Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 32

Salimo la Davide. Malangizo.

32 Ngodala munthu
    amene zolakwa zake zakhululukidwa;
    amene machimo ake aphimbidwa.
Ngodala munthu
    amene machimo ake Yehova sawawerengeranso pa iye
    ndipo mu mzimu mwake mulibe chinyengo.

Pamene ndinali chete,
    mafupa anga anakalamba
    chifukwa cha kubuwula kwanga tsiku lonse.
Pakuti usana ndi usiku
    dzanja lanu linandipsinja;
mphamvu zanga zinatha
    monga nthawi yotentha yachilimwe.
            Sela
Kotero ine ndinavomereza tchimo langa kwa Inu,
    sindinabise mphulupulu zanga.
Ndinati, “Ine ndidzawulula
    zolakwa zanga kwa Yehova,
ndipo Inu munandikhululukira
    mlandu wa machimo anga.”
            Sela

Choncho aliyense okhulupirika apemphere kwa Inuyo
    pomwe mukupezeka;
ndithu pamene madzi amphamvu auka,
    sadzamupeza.
Inu ndi malo anga obisala;
    muzinditeteza ku mavuto ndipo muzindizinga
    ndi nyimbo zachipulumutso.
            Sela

Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo;
    ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira.
Usakhale ngati kavalo kapena bulu,
    zimene zilibe nzeru,
koma ziyenera kuwongoleredwa ndi zitsulo za mʼkamwa ndi pamutu,
    ukapanda kutero sizibwera kwa iwe.
10 Zowawa ndi zambiri za anthu oyipa
    koma chikondi chosatha cha Yehova
    chimamuzinga munthu amene amadalira Iye.

11 Kondwerani mwa Yehova inu olungama;
    imbani, inu nonse amene muli owongoka mtima!

Genesis 4:1-16

Kaini ndi Abele

Adamu anagona malo amodzi ndi Hava mkazi wake ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala Kaini, ndipo anati, “Ndi thandizo la Yehova ndapeza mwana wamwamuna.” Kenaka anabereka mʼbale wake Abele.

Abele anali woweta nkhosa ndipo Kaini anali mlimi. Patapita nthawi, Kaini anatenga zipatso za ku munda nakazipereka kwa Yehova monga nsembe. Nayenso Abele anatenga ana ankhosa oyamba kubadwa pamodzi ndi mafuta ake nakazipereka ngati nsembe kwa Yehova. Yehova anakondwera ndi Abele ndi nsembe yake. Koma sanakondwere ndi Kaini ndi nsembe yake. Kotero Kaini anakwiya kwambiri ndipo nkhope yake inagwa.

Choncho Yehova anati kwa Kaini, “Chifukwa chiyani wakwiya ndipo bwanji nkhope yako yagwa? Ukanachita zabwino sindikanakulandira kodi? Koma tsopano wachita zoyipa ndipo tchimo likukudikira pa khomo pako, likufuna kukugwira; koma iwe uyenera kugonjetsa tchimolo.”

Tsiku lina Kaini anati kwa mʼbale wake Abele, “Tiye tipite ku munda.” Ndipo ali ku mundako, Kaini anawukira mʼbale wake namupha.

Ndipo Yehova anamufunsa Kaini kuti, “Ali kuti mʼbale wako Abele?”

Iye anayankha kuti, “Sindikudziwa. Kodi ine ndine wosunga mʼbale wanga?”

10 Yehova anati, “Kodi wachita chiyani? Tamvera! Magazi a mʼbale wako akulirira kwa Ine kuchokera mʼnthaka. 11 Ndipo tsopano ndiwe wotembereredwa ndipo wachotsedwa mʼdziko limene nthaka yake inatsekula pakamwa pake kulandira magazi a mʼbale wako amene unakhetsa. 12 Udzalima munda koma nthakayo sidzakupatsanso zokolola zake. Udzakhala wosakhazikika; womangoyendayenda pa dziko lapansi.”

13 Kaini anati kwa Yehova, “Chilango changa ndi chachikulu kuposera mphamvu zanga. 14 Lero mukundipirikitsa pa dziko ndi pamaso panu; ndidzakhala wosakhazikika, woyendayenda, ndipo aliyense amene adzandipeze adzandipha.”

15 Koma Yehova anamuwuza kuti, “Sizidzatero ayi; aliyense amene adzaphe Kaini adzalangidwa ndi kulipiritsidwa kasanu ndi kawiri.” Pamenepo Yehova anayika chizindikiro pa Kaini kuti aliyense womupeza asamuphe. 16 Ndipo Kaini anachoka pamaso pa Yehova nakakhala ku dziko la Nodi, kummawa kwa Edeni.

Ahebri 4:14-5:10

Yesu Mkulu wa Ansembe Wopambana

14 Popeza kuti tili ndi Mkulu wa ansembe wopambana, amene analowa kale kumwamba, Yesu Mwana wa Mulungu, tiyeni tigwiritsitse chikhulupiriro chathu chimene timavomereza. 15 Pakuti sitili ndi Mkulu wa ansembe amene sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofowoka zathu. Koma tili naye amene anayesedwa mʼnjira zonse monga ife, koma sanachimwe. 16 Tiyeni tsono tiyandikire ku mpando waufumu, wachisomo mopanda mantha, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo chotithandiza pa nthawi yeniyeni.

Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa kuchokera pakati pa anthu ndipo amayikidwa kuti aziwayimirira pamaso pa Mulungu, kuti azipereka mphatso ndi nsembe chifukwa cha machimo. Popeza kuti iye mwini ali ndi zofowoka zake, amatha kuwalezera mtima amene ali osadziwa ndi osochera. Chifukwa cha ichi, iye amadziperekera nsembe chifukwa cha machimo ake omwe ndiponso chifukwa cha machimo a anthu ena.

Palibe amene amadzipatsa yekha ulemu wotere, koma amachita kuyitanidwa ndi Mulungu monga momwe anayitanidwira Aaroni. Nʼchifukwa chake Khristu sanadzipatse yekha ulemu wokhala Mkulu wa ansembe. Koma Mulungu anamuwuza kuti,

“Iwe ndiwe Mwana wanga;
    Ine lero ndakhala Atate ako.”

Ndipo penanso anati,

“Iwe ndiwe wansembe mpaka muyaya,
    monga mwa unsembe wa Melikizedeki.”

Yesu, pa nthawi imene anali munthu pa dziko lapansi pano, anapereka mapemphero ake ndi zopempha mofuwula ndi misozi kwa Iye amene akanamupulumutsa ku imfa, ndipo anamumvera chifukwa anagonjera modzipereka. Ngakhale Iye anali Mwana wa Mulungu anaphunzira kumvera pomva zowawa. Atasanduka wangwiro kotheratu, anakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye. 10 Ndipo Mulungu anamuyika kukhala Mkulu wa ansembe, monga mwa dongosolo la unsembe wa Melikizedeki.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.