Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
128 Odala ndi onse amene amaopa Yehova,
amene amayenda mʼnjira zake.
2 Udzadya chipatso cha ntchito yako;
madalitso ndi chuma zidzakhala zako.
3 Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka
mʼkati mwa nyumba yako;
ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi
kuzungulira tebulo lako.
4 Ameneyu ndiye munthu wodalitsidwa
amene amaopa Yehova.
5 Yehova akudalitse kuchokera mʼZiyoni
masiku onse a moyo wako;
uwone zokoma za Yerusalemu,
6 ndipo ukhale ndi moyo kuti udzaone zidzukulu zako.
Mtendere ukhale ndi Israeli.
Njoka Yamkuwa
4 Aisraeli anayenda kuchokera ku phiri la Hori kudzera njira ya ku Nyanja Yofiira kuzungulira dziko la Edomu. Koma anthu anataya mtima mʼnjiramo 5 ndipo anayankhula motsutsana ndi Mulungu ndi Mose, nati, “Chifukwa chiyani munatitulutsa kuchoka mʼdziko la Igupto kuti tidzafere mʼchipululu muno? Kuno kulibe chakudya, kulibe madzi ndipo chakudya cha chabechabechi tatopa nacho.”
6 Choncho Yehova anatumiza njoka zaululu pakati pawo. Zinaluma anthu ndipo Aisraeli ambiri anafa. 7 Anthuwo anabwera kwa Mose ndi kunena kuti, “Tachimwa chifukwa tayankhula motsutsana ndi Yehova komanso inu. Pempherani kwa Yehova kuti atichotsere njokazi.” Tsono Mose anapempherera anthuwo.
8 Yehova anati kwa Mose, “Upange njoka yaululu ndipo uyipachike pa mtengo. Aliyense amene walumidwa akangoyangʼana njokayo adzakhala ndi moyo.” 9 Pamenepo Mose anapanga njoka yamkuwa ndi kuyipachika pa mtengo. Ndipo aliyense wolumidwa akayangʼana njoka yamkuwayo ankakhala ndi moyo.
Yesu ndi Wamkulu Kuposa Mose
3 Nʼchifukwa chake abale oyera mtima, amenenso munayitanidwa ndi kumwamba, lingalirani za Yesu amene ndi Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chikhulupiriro chimene timavomereza. 2 Iye anali wokhulupirika kwa Mulungu amene anamupatsa udindowo, monga momwe Mose anali wokhulupirika mʼnyumba yonse ya Mulungu. 3 Yesu anapezeka woyenera kulandira ulemu waukulu kuposa Mose, monga momwemonso womanga nyumba amalandira ulemu waukulu kuposa nyumbayo. 4 Pakuti nyumba iliyonse imamangidwa ndi munthu wina, koma amene anapanga zonse ndi Mulungu. 5 Mose anali wokhulupirika monga mtumiki mʼnyumba yonse ya Mulungu, kuchitira umboni zimene zidzayankhulidwe mʼtsogolo. 6 Koma Khristu ndi wokhulupirika monga mwana pa nyumba ya Mulungu. Ndipo ndife nyumba yake ngati tipitirire kulimbika mtima ndi kunyadira zomwe tikuyembekerazo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.