Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 128

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

128 Odala ndi onse amene amaopa Yehova,
    amene amayenda mʼnjira zake.
Udzadya chipatso cha ntchito yako;
    madalitso ndi chuma zidzakhala zako.
Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka
    mʼkati mwa nyumba yako;
ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi
    kuzungulira tebulo lako.
Ameneyu ndiye munthu wodalitsidwa
    amene amaopa Yehova.

Yehova akudalitse kuchokera mʼZiyoni
    masiku onse a moyo wako;
uwone zokoma za Yerusalemu,
    ndipo ukhale ndi moyo kuti udzaone zidzukulu zako.

Mtendere ukhale ndi Israeli.

Ezekieli 36:22-32

22 “Nʼchifukwa chake awuze Aisraeliwo kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndidzachita zimene ndidzachitezo osati chifukwa cha inuyo Aisraelinu ayi, koma chifukwa cha dzina langa, limene mwaliyipitsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene munapitako. 23 Ndidzaonetsa chiyero cha dzina langa lotchuka, limene layipitsidwa pakati pawo. Anthu a mitundu inayo atadzazindikira kuti ndaonetsa kudzera mwa inu kuti dzina langa ndi loyera, iwo adzadziwanso kuti Ine ndine Yehova. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.

24 “Pakuti Ine ndidzakuchotsani pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzakusonkhanitsani kuchoka ku mayiko onse ndi kukubwezerani ku dziko lanulanu. 25 Ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera mtima. Zonse zimene zimakuyipitsani zidzachoka. Ndidzakuyeretsani pochotsa mafano anu onse. 26 Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kulowetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzachotsa mwa inu mtima wanu wowuma ngati mwala ndi kukupatsani mtima wofewa ngati mnofu. 27 Ndipo ndidzayika Mzimu wanga mwa inu ndipo ndidzakuthandizani kutsatira malangizo anga ndi kukusungitsani mosamala kwambiri malamulo anga. 28 Mudzakhala mʼdziko limene ndinapatsa makolo anu. Mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu. 29 Ndidzakupulumutsani ku zonse zokuyipitsani. Ndidzakuchulukitsirani tirigu ndipo sindidzakugwetseraninso njala. 30 Ndidzachulukitsa zipatso za mʼmitengo yanu ndi zokolola za mʼmunda mwanu, kotero kuti simudzanyozedwanso pakati pa anthu a mitundu ina chifukwa cha njala. 31 Pamenepo mudzakumbukira makhalidwe anu oyipa ndi ntchito zanu zoyipa. Machimo anu ndi ntchito zanu zonyansa zidzakuchititsa nokha manyazi. 32 Tsono dziwani kuti Ine sindidzachita zimenezi chifukwa cha inuyo ayi, ndikutero Ine Ambuye Wamphamvuzonse. Ndiyetu chitani manyazi ndipo mugwetse nkhope zanu, inu Aisraeli chifukwa cha makhalidwe anu!

Yohane 7:53-8:11

[Mipukutu yoyambirira ndi maumboni akale mulibe 7:53 mpaka 8:11]

Za Mkazi Wachigololo

53 Kenaka onse anachoka, napita kwawo. Koma Yesu anapita ku phiri la Olivi. Mmamawa Iye anaonekeranso ku Nyumba ya Mulungu kumene anthu onse anamuzungulira ndipo Iye anakhala pansi nawaphunzitsa. Aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi anabweretsa mkazi amene anagwidwa akuchita chigololo. Iwo anamuyimiritsa patsogolo pa anthu ndipo anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, mkazi uyu tinamugwira akuchita chigololo. Mʼmalamulo a Mose anatilamulira kuti akazi otere tiwagende ndi miyala. Tsopano Inu mukuti chiyani?” Iwo anagwiritsa ntchito funsoli ngati msampha, ndi cholinga choti apeze chifukwa cha kumuneneza Iye.

Koma Yesu anawerama pansi ndi kuyamba kulemba pa dothi ndi chala chake. Pamene iwo anapitirira kumufunsa, Iye anaweramuka ndipo anawawuza kuti, “Ngati wina wa inu alipo wopanda tchimo, ayambe iyeyo kumugenda ndi miyala mkaziyu.” Iye anaweramanso pansi ndi kulemba pa dothi.

Iwo atamva izi anayamba kuchoka mmodzimmodzi, akuluakulu poyamba, mpaka Yesu anatsala yekha ndi mkaziyo atayimirira pomwepo. 10 Yesu anaweramuka ndipo anamufunsa iye kuti, “Akuluakulu aja ali kuti? Kodi palibe amene wakutsutsa?”

11 Iye anati, “Ambuye, palibe ndi mmodzi yemwe.”

“Inenso sindikukutsutsa iwe. Pita kuyambira tsopano usakachimwenso.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.