Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
He
33 Yehova, phunzitseni kutsatira zophunzitsa zanu;
ndipo ndidzazisunga mpaka kumapeto.
34 Mundipatse mtima womvetsa zinthu ndipo ndidzasunga malamulo anu
ndi kuwamvera ndi mtima wanga wonse.
35 Munditsogolere mʼnjira ya malamulo anu,
pakuti mʼmenemo ndimapezamo chikondwerero changa.
36 Tembenuzani mtima wanga kuti uzikonda malamulo anu,
osati chuma.
37 Tembenuzani maso anga kuchoka ku zinthu zachabechabe;
sungani moyo wanga monga mwa mawu anu.
38 Kwaniritsani lonjezo lanu kwa mtumiki wanu,
kuti Inu muopedwe.
39 Mundichotsere chipongwe chimene ndikuchiopa,
pakuti malamulo anu ndi abwino.
40 Taonani, ndimalakalakatu malangizo anu!
Sungani moyo wanga mʼchilungamo chanu.
6 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Ngati munthu wina aliyense achimwa, nachita zinthu mosakhulupirika kwa Yehova chifukwa cha kunyenga mnzake pokana kumubwezera zimene anamusungitsa, kapena kumubera kapenanso kumulanda, 3 kapena ndi kunama kuti sanatole chinthu chimene chinatayika, kapena kulumbira mwachinyengo pa chinthu chilichonse chimene munthu akachita amachimwa nacho, 4 ndi wopalamula ndithu, ndipo ayenera kubweza zimene anabazo, zimene analanda mwachinyengozo, zimene anamusungitsazo, zimene anatolazo 5 kapena zimene analumbira monyengazo. Pa tsiku limene apezeke kuti wapalamuladi, iye ayenera kumubwezera mwini wake zinthu zonsezi ndi kuwonjezerapo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse. 6 Pambuyo pake apereke kwa Yehova nsembe yopalamula. Nsembe yake ikhale nkhosa yayimuna yopanda chilema ndipo mtengo wake wogwirizana ndi nsembe yopepesera machimo. 7 Kenaka wansembe achite mwambo wopepesera tchimo la munthuyo pamaso pa Yehova, ndipo adzakhululukidwa chilichonse chomwe anachita kuti akhale wopalamula.”
2 Chonde mvetsetsani! Ine Paulo, ndikukuwuzani kuti mukalola kuchita mdulidwe, Khristu simupindula nayenso konse. 3 Ndikubwerezanso kuwuza munthu aliyense wovomereza kuchita mdulidwe kuti ayeneranso kutsata Malamulo onse. 4 Inu amene mukufuna kulungamitsidwa ndi lamulo mwachotsedwa mwa Khristu; munagwa kusiyana nacho chisomo. 5 Koma mwachikhulupiriro, ife tikudikira mwachidwi kudzera mwa Mzimu, chilungamo chimene tikuyembekeza. 6 Pakuti mwa Khristu Yesu mdulidwe kapena kusachita mdulidwe zilibe phindu. Chinthu chokhacho chimene chimafunika ndi chikhulupiriro chogwira ntchito mwachikondi.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.