Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 78:17-20

17 Komabe iwowo anapitiriza kumuchimwira Iye,
    kuwukira Wammwambamwamba mʼchipululu.
18 Ananyoza Mulungu mwadala
    pomuwumiriza kuti awapatse chakudya chimene anachilakalaka.
19 Iwo anayankhula motsutsana naye ponena kuti,
    “Kodi Mulungu angatipatse chakudya mʼchipululu?
20 Iye atamenya thanthwe
    madzi anatuluka,
    ndipo mitsinje inadzaza ndi madzi.
Koma iye angatipatsenso ife chakudya?
    Kodi angapereke nyama kwa anthu akewa?”

Masalimo 78:52-55

52 Koma Iye anatulutsa anthu ake ngati ziweto;
    anawatsogolera ngati nkhosa kudutsa mʼchipululu.
53 Anawatsogolera bwinobwino kotero kuti analibe mantha
    koma nyanja inamiza adani awo.
54 Kotero anawafikitsa ku malire a dziko lake loyera,
    ku dziko lamapiri limene dzanja lake lamanja linawatengera.
55 Iye anathamangitsa mitundu ya anthu patsogolo pawo
    ndipo anapereka mayiko awo kwa Aisraeli kuti akhale awo;
    Iye anakhazikitsa mafuko a Israeli mʼnyumba zawo.

Eksodo 33:7-23

Tenti ya Msonkhano

Tsono Mose ankatenga tenti ndi kukayimanga kunja kwa msasa chapatalipo, ndipo ankayitcha “tenti ya msonkhano.” Aliyense wofuna kukafunsa kanthu kwa Yehova amapita ku tenti ya msonkhano kunja kwa msasa. Ndipo nthawi ina iliyonse imene Mose amapita ku tenti anthu onse amanyamuka ndi kuyimirira pa makomo amatenti awo, kumuyangʼana Mose mpaka atalowa mu tentimo. Mose akamalowa mu tenti, chipilala cha mtambo chimatsika ndi kukhala pa khomo pamene Yehova amayankhula ndi Mose. 10 Nthawi zonse anthu akaona chipilala cha mtambo chitayima pa khomo la tentiyo amayimirira ndi kupembedza, aliyense ali pa khomo la tenti yake. 11 Yehova amayankhula ndi Mose maso ndi maso ngati mmene munthu amayankhulira ndi bwenzi lake. Kenaka Mose amabwerera ku msasa koma womuthandiza wake, Yoswa, mwana wa Nuni samachoka pa tentiyo.

Mose ndi Ulemerero wa Yehova

12 Mose anati kwa Yehova, “Inu mwakhala mukundiwuza kuti, ‘Tsogolera anthu awa,’ koma simunandiwuze amene mudzamutuma kuti apite pamodzi nane. Inu mwanena kuti, ‘Ndikukudziwa bwino kwambiri ndipo wapeza chisomo pamaso panga.’ 13 Ngati mwakondwera nane ndiphunzitseni njira zanu kuti ndikudziweni ndi kupitiriza kupeza chisomo pamaso panu. Kumbukirani kuti mtundu uwu ndi anthu anu.”

14 Yehova anayankha kuti, “Ine ndemwe ndidzapita pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakupatsa mpumulo.”

15 Kenaka Mose anati kwa Yehova, “Ngati inu simupita nafe, musatitumize kuti tipite, kutichotsa pano. 16 Kodi wina adzadziwa bwanji kuti inu mwandikomera mtima pamodzi ndi anthu awa ngati simupita nafe? Kodi nʼchiyani chomwe chidzatisiyanitse pakati pa anthu onse amene ali pa dziko lapansi?”

17 Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Ine ndidzachita zimene iwe wandipempha chifukwa Ine ndikukondwera nawe, ndikukudziwa bwino lomwe.”

18 Kenaka Mose anati, “Tsopano ndionetseni ulemerero wanu.”

19 Ndipo Yehova anati, “Ine ndidzakuonetsa ulemerero wanga wonse ndipo ndidzatchula dzina langa lakuti Yehova pamaso pako. Ine ndidzachitira chifundo amene ndikufuna kumuchitira chifundo ndipo ndidzakomera mtima amene ndikufuna kumukomera mtima.” 20 Iye anati, “Koma iwe sungaone nkhope yanga, pakuti palibe munthu amene amaona Ine nakhala ndi moyo.”

21 Ndipo Yehova anati, “Pali malo pafupi ndi ine pomwe ungathe kuyima pa thanthwe. 22 Pamene ulemerero wanga udutsa, ndidzakuyika mʼphanga la thanthwe ndi kukuphimba ndi dzanja langa mpaka nditadutsa. 23 Kenaka ine ndidzachotsa dzanja langa ndipo iwe udzaona msana wanga, koma nkhope yanga sidzaoneka.”

Machitidwe a Atumwi 7:30-34

30 “Ndipo patapita zaka makumi anayi mngelo anaonekera kwa Mose mʼmalawi amoto pa chitsamba mʼchipululu pafupi ndi Phiri la Sinai. 31 Iye ataona zimenezi, anadabwa. Akupita kuti akaonetsetse pafupi, Mose anamva mawu a Ambuye: 32 ‘Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo.’ Mose ananjenjemera chifukwa cha mantha ndipo sanalimbe mtima kuyangʼananso.

33 “Ndipo Ambuye anati kwa Mose, ‘Vula nsapato zako, pakuti malo amene wayimapo ndi opatulika. 34 Ine ndaona ndithu mazunzo a anthu anga amene ali ku Igupto. Ndamva kulira kwawo choncho ndabwera kuti ndiwapulumutse. Tsopano tiye ndikutume ku Igupto.’

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.