Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
121 Ndikweza maso anga ku mapiri;
kodi thandizo langa limachokera kuti?
2 Thandizo langa limachokera kwa Yehova,
wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
3 Sadzalola kuti phazi lako literereke;
Iye amene amakusunga sadzawodzera.
4 Taonani, Iye amene amasunga Israeli
sadzawodzera kapena kugona.
5 Yehova ndiye amene amakusunga;
Yehova ndiye mthunzi wako ku dzanja lako lamanja.
6 Dzuwa silidzakupweteka nthawi ya masana,
kapena mwezi nthawi ya usiku.
7 Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse;
adzasunga moyo wako.
8 Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako;
kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Chipulumutso Chamuyaya cha Ziyoni
51 “Mverani Ine, inu amene mukufuna chipulumutso
ndiponso amene mumafunafuna Yehova:
Taganizani za thanthwe kumene munasemedwa
ndipo ku ngwenya kumene anakukumbani;
2 taganizani za Abrahamu, kholo lanu,
ndi Sara, amene anakubalani.
Pamene ndinkamuyitana nʼkuti alibe mwana,
koma ndinamudalitsa ndi kumupatsa ana ambiri.
3 Yehova adzatonthozadi Ziyoni,
ndipo adzachitira chifundo mabwinja ake onse;
Dziko lake la chipululu adzalisandutsa ngati Edeni,
malo ake owuma ngati munda wa Yehova.
Anthu adzayimba nyimbo zonditamanda
ndi kundiyamika.
Chilimbikitso Pokhala Wokhulupirika
3 Ndikuyamika Mulungu amene ndimamutumikira ndi chikumbumtima chosatsutsika, monga momwe ankachitira makolo anga. Usiku ndi usana ndimakukumbukira mosalekeza mʼmapemphero anga. 4 Ndikamakumbukira misozi yako, ndimalakalaka nditakuona kuti ndidzazidwe ndi chimwemwe. 5 Ndakumbukira za chikhulupiriro chako choona chimene chinayamba mwa agogo ako a Loisi ndi mwa amayi ako Yunike ndipo ndikutsimikiza mtima kuti chilinso mwa iwe.
Kumvera Paulo ndi Uthenga Wabwino
6 Nʼchifukwa chake ndikukukumbutsa kuti upemerere monga amachitira moto, mphatso imene Mulungu anakupatsa nditakusanjika manja. 7 Pakuti Mzimu amene Mulungu anatipatsa, si Mzimu wotipatsa manyazi, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzisunga.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.