Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Alefu
119 Odala ndi amene moyo wawo ulibe cholakwa,
amene amayenda monga mwa malamulo a Yehova.
2 Odala ndi amene amasunga malamulo ake,
amene amafunafuna Iyeyo ndi mtima wawo wonse.
3 Sachita cholakwa chilichonse;
amayenda mʼnjira zake.
4 Inu mwapereka malangizo
ndipo ayenera kutsatidwa kwathunthu.
5 Aa! Ndikanakonda njira zanga zikanakhala zokhazikika
pa kumvera zophunzitsa zanu!
6 Pamenepo ine sindikanachititsidwa manyazi,
poganizira malamulo anu onse.
7 Ndidzakutamandani ndi mtima wolungama,
pamene ndikuphunzira malamulo anu olungama.
8 Ndidzamvera zophunzitsa zanu;
musanditaye kwathunthu.
34 Nthawi imeneyo nthaka idzasangalalira kuyipumitsa kwake nthawi yonse imene idzakhala yosalimidwa, pamene inu mudzakhala muli mʼdziko la adani anu. Pa nthawi imeneyo dziko lidzapumula ndi kukondwerera kulipumuza kwake. 35 Nthawi zonse pamene dzikolo lidzakhala lopanda anthu, nthaka idzapumula. Mpumulo umenewu udzakhala umene nthakayo sinapumulepo pa nthawi zimene inu munkapumula muli mʼdzikomo.
36 “ ‘Kunena za amene adzatsale, ndidzayika mantha mʼmitima mwawo mʼdziko la adani awo kotero kuti adzathawa ngakhale mtswatswa wa tsamba lowuluka ndi mphepo. Adzathawa ngati akuthawa lupanga, ndipo adzagwa pansi ngakhale padzakhale wopanda kuwapirikitsa. 37 Iwo adzaphunthwitsana ngati akuthawa nkhondo, ngakhale padzakhale popanda wowapirikitsa. Choncho simudzatha kuyima pamaso pa adani anu. 38 Mudzatheratu pakati pa mitundu ya anthu. Dziko la adani anu lidzakudyani. 39 Ngakhale iwo amene adzatsale adzatheratu mʼdziko la adani awo chifukwa cha machimo awo ndi machimo a makolo awo.
40 “ ‘Tsono adzawulula machimo awo ndi machimo a makolo awo, kusakhulupirika kwawo ndi mayendedwe awo otsutsana nane, 41 zomwe zinandipangitsa kuwafulatira ndi kuwapereka mʼmanja mwa adani awo. Ndipo mitima yawo yowumayo ikadzadzichepetsa ndi kuvomera kulangidwa chifukwa cha machimo awo, 42 Ine ndidzakumbukira pangano langa ndi Yakobo, pangano langa ndi Isake, pangano langa ndi Abrahamu. Ndidzakumbukiranso dzikolo. 43 Pakuti adzasiya dziko lawo lopanda anthu, nthaka idzakondwerera zaka zake zoyipumuza pamene iwo kudzakhala kulibe. Koma adzalangidwa chifukwa cha machimo awo popeza anakana malamulo anga ndipo mitima yawo inkayipidwa nawo malangizo anga. 44 Komabe ngakhale adzachite zonsezi ali mʼdziko la adani awo, Ine sindidzawakana kapena kuyipidwa nawo kwakuti nʼkuwawononga kwathunthu ndi kuthetsa pangano langa ndi iwo. Ine ndine Yehova Mulungu wawo. 45 Koma powachitira chifundo, ndidzakumbukira pangano langa ndi makolo awo amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto mitundu ina ikuona kuti Ine ndikhale Mulungu wawo. Ine ndine Yehova.’ ”
46 Amenewa ndi malamulo ndi malangizo amene Yehova anawayika pakati pa Iye mwini ndi Aisraeli pa Phiri la Sinai kudzera mwa Mose.
7 Okondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano koma lakale lomwe lija, limene munali nalo kuyambira pachiyambi. Lamulo la kalelo ndi mawu amene munawamva kale. 8 Komabe ndi lamulo latsopano limene ndikukulemberani. Choonadi chake chikuoneka mwa Yesu ndiponso mwa inu, chifukwa mdima ukutha ndipo kuwunika kwenikweni kwayamba kale kuwala.
9 Aliyense amene amati ali mʼkuwunika, koma nʼkumadana ndi mʼbale wake ali mu mdima. 10 Aliyense amene amakonda mʼbale wake amakhalanso mʼkuwunika, ndipo mwa iye mulibe chokhumudwitsa. 11 Koma aliyense wodana ndi mʼbale wake ali mu mdima ndipo akuyenda mu mdima. Iyeyo sakudziwa kumene akupita, chifukwa mdima wamudetsa mʼmaso mwake.
12 Inu ana okondedwa, ndikukulemberani
popeza kuti machimo anu akhululukidwa chifukwa cha dzina la Yesu.
13 Inu abambo, ndikukulemberani
popeza kuti munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi.
Inu anyamata, ndikukulemberani
popeza kuti munagonjetsa woyipayo.
14 Ana okondedwa, ndikukulemberani
chifukwa mumawadziwa Atate.
Abambo, ndikukulemberani
chifukwa munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi.
Inu anyamata, ndikukulemberani
chifukwa ndinu amphamvu.
Mawu a Mulungu amakhala mwa inu
ndipo mumamugonjetsa woyipayo.
Musakonde Dziko Lapansi
15 Musamakonde dziko lapansi kapena chilichonse cha dziko lapansi. Ngati munthu wina aliyense akonda dziko lapansi, mwa iyeyo mulibe chikondi chokonda Atate. 16 Pakuti zonse za mʼdziko lapansi, zilakolako za thupi, zinthu zimene maso amakhumbira ndiponso kuyandikira zinthu za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi. 17 Dziko lapansi likupita pamodzi ndi zilakolako zake, koma amene amachita chifuniro cha Mulungu amakhalapo mpaka muyaya.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.