Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yesaya 58:1-9

Kusala Kwenikweni

58 “Fuwula kwambiri, usaleke.
    Mawu ako amveke ngati lipenga.
Uwawuze anthu anga za kulakwa kwawo;
    uwuze nyumba ya Yakobo za machimo awo.
Pakuti tsiku ndi tsiku amafunafuna Ine;
    amaoneka ngati a chidwi chofuna kudziwa zimene ndimafuna,
kukhala ngati kuti ndi dziko limene limachita zolondola
    ndipo silinasiye zolamulira za Mulungu wake.
Amandipempha kuti ndigamule mlandu wawo mwachilungamo
    ndipo amaonetsa chidwi chofuna kukhala pafupi ndi Mulungu.
Anthu akufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani ife tasala
    kudya pamene Inu simukulabadirapo?
Kodi ife tavutikiranji nʼkudzichepetsa
    pamene Inu simunasamalepo?’ ”

Yehova akuti, “Komatu tsiku lanu losala kudya, mumachita zinthu zokukondweretsani,
    ndipo mumazunza antchito anu onse.
Mumati uku mukusala kudya, uku mukukangana ndi kumenyana,
    mpaka kumenyana ndi nkhonya zopweteka.
Kusala kudya mukuchitiramu musayembekezere kuti mawu anu amveka kumwamba.
Kodi kusala kudya kumene ndimakufuna Ine nʼkumeneku,
    kungokhala tsiku loti munthu adzichepetse basi?
Kodi ndi tsiku loti munthu angowerama pansi ngati bango
    ndi kumayala ziguduli nʼkuthirapo phulusa nʼkugonapo?
Kodi ndiye mumati kusala kudya kumeneko,
    tsiku lokondweretsa Yehova?

“Kodi si uku kusala kudya kumene Ine ndimakufuna:
Kumasula maunyolo ozunzizira anthu
    ndi kumasula zingwe za goli,
kupereka ufulu kwa oponderezedwa
    ndi kuphwanya goli lililonse?
Anthu anjala kodi mwawagawira chakudya chanu?
    Osowa ndi ongoyendayenda,
kodi mwawapatsa malo ogona?
    Munthu wausiwa kodi mwamupatsa chovala?
Mukatero chipulumutso chanu chidzabwera ngati mʼbandakucha,
    ndipo mabala anu adzachira msangamsanga;
chilungamo chanu chidzakutsogolerani
    ndipo ulemerero wa Yehova udzakhala chokutchinjirizani kumbuyo kwanu.
Mukamadzapemphera Yehova adzakuyankhani;
    mukadzapempha thandizo, Iye adzati: Ine ndili pano.

“Ngati muleka kuzunza anzanu,
    ngati musiya kuloza chala ndiponso kunena zoyipa za anzanu.

Yesaya 58:9-12

Mukamadzapemphera Yehova adzakuyankhani;
    mukadzapempha thandizo, Iye adzati: Ine ndili pano.

“Ngati muleka kuzunza anzanu,
    ngati musiya kuloza chala ndiponso kunena zoyipa za anzanu.
10 Ndipo ngati mudyetsa anthu anjala,
    ndi kuthandiza anthu oponderezedwa,
pamenepo kuwala kwanu kudzaonekera mu mdima,
    ndipo usiku wanu udzakhala ngati usana.
11 Yehova adzakutsogolerani nthawi zonse;
    adzakwaniritsa zosowa zanu mʼdziko longʼalukangʼaluka dzuwa
    ndipo adzalimbitsa matupi anu.
Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri,
    ngati kasupe amene madzi ake saphwa.
12 Anthu ako adzamanganso nyumba zimene zakhala mabwinja nthawi yayitali,
    ndipo adzamanganso pa maziko akalekale;
inu mudzatchedwa okonza makoma opasuka.
    Anthu okonza misewu ndi nyumba zake.

Masalimo 112:1-9

112 Tamandani Yehova.

Wodala munthu amene amaopa Yehova,
    amene amakondwera kwambiri ndi malamulo ake.

Ana ake adzakhala amphamvu mʼdziko;
    mʼbado wa olungama mtima udzadalitsidwa.
Kulemera ndi chuma zili mʼnyumba yake,
    ndipo chilungamo chake ndi chosatha.
Ngakhale mu mdima kuwala kumatulukira olungama mtima;
    wokoma mtima, wachifundo ndi wowongoka mtima.
Zinthu zabwino zidzabwera kwa iye amene amapereka mowolowamanja ndi wokongoletsa mwaufulu,
    amene amachita ntchito yake mwachilungamo.

Ndithu sadzagwedezeka;
    munthu wolungama sadzayiwalika mpaka muyaya.
Saopa akamva zoyipa zimene zachitika;
    mtima wake ndi wokhazikika ndipo amadalira Yehova.
Mtima wake ndi wotetezedwa, sadzakhala ndi mantha;
    potsiriza pake adzayangʼana adani ake mwachipambano.
Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka,
    chilungamo chake chimanka mpaka muyaya;
    nyanga yake idzakwezedwa mwaulemu.

Masalimo 112:10

10 Munthu woyipa adzaona zimenezi ndipo adzapsa mtima;
    adzakukuta mano ake ndipo adzasungunuka.
    Zolakalaka za anthu oyipa sizidzachitika konse.

1 Akorinto 2:1-12

Pamene ndinabwera kwa inu, abale, sindinabwere ndi luntha lodziwa kuyankhula kapena nzeru zapamwamba pamene ndinachitira umboni chinsinsi cha Mulungu. Pakuti ndinatsimikiza pamene ndinali ndi inu kuti ndisadziwe kanthu kena kupatula Yesu Khristu wopachikidwayo. Ndinabwera kwa inu wofowoka ndi wamantha, ndiponso wonjenjemera kwambiri. Uthenga ndi ulaliki wanga sunali wa mawu anzeru ndi onyengerera koma woonetsa mphamvu za Mzimu, kuti chikhulupiriro chanu chisatsamire pa nzeru ya anthu koma pa mphamvu za Mulungu.

Nzeru Yochokera kwa Mzimu

Komabe ife timayankhula uthenga wa nzeru kwa okhwima, koma osati ndi nzeru ya mʼbado uno kapena ya olamula a mʼbado uno, amene mphamvu yawo ikutha. Ayi, ife timayankhula za nzeru yobisika ya Mulungu, nzeru imene inabisidwa ndipo imene Mulungu anatikonzera mu ulemerero wathu isanayambe nthawi. Palibe olamulira aliyense wa mʼbado uno amene anamumvetsetsa popeza anakamumvetsetsa sakanamupachika Ambuye wa ulemerero. Komabe monga zalembedwa kuti,

“Palibe diso linaona,
    palibe khutu linamva,
palibe amene anaganizira,
    zimene Mulungu anakonzera amene amukonda”

10 koma Mulungu waululira ife mwa Mzimu wake.

Mzimu amafufuza zinthu zonse, ndi zozama za Mulungu zomwe. 11 Kodi ndani mwa anthu angadziwe maganizo a munthu wina, kupatula mzimu wa munthuyo wokhala mʼkati mwake? Chimodzimodzinso palibe amene adziwa maganizo a Mulungu kupatula Mzimu wa Mulunguyo. 12 Mzimu amene tinalandira ife si wa dziko lapansi koma Mzimu wochokera kwa Mulungu wotipatsa ife mwaulere.

1 Akorinto 2:13-16

13 Izi ndi zimene timayankhula osati mʼmawu wophunzitsidwa ndi nzeru za munthu koma mʼmawu wophunzitsidwa ndi Mzimu, kufotokozera zoonadi zauzimu mʼmawu auzimu. 14 Munthu wopanda Mzimu savomereza zinthu zimene zichokera kwa Mzimu wa Mulungu, popeza ndi zopusa kwa iyeyo, ndipo sangazimvetsetse chifukwa zimazindikirika mwa Mzimu. 15 Munthu wauzimu amaweruza pa zinthu zonse, koma iye mwini saweruzidwa ndi munthu aliyense. 16 Pakuti

“Ndani anadziwa malingaliro a Ambuye,
    kuti akhoza kumulangiza Iye.”

Koma tili nawo mtima wa Khristu.

Mateyu 5:13-20

Mchere ndi Kuwunika

13 “Inu ndinu mchere wa dziko lapansi. Koma ngati mcherewo usukuluka, adzawukometsanso ndi chiyani? Ulibenso ntchito koma kungowutaya kunja, anthu nawuponda.

14 “Inu ndinu kuwunika kwa dziko lapansi. Mzinda wa pa phiri sungathe kubisika. 15 Anthu sayatsa nyale ndikuyivundikira ndi mbiya, mʼmalo mwake amayika poonekera ndipo imawunikira onse mʼnyumbamo. 16 Momwemonso kuwunika kwanu kuwale pamaso pa anthu kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kulemekeza Atate anu akumwamba.

Kukwaniritsa Malamulo

17 “Musaganize kuti ndinadza kudzathetsa malamulo kapena zonena za aneneri; sindinabwere kudzathetsa koma kukwaniritsa. 18 Ine ndikukuwuzani zoonadi kuti, kufikira kutha kwa thambo ndi dziko lapansi, chilichonse chimene chinalembedwa mʼmalamulo, ngakhale kalemba kakangʼonongʼono, chidzakwaniritsidwa. 19 Chifukwa chake aliyense amene aphwanya limodzi la malamulowa ngakhale lalingʼonongʼono ndi kuphunzitsa ena kuti achite chimodzimodzi, adzakhala wotsirizira mu ufumu wakumwamba, koma aliyense amene achita ndi kuphunzitsa malamulo awa adzakhala wamkulu mu ufumu wakumwamba. 20 Chifukwa chake ndikuwuzani kuti ngati chilungamo chanu sichiposa cha Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo, zoonadi, simudzalowa mu ufumu wakumwamba.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.