Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 146

146 Tamandani Yehova.

Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.
    Ndidzatamanda Yehova ndi moyo wanga wonse;
    ndidzayimba nyimbo zamatamando kwa Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga.

Musamadalire mafumu,
    anthu osakhalitsa, amene sangathe kupulumutsa.
Pamene mizimu yawo yachoka, iwo amabwerera ku dothi;
    zimene ankafuna kuchita zimatha tsiku lomwelo.

Wodala ndi amene thandizo lake ndi
    Mulungu wa Yakobo.
Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi,
    nyanja ndi zonse zili mʼmenemo;
    Yehova, amene ndi wokhulupirika kwamuyaya.
Iye amachitira chilungamo anthu oponderezedwa
    ndipo amapereka chakudya kwa anthu anjala.
Yehova amamasula amʼndende,
    Yehova amatsekula maso anthu osaona,
Yehova amadzutsa onse amene awerama pansi,
    Yehova amakonda anthu olungama.
Yehova amasamalira alendo
    ndipo amathandiza ana ndi akazi amasiye,
    koma amasokoneza njira za anthu oyipa.

10 Yehova ndiye Mfumu mpaka muyaya,
    Mulungu wako iwe Ziyoni, pa mibado yonse.

Tamandani Yehova.

Eksodo 29:1-9

Mwambo Wopatula Ansembe

29 “Pofuna kumupatula Aaroni ndi ana ake kuti akhale ansembe onditumikira Ine, uchite izi: Utenge ngʼombe yayingʼono yayimuna ndi nkhosa ziwiri zazimuna zopanda chilema. Utengenso buledi wopanda yisiti, makeke wopanda yisiti wopakidwa mafuta. Zonsezi uzipange ndi ufa wosalala wa tirigu. Uziyike mʼdengu ndipo ubwere nazo kwa Ine pamodzi ndi ngʼombe yayimuna ija ndi nkhosa ziwiri zazimuna zija. Kenaka ubwere naye Aaroni ndi ana ake pa khomo la tenti ya msonkhano ndipo uwasambitse ndi madzi. Tenga zovala ndipo umuveke Aaroni mwinjiro, mkanjo wa efodi, efodiyo ndi chovala chapachifuwa. Umumange mʼchiwuno lamba wa efodi wolukidwa mwaluso uja. Umuveke nduwira kumutu, ndiponso uyike chizindikiro chopatulika chija pa nduwirayo. Utenge mafuta wodzozera ndipo uwatsanulire pamutu pake kumudzoza. Ubwere ndi ana ake aamuna ndipo uwavekenso minjiro ndi nduwira. Kenaka umange malamba Aaroniyo pamodzi ndi ana ake ndi kuwaveka nduwira. Motero unsembe udzakhala wawo malingana ndi lamulo ili losatha.

“Umu ndi mmene udzadzozere Aaroni ndi ana ake aamuna.

Machitidwe a Atumwi 22:6-21

“Nthawi ya masana, nditayandikira ku Damasiko, mwadzidzidzi kuwala kwakukulu kochokera kumwamba kunandizungulira. Ndinagwa pansi ndipo ndinamva mawu akuti, ‘Saulo! Saulo! Ukundizunziranji?’ ”

Ine ndinafunsa kuti, “Ndinu ndani Ambuye?”

Iye anayankha kuti, “Ndine Yesu wa ku Nazareti, amene iwe ukumuzunza.” Anzanga a paulendo anaona kuwalako, koma sanamve mawuwo, a Iye amene amayankhula nane.

10 Ine ndinafunsa kuti, “Kodi ndichite chiyani Ambuye?”

Ambuye anati, “Imirira ndipo pita ku Damasiko. Kumeneko adzakuwuza zonse zimene ukuyenera kuchita.” 11 Anzanga anandigwira dzanja kupita nane ku Damasiko, popeza kuwala kunja kunandichititsa khungu.

12 “Munthu wina dzina lake Hananiya anabwera kudzandiona. Iyeyu anali munthu woopa Mulungu ndi wosunga Malamulo. Ayuda onse okhala kumeneko amamupatsa ulemu waukulu. 13 Iye anayimirira pafupi nane nati, ‘Mʼbale Saulo, penyanso!’ Ndipo nthawi yomweyo ndinapenya ndikumuona iyeyo.

14 “Ndipo iye anati, ‘Mulungu wa makolo athu wakusankha iwe kuti udziwe chifuniro chake ndi kuona Wolungamayo ndi kumva mawu ochokera pakamwa pake. 15 Iwe udzakhala mboni yake kwa anthu onse pa zimene waziona ndi kuzimva. 16 Ndipo tsopano ukudikira chiyani? Dzuka ndi kutama dzina la Ambuye mopemba, ubatizidwe ndi kuchotsa machimo ako.’

17 “Nditabwerera ku Yerusalemu, ndikupemphera mʼNyumba ya Mulungu, ndinachita ngati ndakomoka. 18 Ndinaona Ambuye akundiwuza kuti, ‘Fulumira! Tuluka mu Yerusalemu msangamsanga, chifukwa anthuwa sadzavomereza umboni wako wonena za Ine.’ ”

19 Ine ndinayankha Ambuye kuti, “Anthu awa akudziwa kuti ine ndinkapita ku sunagoge iliyonse ndipo ndinkawaponya mʼndende ndi kuwakwapula amene ankakhulupirira inu. 20 Ndipo pamene ankapha Stefano, ine ndinali pomwepo kuvomereza ndi kusunga zovala za amene amamupha.”

21 Pamenepo Ambuye anandiwuza kuti, “Nyamuka; Ine ndidzakutuma kutali kwa anthu a mitundu ina.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.