Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Genesis 12:1-4

Mulungu Ayitana Abramu

12 Tsiku lina Yehova anamuwuza Abramu kuti, “Tuluka mʼdziko lako. Siya abale ako ndi banja la abambo ako ndipo pita ku dziko limene ndidzakusonyeza.

“Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu wa anthu
    ndipo ndidzakudalitsa;
ndi kukusandutsa wotchuka kotero kuti
    udzakhala dalitso kwa anthu ambiri.
Ndidzadalitsa amene adzadalitsa iwe,
    ndi kutemberera amene adzatemberera iwe;
ndipo mafuko onse a pa dziko lapansi
    adzadalitsika kudzera mwa iwe.”

Choncho Abramu ananyamuka monga momwe Yehova anamuwuzira, napita pamodzi ndi Loti. Pamene Abramu amachoka ku Harani nʼkuti ali ndi zaka 75.

Masalimo 121

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

121 Ndikweza maso anga ku mapiri;
    kodi thandizo langa limachokera kuti?
Thandizo langa limachokera kwa Yehova,
    wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Sadzalola kuti phazi lako literereke;
    Iye amene amakusunga sadzawodzera.
Taonani, Iye amene amasunga Israeli
    sadzawodzera kapena kugona.

Yehova ndiye amene amakusunga;
    Yehova ndiye mthunzi wako ku dzanja lako lamanja.
Dzuwa silidzakupweteka nthawi ya masana,
    kapena mwezi nthawi ya usiku.

Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse;
    adzasunga moyo wako.
Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako;
    kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Aroma 4:1-5

Abrahamu Analungamitsidwa Mwachikhulupiriro

Nanga tsono tidzati chiyani za Abrahamu kholo lathu, iyeyu anapezana ndi zotani pa nkhani imeneyi? Kunena zoona, Abrahamu akanalungamitsidwa ndi ntchito zake, akanakhala nako kanthu kodzitamandira, koma osati pamaso pa Mulungu. Kodi Malemba akuti chiyani? “Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo ichi chinamuchititsa kukhala wolungama.”

Tsopano munthu amene wagwira ntchito, malipiro ake satengedwa kukhala ngati mphatso koma zimene anayenera kulandira. Koma kwa munthu amene sanagwire ntchito ndipo akhulupirira Mulungu amene amalungamitsa ochimwa, chikhulupiriro chakecho chimatengedwa kukhala chilungamo.

Aroma 4:13-17

13 Abrahamu ndi zidzukulu zake sanalandire lonjezano lakuti adzalandira dziko lapansi kudzera mu Malamulo, koma kudzera mu chilungamo chimene chimabwera ndi chikhulupiriro. 14 Pakuti ngati amene amadalira Malamulo ndiye olowa mʼmalo, ndiye kuti chikhulupiriro nʼchopanda pake ndipo lonjezano ndi lopanda phindu 15 chifukwa Malamulo anabweretsa chilango. Ndipo kumene kulibe Malamulo kulibenso kuwalakwitsa.

16 Motero, timalandira lonjezo mwachikhulupiriro. Laperekedwa mwachisomo kuti patsimikizidwe kuti lonjezolo liperekedwa kwa ana ndi zidzukulu zonse za Abrahamu, osati kwa iwo okha amene amatsatira Malamulo komanso kwa iwo amene ali ndi chikhulupiriro cha Abrahamu. Iye ndiye kholo la ife tonse. 17 Monga kwalembedwa kuti, “Ine ndakusandutsa kukhala kholo la mitundu yambiri.” Iye ndiye kholo lathu pamaso pa Mulungu, amene anamukhulupirira, Mulungu amene amapereka moyo kwa akufa ndipo amapereka moyo kwa zinthu zopanda moyo.

Yohane 3:1-17

Yesu Aphunzitsa Nekodimo za Kubadwa Kwatsopano

Ndipo panali Mfarisi wotchedwa Nekodimo, wa mʼgulu lolamulira la Ayuda. Iye anabwera kwa Yesu usiku ndipo anati, “Rabi, ife tikudziwa kuti ndinu aphunzitsi wochokera kwa Mulungu, pakuti palibe amene angachite zizindikiro zodabwitsa zimene Inu mukuchita ngati Mulungu sali naye.”

Poyankha Yesu ananena kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti, ngati munthu sabadwanso mwatsopano sangathe kuona ufumu wa Mulungu.”

Nekodimo anati, “Kodi munthu angabadwenso bwanji atakalamba? Kodi angalowe kachiwiri mʼmimba ya amayi ake kuti abadwenso?”

Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu Woyera, sangalowe mu ufumu wa Mulungu. Thupi limabereka thupi, koma Mzimu amabereka mzimu. Iwe usadabwe chifukwa ndakuwuza kuti, ‘Uyenera kubadwanso.’ Mphepo imawomba kulikonse kumene ikufuna. Ungathe kumva kuwomba kwake, koma sungathe kudziwa kumene ikuchokera kapena kumene ikupita. Nʼchimodzimodzi ndi amene abadwa ndi Mzimu Woyera.”

Nekodimo anafunsa kuti, “Kodi izi zingatheke bwanji?”

10 Yesu anati, “Iwe mphunzitsi wa Israeli, kodi sukuzindikira zimenezi? 11 Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ife tiyankhula zimene tikuzidziwa ndi kuchitira umboni zimene taziona, komabe inu simuvomereza umboni wathu. 12 Ine ndikuyankhula kwa iwe zinthu za dziko lapansi ndipo sukukhulupirira. Nanga kodi udzakhulupirira bwanji ngati nditayankhula zinthu zakumwamba? 13 Palibe wina aliyense anapita kumwamba, koma yekhayo amene watsika kuchokera kumwamba, Mwana wa Munthu. 14 Tsono monga Mose anapachika njoka mʼchipululu, moteronso Mwana wa Munthu ayenera kupachikidwa, 15 kuti aliyense amene akhulupirira Iye akhale ndi moyo wosatha.

16 “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha. 17 Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake ku dziko lapansi, kuti akaweruze, koma kuti akapulumutse dziko lapansi.

Mateyu 17:1-9

Maonekedwe Aulemerero a Yesu pa Phiri

17 Patapita masiku asanu ndi limodzi Yesu anatenga Petro, Yakobo, ndi Yohane mʼbale wa Yakobo pa okha ndipo anakwera nawo pa phiri lalitali. Pamenepo Iye anasinthika maonekedwe ake pamaso pawo. Nkhope yake inawala ngati dzuwa ndipo zovala zake zinayera kuti mbuu. Nthawi yomweyo Mose ndi Eliya anaonekera kwa iwo akuyankhulana ndi Yesu.

Petro anati kwa Yesu, “Ambuye ndi bwino kuti ife tikhale pano. Ngati mufuna ndidzamanga misasa itatu umodzi wanu, wina wa Mose ndi wina wa Eliya.”

Iye akuyankhulabe, mtambo owala unawaphimba, ndipo mawu ochokera mu mtambo anati, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimukonda ndipo ndikondwera naye kwambiri. Mumumvere Iye!”

Ophunzira atamva zimenezi, anachita mantha nagwa pansi chafufumimba. Ndipo Yesu anabwera nawakhudza nati, “Dzukani, musaope.” Atayangʼana, sanaone wina aliyense kupatula Yesu yekha.

Akutsika ku phiriko, Yesu anawalamula kuti, “Musawuze wina aliyense zimene mwaona, mpaka Mwana wa Munthu ataukitsidwa kwa akufa.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.