Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Nyimbo. Salimo la Asafu.
83 Inu Mulungu musakhale chete;
musangoti phee, Mulungu musangoti duu.
2 Onani adani anu akuchita chiwawa,
amene amadana nanu autsa mitu yawo.
3 Mochenjera iwo akukambirana za chiwembu kutsutsana ndi anthu anu;
Iwo akukonzekera kutsutsana ndi omwe mumawakonda.
4 Iwo akunena kuti, “Bwerani” akutero, “Tiyeni tiwononge mtundu wonsewu
kuti dzina la Israeli lisakumbukikenso.”
5 Ndi mtima umodzi akukonzekera chiwembu;
Iwo achita mgwirizano kutsutsana nanu:
6 Matenti a Edomu ndi Aismaeli,
Mowabu ndi Ahagiri,
7 Agebala, Aamoni ndi Aamaleki,
Afilisti, pamodzi ndi anthu a ku Turo.
8 Ngakhalenso Aasiriya aphatikizana nawo
kupereka mphamvu kwa ana a Loti.
Sela
9 Muwachitire zomwe munachitira Amidiyani,
monga munachitira Sisera ndi Yabini ku mtsinje wa Kisoni.
10 Amene anawonongedwa ku Endori
ndi kukhala ngati zinyalala.
11 Anthu awo otchuka muwachite zomwe munachita Orebu ndi Zeebu
ana a mafumu muwachite zomwe munachita Zeba ndi Zalimuna,
12 amene anati, “Tiyeni tilande dziko
la msipu la Mulungu.”
13 Muwasandutse fumbi lowuluka, Inu Mulungu wanga,
ngati mankhusu owuluka ndi mphepo.
14 Monga moto umatentha nkhalango,
kapena malawi a moto kuyatsa phiri,
15 kotero muwathamangitse ndi mphepo yamkuntho,
ndi kuwachititsa mantha ndi namondwe.
16 Muphimbe nkhope zawo ndi manyazi
kuti adzafunefune dzina lanu Yehova.
17 Achite manyazi ndi mantha nthawi zonse;
awonongeke mwa manyazi.
18 Adziwe kuti Inu amene dzina lanu ndi Yehova,
ndinu nokha Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi.
17 Pamenepo Yakobo anakonzeka nakweza ana ake ndi akazi ake pa ngamira, 18 anakusa ziweto zake zonse patsogolo natenga katundu wake yense amene anamupeza ku Padanaramu, ndipo ananyamuka kupita ku Kanaani, ku dziko la abambo ake, Isake.
19 Labani atachoka pa khomo kupita kukameta nkhosa, mʼmbuyomu Rakele anaba timafano ta milungu ta abambo ake. 20 Komanso nthawi iyi nʼkuti Yakobo atamunamiza Labani Mwaramu posamuwuza zoona kuti afuna kuthawa. 21 Choncho anathawa ndi zonse anali nazo. Ananyamuka nawoloka mtsinje wa Yufurate kupita cha ku Giliyadi, dziko la mapiri.
Labani Alondola Yakobo
22 Patapita masiku atatu, Labani anawuzidwa kuti Yakobo wathawa. 23 Pomwepo anatengana ndi abale ake namulondola Yakobo kwa masiku asanu ndi awiri ndipo anakamupezera ku Giliyadi, dziko la mapiri. 24 Koma Mulungu anabwera kwa Labani, Mwaramu kutulo usiku nati kwa iye, “Samala kuti usamuopseze Yakobo mwa njira iliyonse.”
25 Pamene Labani amamupeza Yakobo, nʼkuti Yakobo atamanga matenti ake ku mapiri a dziko la Giliyadi. Nayenso Labani ndi abale ake anamanga matenti awo komweko. 26 Tsono Labani anati kwa Yakobo, “Kodi ndakuchita chiyani kuti iwe undinamize ndi kutenga ana anga ngati anthu ogwidwa ku nkhondo? 27 Chifukwa chiyani unandinamiza ndi kuthawa mozemba wosandiwuza? Ukanandiwuza, bwezi titatsanzikana mwa chisangalalo ndi kuyimba nyimbo ndi zisekese ndi azeze. 28 Sunandilole kuti ndingopsompsona adzukulu anga ndi ana anga aakazi motsanzikana nawo. Unachita zopusa. 29 Ndili nayo mphamvu yakukuchita choyipa; koma usiku wapitawu, Mulungu wa abambo ako wandiwuza ine kuti, ‘Usamuopseze Yakobo mwa njira iliyonse.’ 30 Ndikudziwa kuti unachoka chifukwa unapukwa kufuna kubwerera kwanu kwa abambo ako. Koma nʼchifukwa chiyani unaba milungu yanga?”
31 Yakobo anayankha Labani kuti, “Ine ndinkaopa chifukwa ndinkaganiza kuti mukhoza kundilanda anawa. 32 Koma mukapeza wina aliyense ndi milungu yanu, ameneyo sakhala ndi moyo. Anthu onse akupenya, lozani chilichonse chanu chimene chili ndi ine, ndipo ngati muchipeze tengani. Koma Yakobo sankadziwa kuti Rakele anabadi milunguyo.”
33 Choncho Labani analowadi mu tenti ya Yakobo, ya Leya ndi mʼmatenti a adzakazi awiri aja, koma sanapeze kalikonse. Atatuluka mu tenti ya Leya, analowa ya Rakele. 34 Koma Rakele anatengadi milungu ija ndi kuyiika mʼkati mwa chokhalira cha pa ngamira, iye nʼkukhalapo. Choncho Labani anafunafuna mu tenti monse koma wosapeza kanthu.
35 Rakele anati kwa abambo ake, “Pepanitu musandikwiyire mbuye wanga chifukwa choti sinditha kuyimirira pamaso panu chifukwa ndili kumwezi.” Choncho Labani anafunafuna koma sanayipeze milungu ija.
Chikhulupiriro Kapena Ntchito za Lamulo
3 Agalatiya opusa inu, anakulodzani ndani? Tinamuonetsa poyera pamaso panu Yesu Khristu monga wopachikidwa pa mtanda. 2 Ine ndikufuna ndiphunzire kuchokera kwa inu chinthu chimodzi ichi: Kodi munalandira Mzimu pochita ntchito za lamulo, kapena pokhulupirira zimene munamva? 3 Kani ndinu opusa chotere? Inu mutayamba ndi Mzimu, kodi mukufuna kutsiriza ndi ntchito zathupi? 4 Kodi munavutika kwambiri pachabe, ngati kunali kwachabedi? 5 Kodi Mulungu amene anakupatsani Mzimu wake ndi kuchita zodabwitsa pakati panu, amachita zimenezi chifukwa mumachita ntchito za lamulo kapena chifukwa mumakhulupirira zimene munamva? 6 Nʼchimodzimodzinso Abrahamu, “Iye anakhulupirira Mulungu, ndipo Mulungu anamutenga kukhala wolungama.”
7 Tsono zindikirani kuti amene akhulupirira, ndi ana a Abrahamu. 8 Malemba anaonetseratu kuti Mulungu adzalungamitsa anthu a mitundu ina mwachikhulupiriro, ndipo ananeneratu Uthenga Wabwino kwa Abrahamu kuti, “Mitundu yonse ya anthu idzadalitsika kudzera mwa iwe.” 9 Choncho iwo amene ali ndi chikhulupiriro ndi odalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu, munthu wachikhulupiriro.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.