Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
He
33 Yehova, phunzitseni kutsatira zophunzitsa zanu;
ndipo ndidzazisunga mpaka kumapeto.
34 Mundipatse mtima womvetsa zinthu ndipo ndidzasunga malamulo anu
ndi kuwamvera ndi mtima wanga wonse.
35 Munditsogolere mʼnjira ya malamulo anu,
pakuti mʼmenemo ndimapezamo chikondwerero changa.
36 Tembenuzani mtima wanga kuti uzikonda malamulo anu,
osati chuma.
37 Tembenuzani maso anga kuchoka ku zinthu zachabechabe;
sungani moyo wanga monga mwa mawu anu.
38 Kwaniritsani lonjezo lanu kwa mtumiki wanu,
kuti Inu muopedwe.
39 Mundichotsere chipongwe chimene ndikuchiopa,
pakuti malamulo anu ndi abwino.
40 Taonani, ndimalakalakatu malangizo anu!
Sungani moyo wanga mʼchilungamo chanu.
21 “Musazunze mlendo kapena kumuchitira nkhanza, pakuti inu munali alendo mʼdziko la Igupto.
22 “Musazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye. 23 Ngati muwazunza ndipo iwo nʼkulirira kwa Ine, ndidzamva kulira kwawo. 24 Ine ndidzakukwiyirani ndipo ndidzakuphani ndi lupanga. Akazi anu adzakhala amasiye ndiponso ana anu adzakhala wopanda abambo.
25 “Ngati mukongoza ndalama kwa mʼbale wanu amene ndi mʼmphawi pakati panu, musadzamuchite monga zimene amachita wokongoza ndalama. Musadzamuyikire chiwongoladzanja. 26 Mukatenga chovala cha mnzanu kuti chikhale chikole mumubwezere dzuwa lisanalowe 27 chifukwa chovala chimene amadzifundira nacho nʼchomwecho. Nanga usiku adzafunda chiyani? Tsonotu ngati adzandilirira, Ine ndidzamva pakuti ndine wachifundo.
Ufulu wa Munthu Wokhulupirira
23 Mutha kunena kuti, “Zinthu zonse nʼzololedwa,” komatu si zonse zili za phindu. “Zinthu zonse nʼzololedwa,” komatu si zonse zimathandiza. 24 Munthu aliyense asafunefune zokomera iye yekha, koma zokomeranso ena.
25 Idyani nyama iliyonse imene amagulitsa pa msika, osafunsa mafunso okhudzana ndi chikumbumtima chanu. 26 Popeza kuti, “Dziko lapansi ndi la Ambuye ndi zonse za mʼmenemo ndi zake.”
27 Ngati wosakhulupirira akuyitanani kuti mukadye naye, inuyo ndi kuvomera kupitako, mukadye chilichonse chimene akakupatseni ndipo musakafunse mafunso okhudzana ndi chikumbumtima chanu. 28 Koma ngati wina akuwuzani kuti, “Izi zaperekedwa nsembe,” musadye zimenezo, pofuna kuthandiza amene wakuwuzaniyo komanso chifukwa cha chikumbumtima. 29 Ndikunena za chikumbumtima cha winayo osati chanu. Tsono mungafunse kuti, nʼchifukwa chiyani ufulu wanga ukuphwanyidwa chifukwa cha chikumbumtima cha munthu wina? 30 Ngati ndikuyamika Mulungu chifukwa cha chakudya, nanga munthu angandinyoze bwanji pa zinthu zomwe ndayamikira nazo Mulungu?
31 Nʼchifukwa chake chilichonse mungadye kapena kumwa, kapena chimene mungachite, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu. 32 Musakhumudwitse aliyense, kaya ndi Myuda, Mgriki, kapena mpingo wa Mulungu. 33 Mu zonse ndikuyesetsa kukondweretsa aliyense mʼnjira iliyonse. Popeza sindikufunafuna zokondweretsa ine ndekha koma zokomera ambiri kuti apulumutsidwe.
11 Tsatirani chitsanzo changa, monga inenso nditsatira chitsanzo cha Khristu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.