Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a gititi. Salimo la Asafu.
81 Imbani mwachimwemwe kwa Mulungu mphamvu yathu;
Fuwulani mokweza kwa Mulungu wa Yakobo!
2 Yambani nyimbo, imbani tambolini
imbani pangwe wolira bwino ndi zeze.
3 Imbani lipenga la nyanga ya nkhosa yayimuna pa mwezi watsopano,
ndi pamene mwezi waoneka wonse, pa tsiku la phwando;
4 ili ndi lamulo kwa Israeli,
langizo la Mulungu wa Yakobo.
5 Iye anapereka lamulolo kwa zidzukulu za Yosefe
pamene anatuluka kulimbana ndi Igupto,
kumene tinamva chiyankhulo chimene sitinachidziwe.
6 Iye akunena kuti, “Ine ndinachotsa zolemetsa pa mapewa awo;
Manja awo anamasulidwa mʼdengu.
7 Pa mavuto anu munayitana ndipo ndinakulanditsani,
ndinakuyankhani kuchokera mʼmitambo ya mabingu;
ndinakuyesani pa madzi a ku Meriba.
Sela
8 “Imvani anthu anga, ndipo ndidzakuchenjezani
ngati mungathe kumvetsera, Inu Israeli!
9 Musadzakhale ndi mulungu wachilendo pakati panu;
musadzagwadire mulungu wina.
10 Ine ndine Yehova Mulungu wanu,
amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto.
Yasamani kukamwa kwanu ndipo ndidzakudyetsani.
11 “Koma anthu anga sanandimvere;
Israeli sanandigonjere.
12 Kotero ndinawasiya ndi mitima yawo yosamverayo
kuti atsate zimene ankafuna.
13 “Anthu anga akanangondimvera,
Israeli akanatsatira njira zanga,
14 nʼkanafulumira motani kuti ndigonjetse adani awo
ndi kutembenuza mkono wanga kulimbana ndi amaliwongo!
15 Iwo amene amadana ndi Yehova akanakhwinyata pamaso pake,
ndipo chilango chawo chinakakhala mpaka kalekale.
16 Koma inu mukanadyetsedwa tirigu wabwino kwambiri;
ndikanakukhutitsani ndi uchi wochokera pa thanthwe.”
Isake ndi Rebeka
24 Tsopano Abrahamu anali atakalamba kwambiri, ndipo Yehova anamudalitsa mu zonse anachita. 2 Tsiku lina Abrahamu anawuza wantchito wake wamkulu amene ankayangʼanira zonse anali nazo, kuti “Ika dzanja lako pansi pa ntchafu yanga. 3 Ndikufuna kuti ulumbire pamaso pa Yehova, Mulungu wakumwamba ndi dziko lapansi, kuti sudzamupezera mwana wanga mkazi pakati pa atsikana Achikanaani a kuno kumene ndikukhala, 4 koma kuti udzapita ku dziko la kwathu ndi kukamupezera mkazi mwana wanga Isake pakati pa abale anga.”
5 Wantchito uja anafunsa kuti, “Nanga atakhala kuti mkaziyo sakufuna kubwera nane kuno? Kodi ine ndingadzatenge mwana wanu ndi kubwerera naye ku dziko kumene munachokera?”
6 Abrahamu anati, “Uwonetsetse kuti usadzabwerere naye mwana wanga kumeneko. 7 Yehova Mulungu wakumwamba amene ananditenga kwa makolo anga nanditulutsa mʼdziko lobadwira, ameneyo anayankhula nane molumbira kuti, ‘Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko ili.’ Iyeyu adzatumiza mngelo wake kuti akutsogolere kumeneko kukapezera mwana wanga mkazi. 8 Ngati mkaziyo adzakana kubwerera nawe ndiye kuti udzakhala womasuka ku lumbiro langa. Koma usadzamutenge mwana wanga ndi kubwerera naye kumeneko.” 9 Choncho wantchitoyo anayika dzanja lake pansi pa ntchafu ya mbuye wake Abrahamu nalumbira kwa iye kuti adzachitadi monga mwa mawu a Abrahamu.
10 Tsono wantchito uja anatengapo ngamira khumi mwa ngamira za mbuye wake pamodzi ndi zinthu zabwino za mitundumitundu. Ndipo ananyamuka kupita ku mzinda wa Nahori, mʼdziko la Mesopotamiya. 11 Atafika, anagwaditsa pansi ngamira zija pafupi ndi chitsime chimene chinali kunja kwa mzinda uja. Awa anali madzulo ndithu, nthawi imene amayi amapita kukatunga madzi.
12 Ndipo wantchito uja anapemphera nati, “Haa, Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abrahamu, mulole kuti zinthu zindiyendere ine lero, ndipo muonetseni mbuye wanga Abrahamu kukoma mtima kwanu kosasinthika. 13 Taonani ndayima pambali pa chitsimechi, ndipo atsikana a mu mzindawu akubwera kudzatunga madzi. 14 Ine ndipempha mtsikana wina kuti, ‘Chonde tula mtsuko wako kuti ndimweko madzi.’ Tsono iye akayankha kuti ‘Imwani,’ ndipo ndidzapatsanso ngamira zanu madziwo, ameneyo akhale mkazi amene mwasankhira mtumiki wanu Isake.” Zimenezi zikachitika, ndidzadziwa kuti mwaonetsadi kukoma mtima kwanu kosasinthika kwa mbuye wanga.
15 Asanatsirize kupemphera, anangoona Rebeka watulukira atasenza mtsuko wake pa phewa. Iyeyu anali mwana wa Betueli mwana wa Milika, mkazi wa Nahori mʼbale wake wa Abrahamu. 16 Mtsikanayo anali wokongola kwambiri, namwali amene sanadziwe mwamuna. Iye anatsikira ku chitsime nadzaza mtsuko nakweranso ku mtunda.
17 Wantchito uja anathamanga kukakumana naye nati, “Chonde patseko madzi pangʼono a mu mtsuko wakowo kuti ndimwe.”
18 Mtsikanayo anati, “Imwani mbuye wanga.” Ndipo mofulumira anatsitsa mtsuko uja nawuyika mʼmanja ndi kumupatsa kuti amwe.
19 Atatha kupereka madzi akumwa kwa mlendo uja, mtsikanayo anati, “Ndikatungiranso ngamira madzi kuti zimwe mpaka zitakwana.” 20 Choncho anafulumira kukhuthula madzi a mu mtsuko aja momwera ziweto, nathamanga kubwerera ku chitsime kukatunga madzi ena, ndipo anatunga okwanira ngamira zake zonse. 21 Modekha, munthu uja anayangʼanitsitsa kwambiri mtsikana uja kuti adziwedi ngati Yehova anamutsogolera pa ulendo wake uja kapena ayi.
22 Ngamira zija zitatha kumwa, mlendo uja anatulutsa chipini chagolide cholemera theka la sekeli ndi zibangiri zagolide ziwiri zolemera masekeli 100. 23 Kenaka anafunsa namwaliyo kuti, “Chonde tandiwuza, kodi ndiwe mwana wa yani? Ndipo kodi malo alipo kwanu woti ife nʼkugona?”
24 Anamuyankha kuti, “Ine ndine mwana wa Betueli, mwana amene Milika anaberekera Nahori.” 25 Ndipo anapitiriza kunena kuti, “Chakudya chodyetsa nyamazi chilipo kwathu ndipo malo woti mugone aliponso.”
26 Kenaka munthuyo anawerama pansi napembedza Yehova, 27 nati, “Alemekezeke Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abrahamu, amene waonetsa kukoma mtima kwake kosasintha ndi kukhulupirika kwake kwa mbuye wanga. Yehova wanditsogolera pa ulendo wanga mpaka ndafika ku nyumba kwa abale ake a mbuye wanga.”
1 Ndine mkulu wampingo, kulembera:
Mayi wosankhidwa ndi Mulungu ndi kwa ana ake amene ndimawakonda mʼchoonadi. Ndipo sindine ndekha amene ndimawakonda, komanso onse odziwa choonadi. 2 Timakukondani chifukwa cha choonadi chimene chimakhala mwa ife ndipo chidzakhala mwa ife mpaka muyaya.
3 Chisomo, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi kwa Yesu Khristu, Mwana wa Atate, zikhale ndi ife mʼchoonadi ndi mʼchikondi.
Choonadi ndi Chikondi
4 Ndinakondwera kwambiri nditapeza ana anu ena akuyenda mʼchoonadi, monga Atate anatilamulira. 5 Ndipo tsopano, amayi wokondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano koma lomwe lija takhala nalo kuyambira pachiyambi. Ine ndikukupemphani kuti tidzikondana wina ndi mnzake. 6 Ndipo chikondi ndiye kuyenda momvera malamulo ake. Lamulo lake ndi lakuti mukhale moyo wachikondi monga munamva kuyambira pachiyambi.
7 Ndikunena zimenezi chifukwa anthu ambiri onyenga, amene savomereza kuti Yesu Khristu anabwera monga munthu, akuyenda mʼdziko lapansi. Munthu aliyense otere ndi wonyenga ndiponso wokana Khristu. 8 Chenjerani kuti mungataye chimene mwagwirira ntchito, koma chitani khama kuti mukalandire mphotho yanu yonse. 9 Aliyense amene sasunga chiphunzitso cha Khristu, alibe Mulungu. Koma amene amasunga chiphunzitsochi, ameneyo alinso ndi Atate ndi Mwana. 10 Ngati wina aliyense abwera kwa inu osaphunzitsa zimenezi, musamulandire mʼnyumba mwanu kapena kumupatsa moni. 11 Aliyense wolandira munthu wotere ndiye kuti akuvomerezana nazo ntchito zake zoyipa.
12 Ndili nazo zambiri zoti ndikulembereni, koma sindikufuna kuzilemba mʼkalata. Mʼmalo mwake, ndikuyembekeza kufika kwanuko kuti tidzakambirane nanu pamaso ndi pamaso, potero chimwemwe chathu chidzakhala chathunthu.
13 Ana a mlongo wanu wosankhidwa ndi Mulungu akupereka moni.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.