Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
112 Tamandani Yehova.
Wodala munthu amene amaopa Yehova,
amene amakondwera kwambiri ndi malamulo ake.
2 Ana ake adzakhala amphamvu mʼdziko;
mʼbado wa olungama mtima udzadalitsidwa.
3 Kulemera ndi chuma zili mʼnyumba yake,
ndipo chilungamo chake ndi chosatha.
4 Ngakhale mu mdima kuwala kumatulukira olungama mtima;
wokoma mtima, wachifundo ndi wowongoka mtima.
5 Zinthu zabwino zidzabwera kwa iye amene amapereka mowolowamanja ndi wokongoletsa mwaufulu,
amene amachita ntchito yake mwachilungamo.
6 Ndithu sadzagwedezeka;
munthu wolungama sadzayiwalika mpaka muyaya.
7 Saopa akamva zoyipa zimene zachitika;
mtima wake ndi wokhazikika ndipo amadalira Yehova.
8 Mtima wake ndi wotetezedwa, sadzakhala ndi mantha;
potsiriza pake adzayangʼana adani ake mwachipambano.
9 Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka,
chilungamo chake chimanka mpaka muyaya;
nyanga yake idzakwezedwa mwaulemu.
10 Munthu woyipa adzaona zimenezi ndipo adzapsa mtima;
adzakukuta mano ake ndipo adzasungunuka.
Zolakalaka za anthu oyipa sizidzachitika konse.
13 Ambuye akuti,
“Anthu awa amandipembedza Ine ndi pakamwa pawo,
ndi kundilemekeza Ine ndi milomo yawo,
koma mitima yawo ili kutali ndi Ine.
Kundipembedza kwawo ndi kwa chiphamaso.
Amandipembedza motsata malamulo a anthu amene anaphunzitsidwa.
14 Nʼchifukwa chakenso Ine ndidzapitirira
kuwachitira ntchito zodabwitsa;
nzeru za anthu anzeru zidzatha,
luntha la anthu aluntha Ine ndidzalinyoza.”
15 Tsoka kwa amene amayesetsa
kubisira Yehova maganizo awo,
amene amachita ntchito zawo mu mdima nʼkumanena kuti,
“Ndani amene akundiona kapena ndani akudziwa zimene ndikuchita?”
16 Inu mumazondotsa zinthu
ngati kuti dothi lasanduka wowumba mbiya.
Kodi chinthu chopangidwa chingawuze wochipanga kuti
“Sunandipange ndi iwe?”
Kapena mʼphika kunena kwa amene anawuwumba kuti,
“Iwe sudziwa chilichonse?”
Miyambo ya Makolo ya Ayuda
7 Afarisi ndi ena mwa aphunzitsi amalamulo omwe anachokera ku Yerusalemu anasonkhana momuzungulira Yesu ndipo 2 iwo anaona ophunzira ake akudya chakudya ndi mʼmanja mwakuda kapena kuti mʼmanja mosasamba. 3 (Afarisi ndi Ayuda onse sadya pokhapokha atasamba mʼmanja, kusunga mwambo wa makolo awo. 4 Akabwera kuchokera ku msika samadya pokhapokha atasamba. Ndipo amasunga miyambo ina yambiri monga, kutsuka zikho, mitsuko ndi maketulo).
5 Choncho Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo anafunsa Yesu kuti, “Nʼchifukwa chiyani ophunzira anu satsatira mwambo wa makolo, mʼmalo mwake amangodya chakudya ndi mʼmanja mwakuda?”
6 Iye anayankha kuti, “Yesaya ananena zoona pamene ananenera za inu achiphamaso; monga kunalembedwa kuti:
“Anthu awa amandilemekeza Ine ndi milomo yawo,
koma mitima yawo ili kutali ndi Ine.
7 Amandilambira Ine kwachabe;
ndi kuphunzitsa malamulo ndi malangizo a anthu.
8 Mwasiya malamulo a Mulungu ndipo mwagwiritsitsa miyambo ya anthu.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.