Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Davide. Malangizo.
32 Ngodala munthu
amene zolakwa zake zakhululukidwa;
amene machimo ake aphimbidwa.
2 Ngodala munthu
amene machimo ake Yehova sawawerengeranso pa iye
ndipo mu mzimu mwake mulibe chinyengo.
3 Pamene ndinali chete,
mafupa anga anakalamba
chifukwa cha kubuwula kwanga tsiku lonse.
4 Pakuti usana ndi usiku
dzanja lanu linandipsinja;
mphamvu zanga zinatha
monga nthawi yotentha yachilimwe.
Sela
5 Kotero ine ndinavomereza tchimo langa kwa Inu,
sindinabise mphulupulu zanga.
Ndinati, “Ine ndidzawulula
zolakwa zanga kwa Yehova,
ndipo Inu munandikhululukira
mlandu wa machimo anga.”
Sela
6 Choncho aliyense okhulupirika apemphere kwa Inuyo
pomwe mukupezeka;
ndithu pamene madzi amphamvu auka,
sadzamupeza.
7 Inu ndi malo anga obisala;
muzinditeteza ku mavuto ndipo muzindizinga
ndi nyimbo zachipulumutso.
Sela
8 Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo;
ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira.
9 Usakhale ngati kavalo kapena bulu,
zimene zilibe nzeru,
koma ziyenera kuwongoleredwa ndi zitsulo za mʼkamwa ndi pamutu,
ukapanda kutero sizibwera kwa iwe.
10 Zowawa ndi zambiri za anthu oyipa
koma chikondi chosatha cha Yehova
chimamuzinga munthu amene amadalira Iye.
11 Kondwerani mwa Yehova inu olungama;
imbani, inu nonse amene muli owongoka mtima!
Miyala ina Yatsopano
34 Yehova anati kwa Mose, “Sema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija, ndipo Ine ndidzalembapo mawu amene anali pa miyala yoyamba ija, imene unayiphwanya. 2 Ukonzeke mmamawa, ndipo ubwere ku Phiri la Sinai. Udzaonekera pamaso panga pamwamba pa phiri. 3 Palibe amene abwere nawe kapena kuoneka pena paliponse pafupi ndi phiri. Ndipo ngakhale nkhosa kapena ngʼombe zisadye mʼmbali mwa phirilo.”
4 Choncho Mose anasema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija ndipo anapita ku Phiri la Sinai mmawa atanyamula miyala iwiri mʼmanja mwake monga momwe Yehova anamulamulira. 5 Ndipo Yehova anatsika mu mtambo ndi kuyima pamodzi ndi Mose ndi kulengeza dzina lake lakuti Yehova. 6 Ndipo Iye anadutsa kutsogolo kwa Mose akulengeza kuti, “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosapsa mtima msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika, 7 waonetsa chikondi chosasinthika kwa anthu miyandamiyanda, wokhululukira zoyipa, kuwukira, ndiponso tchimo, komatu salekerera ochimwa kuti asalangidwe. Iye amalanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha machimo a makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi.”
8 Pamenepo Mose anawerama pansi napembedza. 9 Iye anati, “Chonde Ambuye, ngati ndapeza chisomo pamaso panu, lolani Ambuye kuti mupite nafe pamodzi. Ngakhale kuti anthuwa ndi nkhutukumve, khululukirani zoyipa ndi machimo athu, ndipo mutenge ife kukhala anthu anu.”
27 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Lemba mawu awa pakuti potsatira mawuwa, ine ndipangana pangano ndi iwe ndi Israeli.” 28 Mose anakhala kumeneko pamodzi ndi Yehova masiku 40, usana ndi usiku, wosadya kanthu kapena kumwa madzi. Ndipo iye analemba pa miyala ija mawu a pangano, malamulo khumi.
Fanizo la Nkhosa Yotayika
10 “Onetsetsani kuti musanyoze mmodzi wa anawa. Pakuti ndikuwuzani kuti angelo awo kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga akumwamba nthawi zonse.” 11 (Mwana wa Munthu anabwera kudzapulumutsa chimene chinatayika).
12 “Kodi mukuganiza bwanji? Ngati munthu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi nʼkusowa, kodi sasiya 99 zija mʼmapiri ndi kupita kukafuna imodzi yosocherayo? 13 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti akayipeza amasangalala kwambiri chifukwa cha nkhosa imodziyo kuposa nkhosa 99 zimene sizinasochere. 14 Chimodzimodzinso Atate anu akumwamba safuna kuti mmodzi wa anawa atayike.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.