Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mafumu 5:1-14

Naamani Achiritsidwa Khate Lake

Tsono Naamani anali mtsogoleri wa gulu lankhondo a mfumu ya ku Aramu. Iye anali munthu wodalirika pamaso pa mbuye wake ndipo anali wokondedwa kwambiri, chifukwa kudzera mwa iye Yehova anapambanitsa Aaramu. Anali msilikali wolimba mtima, koma anali ndi khate.

Tsono magulu a Aaramu anapita ku nkhondo ndipo anakagwira ukapolo mtsikana wamngʼono wa ku Israeli, ndipo ankatumikira mkazi wa Naamani. Mtsikanayo anawuza mkazi wa Naamani kuti, “Mbuye wanga akanapita kukaonana ndi mneneri amene amakhala ku Samariya, akanachiritsidwa khate lawo.”

Naamani anapita kwa mbuye wake kukamuwuza zomwe mtsikana wochokera ku Israeli ananena. Mfumu ya ku Aramu inayankha kuti, “Iwe uyenera kupita. Ine ndilembera kalata mfumu ya ku Israeli.” Choncho Naamani ananyamuka kupita ku Samariya, atatenga ndalama za siliva 30,000, ndalama zagolide 6,000 ndiponso zovala khumi za pa chikondwerero. Kalata imene anapita nayo kwa mfumu ya ku Israeli inali ndi mawu awa: “Taonani, ndikutumiza Naamani mtumiki wanga pamodzi ndi kalatayi kwa inu kuti mumuchiritse khate lake.”

Mfumu ya ku Israeli itangowerenga kalatayo, inangʼamba mkanjo wake ndipo inati, “Kodi ine ndine Mulungu? Kodi ndingathe kupha kapena kupereka moyo? Chifukwa chiyani munthu ameneyu wanditumizira munthu woti ndimuchiritse khate lake? Taonani, iyeyu akungofuna kuti apeze chifukwa choyambanirana nane!”

Elisa munthu wa Mulungu atamva kuti mfumu ya ku Israeli yangʼamba mkanjo wake, anatumiza uthenga uwu: “Chifukwa chiyani mwangʼamba mkanjo wanu? Mutumizeni munthuyo kwa ine ndipo iyeyo adzadziwa kuti muli mneneri mu Israeli.” Choncho Naamani anapita pamodzi ndi akavalo ake ndi magaleta nakayima pa khomo la nyumba ya Elisa. 10 Elisa anatumiza uthenga kwa iye woti, “Pita, kasambe kasanu ndi kawiri mu mtsinje wa Yorodani, thupi lako lidzachira ndi kukhalanso monga kale ndipo udzayeretsedwa.”

11 Koma Naamani anachoka mokwiya ndipo anati, “Ine ndimaganiza kuti munthuyu atuluka ndipo ayimirira nayitana dzina la Yehova Mulungu wake, nayendetsa dzanja lake pamwamba pa nthendayi ndi kundichiritsa khate langa. 12 Kodi Abana ndi Faripara, mitsinje ya ku Damasiko, siyoposa mitsinje ina yonse ya ku Israeli? Kodi sindikanasamba mʼmitsinje imeneyo ndi kuyeretsedwa?” Kotero anatembenuka nachoka ali wokwiya kwambiri.

13 Antchito ake anamuyandikira namufunsa kuti, “Abambo anga, mneneri akanakulamulani chinthu chachikulu, kodi inu simukanachita? Nanga nʼzovuta motani zomwe mneneri wanena kuti ‘Kasambeni ndipo mudzayeretsedwa!’ ” 14 Choncho Naamani anapita ku Yorodani nakadzimiza mʼmadzimo kasanu nʼkawiri, monga momwe munthu wa Mulungu anamuwuzira. Thupi lake linakhalanso monga kale ndipo linakhala losalala ngati la kamnyamata.

Masalimo 30

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba popereka Nyumba ya Mulungu.

30 Ndidzakukwezani Yehova,
    chifukwa mwanditulutsa kwakuya,
    ndipo simunalole kuti adani anga akondwere pa ine.
Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizo
    ndipo Inu munandichiritsa.
Inu Yehova, munanditulutsa ku manda,
    munandisunga kuti ndisatsalire mʼdzenje.

Imbirani Yehova inu anthu ake okhulupirika;
    tamandani dzina lake loyera.
Pakuti mkwiyo wake umakhala kwa kanthawi
    koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse;
utha kuchezera kulira usiku wonse,
    koma chimwemwe chimabwera mmawa.

Pamene ndinaona kuti ndili otetezedwa ndinati,
    “Sindidzagwedezekanso.”
Inu Yehova, pamene munandikomera mtima,
    munachititsa phiri langa kuyima chilili;
koma pamene munabisa nkhope yanu,
    ndinataya mtima.

Kwa Inu Yehova ndinayitana;
    kwa Ambuye ndinapempha chifundo;
“Kodi pali phindu lanji powonongeka kwanga
    ngati nditsikira ku dzenje?
Kodi fumbi lidzakutamandani Inu?
    Kodi lidzalengeza za kukhulupirika kwanu?
10 Imvani Yehova ndipo mundichitire chifundo;
    Yehova mukhale thandizo langa.”

11 Inu munasandutsa kulira kwanga kukhala kuvina;
    munachotsa chiguduli changa ndi kundiveka ndi chimwemwe,
12 kuti mtima wanga uthe kuyimbira Inu usakhale chete.
    Yehova Mulungu wanga, ndidzapereka kwa Inu mayamiko kwamuyaya.

1 Akorinto 9:24-27

Kufunika kwa Kudziretsa

24 Kodi simukudziwa kuti pa mpikisano wa liwiro onse amathamanga ndithu, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphotho? Motero thamangani kuti mupate mphotho. 25 Aliyense wochita mpikisano amakonzekera mwamphamvu. Amachita izi kuti alandire mphotho yankhata yamaluwa yomwe imafota. Koma ife timachita izi kuti tilandire mphotho yosafota. 26 Choncho sindithamanga monga wothamanga wopanda cholinga; komanso sindichita mpikisano wankhonya monga munthu amene amangomenya mophonya. 27 Ine ndimazunza thupi langa ndi kulisandutsa kapolo kuti nditatha kulalikira ena, ineyo ndingadzapezeke wosayenera kulandira nawo mphotho.

Marko 1:40-45

Yesu Achiritsa Wakhate

40 Munthu wakhate anabwera kwa Iye, nagwada, namupempha kuti, “Ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”

41 Yesu pomva naye chifundo, anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo nati, “Ndikufuna, yeretsedwa!” 42 Nthawi yomweyo khate linachoka ndipo anachiritsidwa.

43 Nthawi yomweyo Yesu anamuwuza kuti apite koma anamuchenjeza kuti, 44 “Wonetsetsa kuti usawuze aliyense za zimenezi. Koma pita, kadzionetse wekha kwa wansembe ndi kukapereka nsembe zimene Mose analamulira zotsimikizira kuyeretsedwa kwanu, ngati umboni kwa iwo.” 45 Mʼmalo mwake anapita nayamba kuyankhula momasuka, nafalitsa mbiriyo. Zotsatira zake, Yesu sanathe kulowa mʼmudzi moonekera, koma anakhala kunja kumalo kopanda anthu. Komabe anthu amabwera kwa Iye kuchokera kulikonse.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.