Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 119:57-64

Heti

57 Yehova, Inu ndiye gawo langa;
    ndalonjeza kumvera mawu anu.
58 Ndimafunafuna nkhope yanu ndi mtima wanga wonse;
    mundikomere mtima monga mwa lonjezo lanu.
59 Ndinalingalira za njira zanga
    ndipo ndatembenuza mayendedwe anga kutsatira umboni wanu.
60 Ndidzafulumira ndipo sindidzazengereza
    kumvera malamulo anu.
61 Ngakhale oyipa andimange ndi zingwe,
    sindidzayiwala lamulo lanu.
62 Ndimadzuka pakati pa usiku kuyamika Inu
    chifukwa cha malamulo anu olungama.
63 Ine ndine bwenzi la onse amene amakukondani,
    kwa onse amene amatsatira malangizo anu.
64 Dziko lapansi ladzaza ndi chikondi chanu chosasinthika,
    phunzitseni malamulo anu.

Miyambo 3:27-35

27 Usaleke kuchitira zabwino amene ayenera kulandira zabwino,
    pamene uli nazo mphamvu zochitira zimenezi.
28 Usanene kwa mnansi wako kuti,
    “Pita, uchite kubweranso. Ndidzakupatsa mawa”
    pamene uli nazo tsopano.

29 Usamukonzere chiwembu mnansi wako,
    amene anakhala nawe pafupi mokudalira.
30 Usakangane ndi munthu wopanda chifukwa
    pamene iye sanakuchitire zoyipa.

31 Usachite naye nsanje munthu wachiwawa
    kapena kutsanzira khalidwe lake lililonse.
32 Pakuti Yehova amanyansidwa ndi munthu woyipa
    koma amayanjana nawo anthu olungama.

33 Yehova amatemberera nyumba ya munthu woyipa,
    koma amadalitsa nyumba ya anthu olungama.
34 Anthu onyoza, Iye amawanyoza,
    koma amakomera mtima anthu odzichepetsa.
35 Anthu anzeru adzalandira ulemu,
    koma zitsiru adzazichititsa manyazi.

Luka 18:18-30

Munthu Wachuma ndi Ufumu wa Mulungu

18 Oweruza wina wake anamufunsa Iye kuti, “Aphunzitsi abwino, ndichite chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?”

19 Yesu anamuyankha kuti, “Chifukwa chiyani ukunditcha wabwino, palibe wabwino kupatula Mulungu yekha. 20 Iwe umadziwa malamulo: ‘Usachite chigololo, usaphe, usabe, usapereke umboni wonama, lemekeza abambo ndi amayi ako.’ ”

21 Iye anati, “Zonsezi ndinasunga kuyambira ndili mnyamata.”

22 Yesu atamva izi, anati kwa iye, “Ukusowabe chinthu chimodzi: Gulitsa zonse zimene uli nazo ndipo uzipereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Kenaka ubwere, nunditsate ine.”

23 Atamva zimenezi, anakhumudwa kwambiri chifukwa anali munthu wachuma chambiri. 24 Yesu anamuyangʼana nati, “Nʼkwapatali kwambiri kuti anthu achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu! 25 Ndithudi, nʼkwapafupi kuti ngamira idutse pa kabowo ka zingano kusiyana ndi munthu wachuma kulowa mu ufumu wa Mulungu.”

26 Amene anamva izi anafunsa kuti, “Nanga ndani amene angapulumuke?”

27 Yesu anayankha kuti, “Zinthu zosatheka ndi anthu zimatheka ndi Mulungu.”

28 Petro anati kwa Iye, “Ife tinasiya zonse tinali nazo kutsatira Inu!”

29 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti palibe amene anasiya nyumba kapena mkazi kapena abale kapena makolo kapena ana chifukwa cha ufumu wa Mulungu 30 adzalephera kulandira mowirikiza mʼmoyo uno, ndi mʼmoyo ukubwerawo, moyo wosatha.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.