Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 121

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

121 Ndikweza maso anga ku mapiri;
    kodi thandizo langa limachokera kuti?
Thandizo langa limachokera kwa Yehova,
    wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Sadzalola kuti phazi lako literereke;
    Iye amene amakusunga sadzawodzera.
Taonani, Iye amene amasunga Israeli
    sadzawodzera kapena kugona.

Yehova ndiye amene amakusunga;
    Yehova ndiye mthunzi wako ku dzanja lako lamanja.
Dzuwa silidzakupweteka nthawi ya masana,
    kapena mwezi nthawi ya usiku.

Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse;
    adzasunga moyo wako.
Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako;
    kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Yesaya 51:4-8

“Mverani Ine, anthu anga:
    tcherani khutu, inu mtundu wanga:
malangizo adzachokera kwa Ine;
    cholungama changa chidzawunikira anthu a mitundu yonse.
Ndili pafupi kubwera kudzawombola anthu anga.
    Ndidzabwera mofulumira ngati kuwunika kudzapulumutsa anthu anga;
    ndipo ndidzalamulira anthu a mitundu yonse.
Mayiko akutali akundiyembekezera.
    Iwo akudikira kuti ndidzawapulumutse.
Kwezani maso anu mlengalenga,
    yangʼanani pansi pa dziko;
mlengalenga udzazimirira ngati utsi,
    dziko lapansi lidzatha ngati chovala
    ndipo anthu ake adzafa ngati nsabwe.
Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka muyaya,
    chilungamo changa chidzakhala cha nthawi zonse.

“Mverani Ine, inu amene mukudziwa choonadi,
    anthu inu amene mukusunga malangizo anga mʼmitima yanu;
musaope kudzudzulidwa ndi anthu
    kapena kuopsezedwa akamakulalatirani.
Pakuti njenjete idzawadya ngati chovala;
    mbozi idzawadya ngati thonje.
Koma chilungamo changa chidzakhala mpaka muyaya,
    chipulumutso changa chidzakhala mpaka mibadomibado.”

Luka 7:1-10

Chikhulupiriro cha Kenturiyo

Yesu atamaliza kunena zonsezi pamaso pa anthu amene ankamvetsera, analowa mu Kaperenawo. Kumeneko wantchito wa Kenturiyo, amene amamukhulupirira kwambiri, anadwala ndipo anali pafupi kufa. Kenturiyo anamva za Yesu ndipo anatumiza ena a akulu Ayuda kwa Iye kuti abwere adzachiritse wantchito wakeyo. Iwo atafika kwa Yesu, anamudandaulira kwambiri, nati, “Munthuyu ayenera kuthandizidwa chifukwa amakonda mtundu wathu ndipo anatimangira sunagoge wathu.” Pamenepo Yesu anapita nawo.

Iye sanali patali ndi nyumba pamene Kenturiyo anatumiza anzake kuti akamuwuze kuti, “Ambuye, musadzivutitse, pakuti ndine wosayenera kuti mulowe mʼnyumba mwanga. Nʼchifukwa chake sindinadziyenereze ndi pangʼono pomwe kuti ndibwere kwa inu. Koma nenani mawu, ndipo wantchito wanga adzachira. Pakuti ndili pansi paulamuliro, ndiponso ndili ndi asilikali pansi panga. Ndikamuwuza uyu kuti, ‘Pita,’ iye amapita; ndi uyo kuti, ‘Bwera,’ amabwera. Ndikamuwuza wantchito wanga kuti, ‘Chita ichi,’ amachita.”

Yesu atamva izi, anadabwa naye, ndipo anatembenukira gulu la anthu limene limamutsatira nati, “Ndikukuwuzani kuti, sindinapeze chikhulupiriro chachikulu ngati ichi mu Israeli.” 10 Kenaka anthu amene anatumidwawo anabwerera ku nyumba ndipo anakamupeza wantchitoyo atachira.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.