Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 119:1-8

Alefu

119 Odala ndi amene moyo wawo ulibe cholakwa,
    amene amayenda monga mwa malamulo a Yehova.
Odala ndi amene amasunga malamulo ake,
    amene amafunafuna Iyeyo ndi mtima wawo wonse.
Sachita cholakwa chilichonse;
    amayenda mʼnjira zake.
Inu mwapereka malangizo
    ndipo ayenera kutsatidwa kwathunthu.
Aa! Ndikanakonda njira zanga zikanakhala zokhazikika
    pa kumvera zophunzitsa zanu!
Pamenepo ine sindikanachititsidwa manyazi,
    poganizira malamulo anu onse.
Ndidzakutamandani ndi mtima wolungama,
    pamene ndikuphunzira malamulo anu olungama.
Ndidzamvera zophunzitsa zanu;
    musanditaye kwathunthu.

Genesis 26:1-5

Isake ndi Abimeleki

26 Tsono kunagwa njala ina mʼdzikomo kuwonjezera pa ija ya poyamba ya nthawi ya Abrahamu ndipo Isake anapita kwa Abimeleki mfumu ya Afilisti ku Gerari. Yehova anadza kwa Isake nati, “Usapite ku Igupto; koma ukhale mʼdziko limene ndidzakuwuza kuti ukakhalemo. Khala mʼdziko lino ndipo ndidzakhala nawe ndi kukudalitsa. Pakuti kwa iwe ndi zidzukulu zako ndidzapereka mayiko onsewa. Choncho ndidzakwaniritsa pangano limene ndinalumbira kwa Abrahamu, abambo ako. Zidzukulu zako ndidzazichulukitsa ngati nyenyezi za mu mlengalenga ndi kuzipatsa mayiko onsewa. Ndiponso anthu onse a pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa zidzukulu zako, chifukwa Abrahamu anandimvera, nasunga malamulo anga onse.”

Yakobo 1:12-16

12 Wodala ndi munthu amene amapirira mʼmayesero, chifukwa akapambana adzalandira chipewa cha ulemerero chimene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda.

13 Munthu akayesedwa asanene kuti, “Mulungu akundiyesa.” Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi choyipa kapena Iyeyo kuyesa munthu aliyense. 14 Koma munthu aliyense amayesedwa akakokedwa ndi zilakolako zake zoyipa ndi kukopedwa nazo. 15 Pamenepo, chilakolako chikakula chimabala tchimo; ndipo tchimo likakhwima limabereka imfa.

16 Musanyengedwe abale anga okondedwa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.