Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 119:105-112

Nuni

105 Mawu anu ndi nyale ya kumapazi kwanga
    ndi kuwunika kwa pa njira yanga.
106 Ndalumbira ndipo ndatsimikiza,
    kuti ndidzatsatira malamulo anu olungama.
107 Ndazunzika kwambiri;
    Inu Yehova, sungani moyo wanga molingana ndi mawu anu.
108 Inu Yehova, landirani matamando aufulu ochokera pakamwa panga,
    ndipo ndiphunzitseni malamulo anu.
109 Ngakhale moyo wanga umakhala mʼzoopsa nthawi ndi nthawi,
    sindidzayiwala malamulo anu.
110 Anthu oyipa anditchera msampha,
    koma sindinasochere kuchoka pa malangizo anu.
111 Umboni wanu ndiye cholowa changa kwamuyaya;
    Iwo ndiye chimwemwe cha mtima wanga.
112 Mtima wanga wakhazikika pa kusunga zophunzitsa zanu
    mpaka kumapeto kwenikweni.

Miyambo 6:6-23

Pita kwa nyerere, mlesi iwe;
    kaonetsetse njira zake kuti uphunzirepo kanthu!
Zilibe mfumu,
    zilibe woyangʼanira kapena wolamulira,
komabe zimasungiratu chakudya chake nthawi ya chilimwe
    ndipo zimatuta chakudyacho nthawi yokolola.

Kodi uzingogonabe pamenepo mpaka liti mlesi iwe?
    Kodi tulo tako tidzatha liti?
10 Ukati ndingogona pangʼono, ndingowodzera pangʼono
    ndingopinda manjawa pangʼono kuti ndipumule,
11 umphawi udzakugwira ngati mbala
    ndipo usiwa udzafika ngati munthu wachifwamba.

12 Munthu wachabechabe, munthu woyipa,
    amangoyendayenda ndi kumayankhula zoyipa,
13     amatsinzinira maso ake,
    namakwakwaza mapazi ake
    ndi kulozaloza ndi zala zake,
14     amalingalira zoyipa ndi mtima wake wachinyengo
    ndipo nthawi zonse amangokhalira kuyambitsa mikangano pakati pa anthu.
15 Nʼchifukwa chake tsoka lidzamugwera modzidzimutsa;
    adzawonongeka msangamsanga popanda chomupulumutsa.

16 Pali zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Yehova amadana nazo,
    zinthu zisanu ndi ziwiri zimene zimamunyansa:
17         maso onyada,
        pakamwa pabodza,
        manja akupha munthu wosalakwa,
18         mtima wokonzekera kuchita zoyipa,
        mapazi othamangira msanga ku zoyipa,
19         mboni yonama yoyankhula mabodza
        komanso munthu amene amayambitsa mikangano pakati pa abale.

Chenjezo pa za Chigololo

20 Mwana wanga, usunge malamulo a abambo ako;
    ndipo usataye zimene anakuphunzitsa amayi ako.
21 Zimenezi uzimatirire pa mtima pako masiku onse,
    uzimangirire mʼkhosi mwako.
22 Ukamayenda, zidzakulozera njira;
    ukugona, zidzakulondera;
    ukudzuka, zidzakuyankhula.
23 Paja malamulo awa ali ngati nyale,
    malangizowa ali ngati kuwunika,
ndipo chidzudzulo cha mwambo ndiwo
    moyo weniweni,

Yohane 8:12-30

Za Umboni wa Yesu

12 Yesu atayankhulanso kwa anthu, anati, “Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi. Aliyense amene anditsata Ine sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuwala kotsogolera anthu ku moyo.”

13 Afarisi anamutsutsa Iye nati, “Iwe ukudzichitira umboni wa Iwe mwini, umboni wako siwoona.”

14 Yesu anayankha kuti, “Ngakhale Ine ndidzichitire umboni, umboni wangawu ndi woona, pakuti Ine ndikudziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndikupita. Koma inu simukudziwa ndi pangʼono pomwe kumene ndinachokera kapena kumene ndikupita. 15 Inu mumaweruza potsata maganizo a anthu chabe. Ine sindiweruza munthu wina aliyense. 16 Koma Ine ndikati ndiweruze, ndimaweruza molondola, chifukwa Ine sindili ndekha koma ndili ndi Atate amene anandituma. 17 Mʼmalamulo anu munalembedwa kuti umboni wa anthu awiri ndi wovomerezeka. 18 Ine ndikudzichitira ndekha umboni; ndipo mboni inanso ndi Atate amene anandituma.”

19 Kenaka iwo anamufunsa Iye kuti, “Kodi Atate anuwo ali kuti?”

Yesu anayankha kuti, “Inu simundidziwa Ine. Atate anganso simuwadziwa. Mukanandidziwa Ine, mukanawadziwanso Atate anga.” 20 Iye anayankhula mawu awa pamene amaphunzitsa Nyumba ya Mulungu pafupi ndi malo amene amaponyapo zopereka. Komabe palibe amene anamugwira Iye, chifukwa nthawi yake inali isanakwane.

Mkangano Woti Yesu Ndani

21 Kenakanso Yesu anawawuza kuti, “Ine ndikupita, ndipo mudzandifunafuna, koma mudzafa muli mʼmachimo anu. Kumene ndikupita, inu simungabwereko.”

22 Izi zinachititsa Ayuda kufunsa kuti, “Kodi adzadzipha yekha? Kodi ndicho chifukwa chake akuti, ‘Kumene ndikupita, inu simungabwereko?’ ”

23 Koma Iye anapitiriza kuti, “Inu ndi ochokera pansi pano. Ine ndine wochokera kumwamba. Inu ndinu anthu a dziko la pansi. Ine sindine wa dziko lapansi lino. 24 Ine ndinakuwuzani kuti mudzafera mʼmachimo anu ngati simukhulupirira kuti Ine Ndine. Ndithu inu mudzafera mʼmachimo anu.”

25 Iwo anafunsa kuti, “Ndinu ndani?”

Yesu anayankha kuti, “Monga Ine ndakhala ndikunena nthawi yonseyi, 26 ndili ndi zambiri zoti ndinene zoweruza inu. Koma Iye amene anandituma ndi woona, ndipo chimene Ine ndamva kuchokera kwa Iye, ndi chimene ndimaliwuza dziko lapansi.”

27 Iwo sanazindikire kuti Iye amawawuza za Atate ake. 28 Choncho Yesu anati, “Inu mukadzapachika Mwana wa Munthu, pamenepo mudzadziwa kuti Ine Ndine. Mudzadziwa kuti sindichita kalikonse pa Ine ndekha koma ndimayankhula zokhazo zimene Atate anandiphunzitsa. 29 Iye amene anandituma Ine ali nane pamodzi. Iye sanandisiye ndekha popeza nthawi zonse ndimachita zomwe zimamukondweretsa Iye.” 30 Pamene Iye ankayankhula zimenezi, ambiri anamukhulupirira.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.