe zadama, kapena za mtundu wina uliwonse wa chodetsa, kapena za umbombo, chifukwa izi ndi zosayenera kwa anthu oyera a Mulungu. Musamatukwane, kuyankhula zopusa kapena kunena nthabwala zopanda pake, zomwe ndi zosayenera, koma mʼmalo mwake muziyamika. Dziwani ichi, palibe wadama, wochita zonyansa kapena waumbombo, munthu wotero ali ngati wopembedza mafano, amenewa alibe malo mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu. Musalole wina akunamizeni ndi mawu opanda pake, pakuti chifukwa cha zinthu ngati izi mkwiyo wa Mulungu ukubwera pa amene samvera. Nʼchifukwa chake musamayanjane nawo anthu otere.

Pajatu inu nthawi ina munali mdima, koma tsopano ndinu kuwunika mwa Ambuye. Mukhale ngati ana akuwunika (pakuti pamene pali kuwunika pamapezekaponso zabwino zonse, chilungamo ndi choonadi).

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.