Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 119:9-16

Beti

Kodi mnyamata angathe bwanji kuyeretsa mayendedwe ake?
    Akawasamala potsata mawu anu.
10 Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse;
    musalole kuti ndisochere kuchoka pa malamulo anu.
11 Ndasunga mawu anu mu mtima mwanga
    kuti ndisakuchimwireni.
12 Mutamandike Inu Yehova;
    phunzitseni malamulo anu.
13 Ndi milomo yanga ndimafotokoza malamulo anu onse
    amene amachokera pakamwa panu.
14 Ndimakondwera potsatira malamulo anu
    monga momwe munthu amakondwera akakhala ndi chuma chambiri.
15 Ndimalingalira malangizo anu
    ndipo ndimaganizira njira zanu.
16 Ndimakondwera ndi malamulo anu;
    sindidzayiwala konse mawu anu.

Deuteronomo 23:21-24:4

21 Mukalumbira kupereka kanthu kwa Yehova Mulungu wanu, musamachedwetse kupereka, chifukwa Yehova Mulungu wanu adzakufunsanibe kanthuko ndipo mudzapezeka wochimwa. 22 Koma ngati mupewa kupanga mapangano simudzapezeka ochimwa. 23 Zilizonse zimene mulumbira ndi pakamwa panu muzitsimikiza kuzichita, chifukwa mwalumbira mwaufulu pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi pakamwa panu.

24 Mukalowa mʼmunda wamphesa wa mnzanu mukhoza kudya mphesa mmene mungafunire koma musayike zina mʼdengu mwanu. 25 Mukalowa mʼmunda wa tirigu wa mʼbale wanu, mukhoza kutengako ngala mʼmanja mwanu, koma osasenga tirigu ndi chikwakwa.

24 Ngati mwamuna wakwatira mkazi amene sakukondwera naye chifukwa wapeza vuto pa mkaziyo, namulembera mkaziyo kalata ya chisudzulo, namupatsa ndi kumutulutsa mʼnyumba mwake, mkaziyo ndi kukakwatiwa ndi mwamuna wina, ndipo mwamuna wachiwiriyo nʼkuyipidwa nayenso ndi kumulemberanso kalata ya chisudzulo nʼkumutulutsa mʼnyumba mwake, kapena ngati mwamunayo amwalira, mwamuna wake woyamba uja, amene anamuleka saloledwanso kumukwatira kachiwiri popeza mkaziyo wadetsedwa. Chimenechi ndi chonyansa pamaso pa Yehova. Musalowetse tchimo mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu.

Deuteronomo 24:10-15

10 Ukabwereketsa mnzako kanthu kena kalikonse, usalowe mʼnyumba mwake kukatenga chimene wachipereka ngati chikole. 11 Uziyima kunja kwa nyumba kuti munthu amene wamubwereketsa kanthuyo akubweretsere kunja komweko. 12 Ngati munthuyo ndi wosauka, usamutengere chikolecho mpaka kukagona nacho kwanu. 13 Pomalowa dzuwa ukhale utamubwezera mkanjo wakewo kuti akafunde. Pamenepo adzakuthokoza, ndipo amenewa adzawerengedwa ngati machitidwe olungama kwa iweyo pamaso pa Yehova Mulungu wako.

14 Osamapezera mwayi pa anthu aganyu osauka ndi aumphawi, kaya ndi Mwisraeli kapena mlendo wokhala mu umodzi mwa mizinda yanu. 15 Mumulipire malipiro ake a tsiku dzuwa lisanalowe chifukwa ndi wosauka ndipo akudalira malipirowo. Kupanda kutero adzakudandaulirani kwa Yehova ndipo mudzapezeka ochimwa.

Yakobo 2:1-13

Kuchita Tsankho Nʼkosaloledwa

Abale anga, okhulupirira Yesu Khristu waulemerero, musaonetse tsankho. Tangoganizirani, pakati panu patabwera munthu atavala mphete yagolide ndi zovala zapamwamba, ndipo winanso wosauka nʼkulowa atavala sanza. Ngati musamala kwambiri munthu wovala bwinoyu uja, nʼkumuwuza kuti, “Khalani pa mpando wabwinowu,” koma wosauka uja nʼkumuwuza kuti, “Ima apo,” kapena “Khala pansi pafupi ndi chopondapo mapazi angawa,” kodi simunachite tsankho pakati panu ndi kukhala oweruza a maganizo oyipa?

Tamverani abale anga okondedwa, kodi Mulungu sanasankhe amene dziko lapansi limawaona ngati amphawi kuti akhale olemera mʼchikhulupiriro ndi kulowa ufumu umene Iye analonjeza kwa amene amamukonda? Koma mwakhala mukunyoza amphawi. Kodi si anthu olemerawa amene akukudyerani masuku pamutu? Si anthu amenewa amene amakukokerani ku bwalo la milandu? Kodi si omwewa amene amachita chipongwe dzina la wolemekezeka, limene inu mumatchulidwa?

Ngati musungadi lamulo laufumu lija lopezeka mʼMalemba lakuti, “Konda mnansi wako monga iwe mwini,” ndiye kuti mukuchita bwino. Koma mukamaonetsa tsankho mukuchimwa, ndipo ndinu wochimwa monga wophwanya lamulo. 10 Pakuti amene amasunga Malamulo onse, akangophwanya fundo imodzi yokha, waphwanya Malamulo onse. 11 Pakuti amene anati “Usachite chigololo” ndi yemweyonso anati “Usaphe.” Ngati suchita chigololo koma umapha, ndiwe wophwanya Malamulo.

12 Muziyankhula ndi kuchita zinthu monga anthu amene mudzaweruzidwe ndi lamulo limene limapereka ufulu, 13 chifukwa munthu woweruza mopanda chifundo, nayenso adzaweruzidwa mopanda chifundo. Chifundo chimapambana pa chiweruzo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.