Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 128

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

128 Odala ndi onse amene amaopa Yehova,
    amene amayenda mʼnjira zake.
Udzadya chipatso cha ntchito yako;
    madalitso ndi chuma zidzakhala zako.
Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka
    mʼkati mwa nyumba yako;
ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi
    kuzungulira tebulo lako.
Ameneyu ndiye munthu wodalitsidwa
    amene amaopa Yehova.

Yehova akudalitse kuchokera mʼZiyoni
    masiku onse a moyo wako;
uwone zokoma za Yerusalemu,
    ndipo ukhale ndi moyo kuti udzaone zidzukulu zako.

Mtendere ukhale ndi Israeli.

Yesaya 65:17-25

Chilengedwe Chatsopano

17 “Taonani, ndikulenga
    mlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.
Zinthu zakale sizidzakumbukika,
    zidzayiwalika kotheratu.
18 Koma inu mukhale osangalala ndi okondwa mpaka muyaya
    chifukwa cha zimene ndikulenga,
pakuti ndikulenga Yerusalemu kukhala malo wosangalatsa
    ndipo anthu ake adzakhala achimwemwe.
19 Ine ndidzakondwa chifuwa cha Yerusalemu
    ndipo ndidzasangalala chifukwa cha anthu anga.
Kumeneko sikudzamvekanso kulira
    ndi mfuwu wodandaula.

20 “Ana sadzafa ali akhanda
    ndipo nkhalamba zonse zidzakwaniritsa zaka zawo zonse.
    Wamngʼono mwa iwo
adzafa ali ndi zaka 100.
    Amene adzalephere kufika zaka 100
adzatengedwa kukhala
    wotembereredwa.
21 Anthu adzamanga nyumba ndi kukhalamo,
    adzadzala mpesa ndipo adzadya zipatso zake.
22 Sadzamanganso nyumba anthu ena nʼkukhalamo,
    kapena kudzala ndi ena nʼkudya.
Pakuti anthu anga adzakhala ndi moyo
    wautali ngati mitengo.
Osankhidwa anga adzakondwera ndi ntchito
    ya manja awo nthawi yayitali.
23 Sadzagwira ntchito pachabe
    kapena kubereka ana kuti aone tsoka;
chifukwa adzakhala anthu odalitsidwa ndi Yehova,
    iwowo pamodzi ndi adzukulu awo omwe.
24 Ndidzawayankha ngakhale asanathe nʼkupempha komwe.
    Pamene akuyankhula kumene Ine ndidzakhala nditamva kale.
25 Mʼmbulu ndi mwana wankhosa wamkazi zidzadyera pamodzi.
    Mkango udzadya udzu monga ngʼombe,
    koma fumbi ndiye chidzakhale chakudya cha njoka.
Pa phiri langa lopatulika sipadzakhala
    chinthu chopweteka kapena chowononga,”
            akutero Yehova.

Aroma 4:6-13

Davide ponena zomwezi pamene anayankhula za kudala kwa munthu amene Mulungu amulungamitsa osati chifukwa cha ntchito zake akuti,

“Odala ndi amene
    zoyipa zawo zakhululukidwa;
    amene machimo awo afafanizidwa.
Ngodala munthu amene
    machimo ake Ambuye sadzawakumbukiranso.”

Kodi madalitso amenewa ali kwa ochita mdulidwe okha kapena kwa amene sanachitepo mdulidwe? Ife takhala tikunena kuti chikhulupiriro cha Abrahamu chinamuchititsa kukhala wolungama. 10 Kodi chinatengedwa bwanji? Kodi nʼkuti iye atachita mdulidwe kapena asanachite? Osati atachita mdulidwe koma asanachite! 11 Ndipo iye anachita mdulidwe ngati chizindikiro ndi chitsimikizo cha kulungama kumene anali nako mwachikhulupiriro pomwe anali asanachite mdulidwe. Choncho, iye ndi kholo la onse amene akhulupirira koma sanachite mdulidwe, ndi cholinga chakuti alungamitsidwe. 12 Ndipo iyenso ndiyenso kholo la ochita mdulidwe osati amene anangochita mdulidwe kokha koma amene amatsata chitsanzo cha chikhulupiriro chimene kholo lathu Abrahamu anali nacho asanachite mdulidwe.

13 Abrahamu ndi zidzukulu zake sanalandire lonjezano lakuti adzalandira dziko lapansi kudzera mu Malamulo, koma kudzera mu chilungamo chimene chimabwera ndi chikhulupiriro.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.