Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Nuni
105 Mawu anu ndi nyale ya kumapazi kwanga
ndi kuwunika kwa pa njira yanga.
106 Ndalumbira ndipo ndatsimikiza,
kuti ndidzatsatira malamulo anu olungama.
107 Ndazunzika kwambiri;
Inu Yehova, sungani moyo wanga molingana ndi mawu anu.
108 Inu Yehova, landirani matamando aufulu ochokera pakamwa panga,
ndipo ndiphunzitseni malamulo anu.
109 Ngakhale moyo wanga umakhala mʼzoopsa nthawi ndi nthawi,
sindidzayiwala malamulo anu.
110 Anthu oyipa anditchera msampha,
koma sindinasochere kuchoka pa malangizo anu.
111 Umboni wanu ndiye cholowa changa kwamuyaya;
Iwo ndiye chimwemwe cha mtima wanga.
112 Mtima wanga wakhazikika pa kusunga zophunzitsa zanu
mpaka kumapeto kwenikweni.
3 Mʼchaka cha 18 cha ufumu wake, Mfumu Yosiya anatuma mlembi wa nyumba ya mfumu, Safani, mwana wa Azariya, mwana wa Mesulamu, ku Nyumba ya Yehova. Iye anati, 4 “Pita kwa mkulu wa ansembe Hilikiya ndipo ukamuwuze kuti awerenge ndalama zimene anthu abwera nazo ku Nyumba ya Yehova, zimene alonda a pa khomo anasonkhanitsa kwa anthu. 5 Ndalamazo azipereke kwa anthu amene asankhidwa kuti ayangʼanire ntchito ya Nyumba ya Yehova. Ndipo anthu amenewa azilipira antchito amene akukonzanso Nyumba ya Yehova, 6 amisiri a matabwa, amisiri omanga ndi amisiri a miyala. Iwo akagulenso matabwa ndi miyala yosemedwa kuti akonzere Nyumba ya Yehova. 7 Koma anthu amene apatsidwa ndalama zolipira antchito okonza Nyumbayo asawafunse za kagwiritsidwe ntchito ka ndalamazo, popeza ndi anthu wokhulupirika.”
8 Mkulu wa ansembe Hilikiya anawuza Safani, mlembiyo kuti, “Ndapeza Buku la Malamulo mʼNyumba ya Yehova.” Anapereka bukulo kwa Safani amene analiwerenga. 9 Ndipo Safani mlembi uja, anapita nakafotokozera mfumu kuti, “Atumiki anu apereka ndalama zija zinali mʼNyumba ya Yehova kwa anthu amene akugwira ntchito ndi kuyangʼanira ntchito yokonza Nyumba ya Yehova.” 10 Kenaka Safani mlembiyo, anafotokozera mfumu kuti, “Wansembe Hilikiya wandipatsa buku.” Ndipo Safani analiwerenga pamaso pa mfumu.
11 Mfumu itamva mawu a mʼBuku la Malamulo, inangʼamba zovala zake. 12 Iyo inalamula wansembe Hilikiya, Ahikamu mwana wa Safani, Akibo mwana wa Mikaya, Safani mlembi uja ndi Asaiya mtumiki wa mfumu, kuti, 13 “Pitani mukafunse Yehova mʼmalo mwanga ndi mʼmalo mwa anthu onse a mʼdziko la Yuda, za zomwe zalembedwa mʼbuku limene lapezekali. Mkwiyo wa Yehova ndi waukulu kwambiri pa ife ndipo watiyakira chifukwa makolo athu sanamvere mawu a buku ili. Iwo sanachite molingana ndi zonse zimene zalembedwa mʼmenemu zokhudza ife.”
14 Choncho Hilikiya wansembe, Ahikamu, Akibo, Safani ndi Asaiya anapita kukayankhula ndi Hulida, mneneri wamkazi, mkazi wa Salumu mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi, wosunga zovala zaufumu. Mneneri wamkaziyu ankakhala mu Yerusalemu, ku chigawo chachiwiri cha mzindawo.
15 Ndipo iye anawawuza kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti: Kamuwuzeni munthu amene wakutumani kwa ine kuti, 16 ‘Ichi ndi chimene Yehova akunena: Taonani, ndidzabweretsa mavuto pa malo ano ndi pa anthu ake, molingana ndi zonse zimene zalembedwa mʼbuku limene mfumu ya Yuda yawerenga. 17 Chifukwa anthuwo andisiya Ine ndi kumafukiza lubani kwa milungu ina nandikwiyitsa ndi mafano onse amene manja awo anapanga, mkwiyo wanga udzayaka pa malo ano ndipo sudzazimitsidwa.’ 18 Koma mfumu ya Yuda imene inakutumani kuti mudzafunse kwa Yehova kayiwuzeni kuti, ‘Ichi ndi chimene Yehova Mulungu wa Israeli akunena molingana ndi mawu amene unamva: 19 Chifukwa unasweka mtima ndi kudzichepetsa wekha pamaso pa Yehova, pamene unamva zomwe zinayankhulidwa zotsutsana ndi malo ano ndi anthu ake, kuti adzakhala otembereredwa nasanduka bwinja, ndiponso chifukwa unangʼamba zovala ndi kulira pamaso panga, ndamva pemphero lako, akutero Yehova. 20 Choncho taona, Ine ndidzakutenga kupita kwa makolo ako ndipo udzayikidwa mʼmanda mwako mwamtendere. Maso ako sadzaona mavuto onse amene ndidzabweretse pamalo pano.’ ”
Ndipo anthu aja anabwerera nakafotokoza mawu amenewa kwa mfumu.
2 Mulungu sanawakane anthu ake amene Iye anawadziwiratu. Kodi inu simukudziwa zimene Malemba akunena pa ndime imene Eliya akudandaula kwa Mulungu kuneneza Aisraeli? Iye anati, 3 “Ambuye, anthuwa apha aneneri anu ndi kugwetsa maguwa anu ansembe. Ndatsala ine ndekha wamoyo ndipo akufuna kundipha?” 4 Ndipo yankho la Mulungu linali lotani? “Ine ndadzisungira ndekha anthu 7,000 amene sanapembedzepo Baala.” 5 Chimodzimodzinso lero lino, alipo Aisraeli pangʼono osankhidwa mwachisomo. 6 Ndipo ngati ndi mwachisomo, sikungakhalenso mwa ntchito. Ngati zikanatero, chisomo sichikanakhalanso chisomo ayi.
7 Nʼchiyani tsopano? Chimene Aisraeli anachifuna ndi mtima wonse sanachipeze koma osankhidwawo anachipeza. Enawo anawumitsidwa mtima 8 monga kwalembedwa kuti,
“Mulungu anawapatsa mzimu wosatha kumvetsa zinthu,
maso osatha kupenya;
makutu osatha kumva
mpaka lero lino.”
9 Ndipo Davide akuti,
“Maphwando awo asanduke msampha ndi diwa lowakola
ndi chopunthwitsa kuti alandire chilango.
10 Maso awo atsekedwe kuti asaone,
ndi misana yawo ikhale yokhota nthawi zonse.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.