Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
17 Komabe iwowo anapitiriza kumuchimwira Iye,
kuwukira Wammwambamwamba mʼchipululu.
18 Ananyoza Mulungu mwadala
pomuwumiriza kuti awapatse chakudya chimene anachilakalaka.
19 Iwo anayankhula motsutsana naye ponena kuti,
“Kodi Mulungu angatipatse chakudya mʼchipululu?
20 Iye atamenya thanthwe
madzi anatuluka,
ndipo mitsinje inadzaza ndi madzi.
Koma iye angatipatsenso ife chakudya?
Kodi angapereke nyama kwa anthu akewa?”
52 Koma Iye anatulutsa anthu ake ngati ziweto;
anawatsogolera ngati nkhosa kudutsa mʼchipululu.
53 Anawatsogolera bwinobwino kotero kuti analibe mantha
koma nyanja inamiza adani awo.
54 Kotero anawafikitsa ku malire a dziko lake loyera,
ku dziko lamapiri limene dzanja lake lamanja linawatengera.
55 Iye anathamangitsa mitundu ya anthu patsogolo pawo
ndipo anapereka mayiko awo kwa Aisraeli kuti akhale awo;
Iye anakhazikitsa mafuko a Israeli mʼnyumba zawo.
9 Kumeneko analowa mʼphanga, nakhala komweko.
Ambuye Aonekera Eliya
Ndipo taonani, Yehova anayankhula naye kuti, “Eliya, ukuchita chiyani kuno?”
10 Iye anayankha kuti, “Ndakhala wodzipereka kwambiri kwa Yehova Mulungu Wamphamvuzonse. Aisraeli asiya pangano lanu, agwetsa maguwa anu ansembe, ndipo apha aneneri anu ndi lupanga. Ndatsala ine ndekha ndipo tsopano akufuna kundipha.”
11 Yehova anati, “Tuluka ndipo ukayime pa phiri pamaso pa Yehova, pakuti Yehova ali pafupi kudutsa pamenepo.”
Tsono mphepo yayikulu ndi yamphamvu inawomba ningʼamba mapiri ndi kuswa matanthwe pamaso pa Yehova, koma Yehova sanali mʼmphepomo. Itapita mphepoyo panachita chivomerezi, koma Yehova sanali mʼchivomerezicho. 12 Chitapita chivomerezicho, panafika moto, koma Yehova sanali mʼmotomo. Ndipo utapita motowo, panamveka kamphepo kayaziyazi. 13 Eliya atamva kamphepoko, anakokera chovala chake naphimba kumutu. Anatuluka ndipo anayima pa khomo la phanga.
Ndipo panamveka mawu akuti, “Eliya, ukuchita chiyani kuno?”
14 Iye anayankha kuti, “Ndakhala wodzipereka kwambiri kwa Yehova Mulungu Wamphamvuzonse. Aisraeli asiya pangano lanu, agwetsa maguwa anu ansembe, ndipo apha aneneri anu ndi lupanga. Ndatsala ine ndekha ndipo tsopano akufuna kundipha.”
15 Yehova anati kwa Eliyayo, “Bwerera njira imene unadzera, ndipo upite ku Chipululu cha ku Damasiko. Ukakafika kumeneko, ukadzoze Hazaeli kuti akhale mfumu ya ku Aramu. 16 Ukadzozenso Yehu mwana wa Nimisi kuti akhale mfumu ya Israeli, ndiponso ukadzoze Elisa mwana wa Safati wa ku Abeli-Mehola kuti akhale mneneri wolowa mʼmalo mwako. 17 Yehu adzapha aliyense amene adzapulumuke ku lupanga la Hazaeli, ndipo Elisa adzapha aliyense amene adzapulumuke ku lupanga la Yehu. 18 Komabe ndasunga anthu 7,000 ku Israeli, anthu onse amene mawondo awo sanagwadirepo Baala, onse amene pakamwa pawo sipanapsompsoneko fano lake.”
Aisraeli Otsala
11 Ine ndikufunsa kuti kodi Mulungu anakana anthu ake? Ayi. Ndi pangʼono pomwe! Inenso ndine Mwisraeli, mmodzi mwa zidzukulu za Abrahamu, ndiponso wa fuko la Benjamini. 2 Mulungu sanawakane anthu ake amene Iye anawadziwiratu. Kodi inu simukudziwa zimene Malemba akunena pa ndime imene Eliya akudandaula kwa Mulungu kuneneza Aisraeli? Iye anati, 3 “Ambuye, anthuwa apha aneneri anu ndi kugwetsa maguwa anu ansembe. Ndatsala ine ndekha wamoyo ndipo akufuna kundipha?” 4 Ndipo yankho la Mulungu linali lotani? “Ine ndadzisungira ndekha anthu 7,000 amene sanapembedzepo Baala.” 5 Chimodzimodzinso lero lino, alipo Aisraeli pangʼono osankhidwa mwachisomo. 6 Ndipo ngati ndi mwachisomo, sikungakhalenso mwa ntchito. Ngati zikanatero, chisomo sichikanakhalanso chisomo ayi.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.